< Yobu 3 >
1 Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa.
μετὰ τοῦτο ἤνοιξεν Ιωβ τὸ στόμα αὐτοῦ
καὶ κατηράσατο τὴν ἡμέραν αὐτοῦ λέγων
3 “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
ἀπόλοιτο ἡ ἡμέρα ἐν ᾗ ἐγεννήθην καὶ ἡ νύξ ἐν ᾗ εἶπαν ἰδοὺ ἄρσεν
4 Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
ἡ ἡμέρα ἐκείνη εἴη σκότος καὶ μὴ ἀναζητήσαι αὐτὴν ὁ κύριος ἄνωθεν μηδὲ ἔλθοι εἰς αὐτὴν φέγγος
5 Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli; mtambo uphimbe tsikuli; mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
ἐκλάβοι δὲ αὐτὴν σκότος καὶ σκιὰ θανάτου ἐπέλθοι ἐπ’ αὐτὴν γνόφος
6 Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani; usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka, kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
καταραθείη ἡ ἡμέρα καὶ ἡ νὺξ ἐκείνη ἀπενέγκαιτο αὐτὴν σκότος μὴ εἴη εἰς ἡμέρας ἐνιαυτοῦ μηδὲ ἀριθμηθείη εἰς ἡμέρας μηνῶν
7 Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino; kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
ἀλλὰ ἡ νὺξ ἐκείνη εἴη ὀδύνη καὶ μὴ ἔλθοι ἐπ’ αὐτὴν εὐφροσύνη μηδὲ χαρμονή
8 Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo, iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
ἀλλὰ καταράσαιτο αὐτὴν ὁ καταρώμενος τὴν ἡμέραν ἐκείνην ὁ μέλλων τὸ μέγα κῆτος χειρώσασθαι
9 Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima; tsikulo liyembekezere kucha pachabe ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
σκοτωθείη τὰ ἄστρα τῆς νυκτὸς ἐκείνης ὑπομείναι καὶ εἰς φωτισμὸν μὴ ἔλθοι καὶ μὴ ἴδοι ἑωσφόρον ἀνατέλλοντα
10 Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.
ὅτι οὐ συνέκλεισεν πύλας γαστρὸς μητρός μου ἀπήλλαξεν γὰρ ἂν πόνον ἀπὸ ὀφθαλμῶν μου
11 “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
διὰ τί γὰρ ἐν κοιλίᾳ οὐκ ἐτελεύτησα ἐκ γαστρὸς δὲ ἐξῆλθον καὶ οὐκ εὐθὺς ἀπωλόμην
12 Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo ndi mawere woti andiyamwitsepo?
ἵνα τί δὲ συνήντησάν μοι γόνατα ἵνα τί δὲ μαστοὺς ἐθήλασα
13 Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere; ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
νῦν ἂν κοιμηθεὶς ἡσύχασα ὑπνώσας δὲ ἀνεπαυσάμην
14 pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi, amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
μετὰ βασιλέων βουλευτῶν γῆς οἳ ἠγαυριῶντο ἐπὶ ξίφεσιν
15 pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide, amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
ἢ μετὰ ἀρχόντων ὧν πολὺς ὁ χρυσός οἳ ἔπλησαν τοὺς οἴκους αὐτῶν ἀργυρίου
16 Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale, ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
ἢ ὥσπερ ἔκτρωμα ἐκπορευόμενον ἐκ μήτρας μητρὸς ἢ ὥσπερ νήπιοι οἳ οὐκ εἶδον φῶς
17 Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto, ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
ἐκεῖ ἀσεβεῖς ἐξέκαυσαν θυμὸν ὀργῆς ἐκεῖ ἀνεπαύσαντο κατάκοποι τῷ σώματι
18 A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere; sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
ὁμοθυμαδὸν δὲ οἱ αἰώνιοι οὐκ ἤκουσαν φωνὴν φορολόγου
19 Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko, ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.
μικρὸς καὶ μέγας ἐκεῖ ἐστιν καὶ θεράπων οὐ δεδοικὼς τὸν κύριον αὐτοῦ
20 “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto, ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
ἵνα τί γὰρ δέδοται τοῖς ἐν πικρίᾳ φῶς ζωὴ δὲ ταῖς ἐν ὀδύναις ψυχαῖς
21 kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera, amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
οἳ ὁμείρονται τοῦ θανάτου καὶ οὐ τυγχάνουσιν ἀνορύσσοντες ὥσπερ θησαυρούς
22 amene amakondwa ndi kusangalala akamalowa mʼmanda?
περιχαρεῖς δὲ ἐγένοντο ἐὰν κατατύχωσιν
23 Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu amene njira yake yabisika, amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
θάνατος ἀνδρὶ ἀνάπαυμα συνέκλεισεν γὰρ ὁ θεὸς κατ’ αὐτοῦ
24 Mʼmalo moti ndidye, ndimalira, ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
πρὸ γὰρ τῶν σίτων μου στεναγμός μοι ἥκει δακρύω δὲ ἐγὼ συνεχόμενος φόβῳ
25 Chimene ndinkachiopa chandigwera; chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
φόβος γάρ ὃν ἐφρόντισα ἦλθέν μοι καὶ ὃν ἐδεδοίκειν συνήντησέν μοι
26 Ndilibe mtendere kapena bata, ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”
οὔτε εἰρήνευσα οὔτε ἡσύχασα οὔτε ἀνεπαυσάμην ἦλθεν δέ μοι ὀργή