< Yobu 27 >

1 Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
וַיֹּסֶף אִיּוֹב שְׂאֵת מְשָׁלוֹ וַיֹּאמַֽר׃
2 “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama, Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
חַי־אֵל הֵסִיר מִשְׁפָּטִי וְשַׁדַּי הֵמַר נַפְשִֽׁי׃
3 nthawi zonse pamene ndili ndi moyo, mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
כִּי־כׇל־עוֹד נִשְׁמָתִי בִי וְרוּחַ אֱלוֹהַּ בְּאַפִּֽי׃
4 pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa, lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
אִם־תְּדַבֵּרְנָה שְׂפָתַי עַוְלָה וּלְשׁוֹנִי אִם־יֶהְגֶּה רְמִיָּֽה׃
5 Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona; mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
חָלִילָה לִּי אִם־אַצְדִּיק אֶתְכֶם עַד־אֶגְוָע לֹֽא־אָסִיר תֻּמָּתִי מִמֶּֽנִּי׃
6 Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere; chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.
בְּצִדְקָתִי הֶחֱזַקְתִּי וְלֹא אַרְפֶּהָ לֹא־יֶחֱרַף לְבָבִי מִיָּמָֽי׃
7 “Mdani wanga akhale ngati woyipa, wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
יְהִי כְרָשָׁע אֹיְבִי וּמִתְקוֹמְמִי כְעַוָּֽל׃
8 Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu achotsa moyo wake?
כִּי מַה־תִּקְוַת חָנֵף כִּי יִבְצָע כִּי יֵשֶׁל אֱלוֹהַּ נַפְשֽׁוֹ׃
9 Kodi Mulungu amamva kulira kwake pamene zovuta zamugwera?
הֲֽצַעֲקָתוֹ יִשְׁמַע ׀ אֵל כִּֽי־תָבוֹא עָלָיו צָרָֽה׃
10 Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse? Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
אִם־עַל־שַׁדַּי יִתְעַנָּג יִקְרָא אֱלוֹהַּ בְּכׇל־עֵֽת׃
11 “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
אוֹרֶה אֶתְכֶם בְּיַד־אֵל אֲשֶׁר עִם־שַׁדַּי לֹא אֲכַחֵֽד׃
12 Inu mwadzionera nokha zonsezi. Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?
הֵן־אַתֶּם כֻּלְּכֶם חֲזִיתֶם וְלָמָּה־זֶּה הֶבֶל תֶּהְבָּֽלוּ׃
13 “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa, cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
זֶה ׀ חֵלֶק־אָדָם רָשָׁע ׀ עִם־אֵל וְֽנַחֲלַת עָרִיצִים מִשַּׁדַּי יִקָּֽחוּ׃
14 Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
אִם־יִרְבּוּ בָנָיו לְמוֹ־חָרֶב וְצֶאֱצָאָיו לֹא יִשְׂבְּעוּ־לָֽחֶם׃
15 Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri, ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
שְׂרִידָו בַּמָּוֶת יִקָּבֵרוּ וְאַלְמְנֹתָיו לֹא תִבְכֶּֽינָה׃
16 Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, ndi kukundika zovala ngati mchenga,
אִם־יִצְבֹּר כֶּעָפָר כָּסֶף וְכַחֹמֶר יָכִין מַלְבּֽוּשׁ׃
17 zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale, ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
יָכִין וְצַדִּיק יִלְבָּשׁ וְכֶסֶף נָקִי יַחֲלֹֽק׃
18 Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche, ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
בָּנָה כָעָשׁ בֵּיתוֹ וּכְסֻכָּה עָשָׂה נֹצֵֽר׃
19 Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko; akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
עָשִׁיר יִשְׁכַּב וְלֹא יֵאָסֵף עֵינָיו פָּקַח וְאֵינֶֽנּוּ׃
20 Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula; mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
תַּשִּׂיגֵהוּ כַמַּיִם בַּלָּהוֹת לַיְלָה גְּנָבַתּוּ סוּפָֽה׃
21 Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo imamuchotsa pamalo pake.
יִשָּׂאֵהוּ קָדִים וְיֵלַךְ וִישָׂעֲרֵהוּ מִמְּקֹמֽוֹ׃
22 Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni, pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
וְיַשְׁלֵךְ עָלָיו וְלֹא יַחְמֹל מִיָּדוֹ בָּרוֹחַ יִבְרָֽח׃
23 Mphepoyo imamuwomba ndithu ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”
יִשְׂפֹּק עָלֵימוֹ כַפֵּימוֹ וְיִשְׁרֹק עָלָיו מִמְּקֹמֽוֹ׃

< Yobu 27 >