< Yobu 21 >

1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
ויען איוב ויאמר׃
2 “Mvetserani bwino mawu anga; ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.
שמעו שמוע מלתי ותהי זאת תנחומתיכם׃
3 Ndiloleni ndiyankhule ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.
שאוני ואנכי אדבר ואחר דברי תלעיג׃
4 “Kodi ine ndikudandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima?
האנכי לאדם שיחי ואם מדוע לא תקצר רוחי׃
5 Ndipenyeni ndipo mudabwe; mugwire dzanja pakamwa.
פנו אלי והשמו ושימו יד על פה׃
6 Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri; thupi langa limanjenjemera.
ואם זכרתי ונבהלתי ואחז בשרי פלצות׃
7 Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo, amakalamba ndi kusanduka amphamvu?
מדוע רשעים יחיו עתקו גם גברו חיל׃
8 Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo, zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.
זרעם נכון לפניהם עמם וצאצאיהם לעיניהם׃
9 Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha; mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.
בתיהם שלום מפחד ולא שבט אלוה עליהם׃
10 Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa; ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.
שורו עבר ולא יגעל תפלט פרתו ולא תשכל׃
11 Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa; makanda awo amavinavina pabwalo.
ישלחו כצאן עויליהם וילדיהם ירקדון׃
12 Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze; amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.
ישאו כתף וכנור וישמחו לקול עוגב׃
13 Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere. (Sheol h7585)
יבלו בטוב ימיהם וברגע שאול יחתו׃ (Sheol h7585)
14 Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.
ויאמרו לאל סור ממנו ודעת דרכיך לא חפצנו׃
15 Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire? Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?
מה שדי כי נעבדנו ומה נועיל כי נפגע בו׃
16 Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.
הן לא בידם טובם עצת רשעים רחקה מני׃
17 “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa? Nʼkangati kamene tsoka limawagwera? Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?
כמה נר רשעים ידעך ויבא עלימו אידם חבלים יחלק באפו׃
18 Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo, ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?
יהיו כתבן לפני רוח וכמץ גנבתו סופה׃
19 Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’ Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.
אלוה יצפן לבניו אונו ישלם אליו וידע׃
20 Mulole kuti adzionere yekha chilango chake, kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.
יראו עינו כידו ומחמת שדי ישתה׃
21 Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo, pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?
כי מה חפצו בביתו אחריו ומספר חדשיו חצצו׃
22 “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
הלאל ילמד דעת והוא רמים ישפוט׃
23 Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse, ali pa mtendere ndi pa mpumulo,
זה ימות בעצם תמו כלו שלאנן ושליו׃
24 thupi lake lili lonenepa, mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.
עטיניו מלאו חלב ומח עצמותיו ישקה׃
25 Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima, wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.
וזה ימות בנפש מרה ולא אכל בטובה׃
26 Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda ndipo onse amatuluka mphutsi.
יחד על עפר ישכבו ורמה תכסה עליהם׃
27 “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza, ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.
הן ידעתי מחשבותיכם ומזמות עלי תחמסו׃
28 Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti, matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’
כי תאמרו איה בית נדיב ואיה אהל משכנות רשעים׃
29 Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo? Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?
הלא שאלתם עוברי דרך ואתתם לא תנכרו׃
30 Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?
כי ליום איד יחשך רע ליום עברות יובלו׃
31 Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo? Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?
מי יגיד על פניו דרכו והוא עשה מי ישלם לו׃
32 Iye amanyamulidwa kupita ku manda ndipo anthu amachezera pa manda ake.
והוא לקברות יובל ועל גדיש ישקוד׃
33 Dothi la ku chigwa limamukomera; anthu onse amatsatira mtembo wake, ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.
מתקו לו רגבי נחל ואחריו כל אדם ימשוך ולפניו אין מספר׃
34 “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”
ואיך תנחמוני הבל ותשובתיכם נשאר מעל׃

< Yobu 21 >