< Yobu 20 >

1 Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti
ויען צפר הנעמתי ויאמר׃
2 “Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe chifukwa ndasautsidwa kwambiri.
לכן שעפי ישיבוני ובעבור חושי בי׃
3 Ndikumva kudzudzula kondinyoza, ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe.
מוסר כלמתי אשמע ורוח מבינתי יענני׃
4 “Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale, kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi,
הזאת ידעת מני עד מני שים אדם עלי ארץ׃
5 kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha, chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa.
כי רננת רשעים מקרוב ושמחת חנף עדי רגע׃
6 Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba ndipo mutu wake uli nengʼaa,
אם יעלה לשמים שיאו וראשו לעב יגיע׃
7 iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe; iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’
כגללו לנצח יאבד ראיו יאמרו איו׃
8 Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso, adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku.
כחלום יעוף ולא ימצאוהו וידד כחזיון לילה׃
9 Diso limene linamuona silidzamuonanso; sadzapezekanso pamalo pake.
עין שזפתו ולא תוסיף ולא עוד תשורנו מקומו׃
10 Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka;
בניו ירצו דלים וידיו תשבנה אונו׃
11 Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake zidzagona naye limodzi mʼfumbi.
עצמותיו מלאו עלומו ועמו על עפר תשכב׃
12 “Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,
אם תמתיק בפיו רעה יכחידנה תחת לשונו׃
13 ngakhale salola kuzilavula, ndipo amazisunga mʼkamwa mwake,
יחמל עליה ולא יעזבנה וימנענה בתוך חכו׃
14 koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake; chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo.
לחמו במעיו נהפך מרורת פתנים בקרבו׃
15 Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.
חיל בלע ויקאנו מבטנו יורשנו אל׃
16 Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo ululu wa mphiri udzamupha.
ראש פתנים יינק תהרגהו לשון אפעה׃
17 Sadzasangalala ndi timitsinje, mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta.
אל ירא בפלגות נהרי נחלי דבש וחמאה׃
18 Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.
משיב יגע ולא יבלע כחיל תמורתו ולא יעלס׃
19 Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.
כי רצץ עזב דלים בית גזל ולא יבנהו׃
20 “Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.
כי לא ידע שלו בבטנו בחמודו לא ימלט׃
21 Palibe chatsala kuti iye adye; chuma chake sichidzachedwa kutha.
אין שריד לאכלו על כן לא יחיל טובו׃
22 Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera; mavuto aakulu adzamugwera.
במלאות שפקו יצר לו כל יד עמל תבואנו׃
23 Akadya nʼkukhuta, Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto ngati mvula yosalekeza.
יהי למלא בטנו ישלח בו חרון אפו וימטר עלימו בלחומו׃
24 Ngakhale athawe mkondo wachitsulo, muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa.
יברח מנשק ברזל תחלפהו קשת נחושה׃
25 Muviwo adzawutulutsira ku msana, songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake. Adzagwidwa ndi mantha aakulu;
שלף ויצא מגוה וברק ממררתו יהלך עליו אמים׃
26 mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake.
כל חשך טמון לצפוניו תאכלהו אש לא נפח ירע שריד באהלו׃
27 Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake; dziko lapansi lidzamuwukira.
יגלו שמים עונו וארץ מתקוממה לו׃
28 Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu.
יגל יבול ביתו נגרות ביום אפו׃
29 Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa, mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.”
זה חלק אדם רשע מאלהים ונחלת אמרו מאל׃

< Yobu 20 >