< Yobu 22 >

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
ויען אליפז התמני ויאמר
2 “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu? Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye?
הלאל יסכן-גבר-- כי-יסכן עלימו משכיל
3 Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama? Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro?
החפץ לשדי כי תצדק ואם-בצע כי-תתם דרכיך
4 “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu?
המיראתך יכיחך יבוא עמך במשפט
5 Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu? Kodi machimo ako si opanda malire?
הלא רעתך רבה ואין-קץ לעונתיך
6 Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa; umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche.
כי-תחבל אחיך חנם ובגדי ערומים תפשיט
7 Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala,
לא-מים עיף תשקה ומרעב תמנע-לחם
8 ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake, munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo.
ואיש זרוע לו הארץ ונשוא פנים ישב בה
9 Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu, ndipo unapondereza ana amasiye.
אלמנות שלחת ריקם וזרעות יתמים ידכא
10 Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira, nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha,
על-כן סביבותיך פחים ויבהלך פחד פתאם
11 nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu, nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza.
או-חשך לא-תראה ושפעת-מים תכסך
12 “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo!
הלא-אלוה גבה שמים וראה ראש כוכבים כי-רמו
13 Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani? Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu?
ואמרת מה-ידע אל הבעד ערפל ישפוט
14 Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’
עבים סתר-לו ולא יראה וחוג שמים יתהלך
15 Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale imene anthu oyipa ankayendamo?
הארח עולם תשמור-- אשר דרכו מתי-און
16 Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane, maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula.
אשר-קמטו ולא-עת נהר יוצק יסודם
17 Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’
האמרים לאל סור ממנו ומה-יפעל שדי למו
18 Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino, choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa.
והוא מלא בתיהם טוב ועצת רשעים רחקה מני
19 “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera; anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa.
יראו צדיקים וישמחו ונקי ילעג-למו
20 Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka ndipo moto wawononga chuma chawo!’
אם-לא נכחד קימנו ויתרם אכלה אש
21 “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere; ukatero udzaona zabwino.
הסכן-נא עמו ושלם בהם תבואתך טובה
22 Landira malangizo a pakamwa pake ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako.
קח-נא מפיו תורה ושים אמריו בלבבך
23 Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa; ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako,
אם-תשוב עד-שדי תבנה תרחיק עולה מאהלך
24 ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi, golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa.
ושית-על-עפר בצר ובצור נחלים אופיר
25 Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali.
והיה שדי בצריך וכסף תועפות לך
26 Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.
כי-אז על-שדי תתענג ותשא אל-אלוה פניך
27 Udzamupempha ndipo adzakumvera, ndipo udzapereka zimene unalonjeza.
תעתיר אליו וישמעך ונדריך תשלם
28 Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi, kuwala kudzakuwunikira pa njira yako.
ותגזר-אמר ויקם לך ועל-דרכיך נגה אור
29 Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’ Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa.
כי-השפילו ותאמר גוה ושח עינים יושע
30 Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa, ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.”
ימלט אי-נקי ונמלט בבר כפיך

< Yobu 22 >