< Yobu 29 >
1 Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
Moreover Job continued his discourse, and said:
2 “Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi, masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,
O that I were as in months past, In the days when God was my guardian;
3 pamene nyale yake inkandiwunikira ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima!
When his lamp shined over my head, And when by his light I walked through darkness!
4 Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri, pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga,
As I was in the autumn of my days, When the friendship of God was over my tent;
5 nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane, ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu,
When the Almighty was yet with me, And my children were around me;
6 pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka, ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi.
When I bathed my steps in milk, And the rock poured me out rivers of oil!
7 “Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo,
When I went forth to the gate by the city, And took my seat in the market-place,
8 anyamata amati akandiona ankapatuka ndipo anthu akuluakulu ankayimirira;
The young men saw me and hid themselves, And the aged arose and stood.
9 atsogoleri ankakhala chete ndipo ankagwira pakamwa pawo;
The princes refrained from speaking, And laid their hand upon their mouth.
10 anthu otchuka ankangoti duu, ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo.
The nobles held their peace, And their tongue cleaved to the roof of their mouth.
11 Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga, ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira,
When the ear heard me, then it blessed me; And when the eye saw me, it gave witness to me.
12 chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.
For I delivered the poor, when they cried; And the fatherless, who had none to help him.
13 Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa; ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.
The blessing of him that was ready to perish came upon me, And I caused the heart of the widow to sing for joy.
14 Chilungamo chinali ngati chovala changa; chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga.
I clothed myself with righteousness, and it clothed itself with me; And justice was my robe and diadem.
15 Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya; ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala.
I was eyes to the blind, And feet was I to the lame;
16 Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake.
I was a father to the poor, And the cause of him I knew not I searched out;
17 Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa ndi kulanditsa amene anali atagwidwa.
And I broke the teeth of the wicked, And plucked the spoil from his jaws.
18 “Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga, masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga.
Then said I, “I shall die in my nest; I shall multiply my days as the sand.
19 Mizu yanga idzatambalalira ku madzi, ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse.
My root is spread abroad to the waters, And the dew abideth on my branches.
20 Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’
My glory is fresh with me, And my bow gathereth strength in my hand.”
21 “Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.
To me men gave ear, and waited, And kept silence for my counsel.
22 Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso; mawu anga ankawagwira mtima.
To my words they made no reply, When my speech dropped down upon them.
23 Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe.
Yea, they waited for me as for the rain; They opened their mouths wide as for the latter rain.
24 Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira; kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo.
If I smiled upon them, they believed it not; Nor did they cause the light of my countenance to fall.
25 Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu; ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo; ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.”
When I came among them, I sat as chief; I dwelt as a king in the midst of an army, As a comforter among mourners.