< Yobu 23 >

1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
וַיַּ֥עַן אִיֹּ֗וב וַיֹּאמַֽר׃
2 “Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri; Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.
גַּם־הַ֭יֹּום מְרִ֣י שִׂחִ֑י יָ֝דִ֗י כָּבְדָ֥ה עַל־אַנְחָתִֽי׃
3 Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu; ndikanangopita kumene amakhalako!
מִֽי־יִתֵּ֣ן יָ֭דַעְתִּי וְאֶמְצָאֵ֑הוּ אָ֝בֹ֗וא עַד־תְּכוּנָתֹֽו׃
4 Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.
אֶעֶרְכָ֣ה לְפָנָ֣יו מִשְׁפָּ֑ט וּ֝פִ֗י אֲמַלֵּ֥א תֹוכָחֹֽות׃
5 Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha, ndi kulingalira bwino zimene akananena!
אֵ֭דְעָה מִלִּ֣ים יַעֲנֵ֑נִי וְ֝אָבִ֗ינָה מַה־יֹּ֥אמַר לִֽי׃
6 Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu? Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.
הַבְּרָב־כֹּ֖חַ יָרִ֣יב עִמָּדִ֑י לֹ֥א אַךְ־ה֝֗וּא יָשִׂ֥ם בִּֽי׃
7 Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake, ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.
שָׁ֗ם יָ֭שָׁר נֹוכָ֣ח עִמֹּ֑ו וַאֲפַלְּטָ֥ה לָ֝נֶ֗צַח מִשֹּׁפְטִֽי׃
8 “Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko, ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.
הֵ֤ן קֶ֣דֶם אֶהֱלֹ֣ךְ וְאֵינֶ֑נּוּ וְ֝אָחֹ֗ור וְֽלֹא־אָבִ֥ין לֹֽו׃
9 Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko akapita kummwera, sindimuona.
שְׂמֹ֣אול בַּעֲשֹׂתֹ֣ו וְלֹא־אָ֑חַז יַעְטֹ֥ף יָ֝מִ֗ין וְלֹ֣א אֶרְאֶֽה׃
10 Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.
כִּֽי־יָ֭דַע דֶּ֣רֶךְ עִמָּדִ֑י בְּ֝חָנַ֗נִי כַּזָּהָ֥ב אֵצֵֽא׃
11 Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake; ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.
בַּ֭אֲשֻׁרֹו אָחֲזָ֣ה רַגְלִ֑י דַּרְכֹּ֖ו שָׁמַ֣רְתִּי וְלֹא־אָֽט׃
12 Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.
מִצְוַ֣ת שְׂ֭פָתָיו וְלֹ֣א אָמִ֑ישׁ מֵ֝חֻקִּ֗י צָפַ֥נְתִּי אִמְרֵי־פִֽיו׃
13 “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye? Iye amachita chilichonse chimene wafuna.
וְה֣וּא בְ֭אֶחָד וּמִ֣י יְשִׁיבֶ֑נּוּ וְנַפְשֹׁ֖ו אִוְּתָ֣ה וַיָּֽעַשׂ׃
14 Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire, ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.
כִּ֭י יַשְׁלִ֣ים חֻקִּ֑י וְכָהֵ֖נָּה רַבֹּ֣ות עִמֹּֽו׃
15 Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake; ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.
עַל־כֵּ֭ן מִפָּנָ֣יו אֶבָּהֵ֑ל אֶ֝תְבֹּונֵ֗ן וְאֶפְחַ֥ד מִמֶּֽנּוּ׃
16 Mulungu walefula mtima wanga; Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.
וְ֭אֵל הֵרַ֣ךְ לִבִּ֑י וְ֝שַׁדַּ֗י הִבְהִילָֽנִי׃
17 Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima, ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.
כִּֽי־לֹ֣א נִ֭צְמַתִּי מִפְּנֵי־חֹ֑שֶׁךְ וּ֝מִפָּנַ֗י כִּסָּה־אֹֽפֶל׃

< Yobu 23 >