< Yobu 26 >

1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
Entonces Job respondió:
2 “Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu! Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
¡Qué bien ayudas al débil y socorres al brazo que no tiene fuerza!
3 Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru! Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
¡Qué útil discernimiento proveíste abundantemente!
4 Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa? Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?
¿Para quién pronunciaste tus palabras? ¿El espíritu de quién se expresó por medio de ti?
5 “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi, ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
La sombra de los muertos se estremece bajo las aguas y sus habitantes.
6 Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu; chiwonongeko ndi chosaphimbidwa. (Sheol h7585)
El Seol está desnudo ante ʼElohim, y el Abadón no tiene cubierta. (Sheol h7585)
7 Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho; Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
Él extiende el norte sobre el abismo y cuelga la tierra de la nada.
8 Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake, koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
Encierra las aguas en sus nubes y las nubes no se rompen con ellas.
9 Iye amaphimba mwezi wowala, amawuphimba ndi mitambo yake.
Encubre la cara de la luna llena y sobre ella extiende su nube.
10 Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta, kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
Trazó un círculo sobre la superficie del agua en el límite entre la luz y la oscuridad.
11 Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
Las columnas del cielo se estremecen y están pasmadas ante su reprensión.
12 Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja; ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
Aquieta el mar con su poder, y con su entendimiento rompe la tormenta.
13 Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga, dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
Su soplo despejó el cielo, y su mano traspasó la serpiente cautelosa.
14 Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake; tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona! Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”
Ciertamente estos son solo los bordes de sus caminos. ¡Cuán leve murmullo oímos de Él! Pero el trueno de su poder, ¿quién lo puede entender?

< Yobu 26 >