< Yobu 19 >
1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
Entonces Job respondió:
2 “Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti, ndi kundilasa ndi mawu anuwo?
¿Hasta cuándo afligen mi alma y me muelen con palabras?
3 Inuyo mwandinyoza kwambiri; mwanditsutsa mopanda manyazi.
Ya me insultaron diez veces. ¿No se avergüenzan de ultrajarme?
4 Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera, cholakwachotu nʼchanga.
Si en verdad yo erré, mi error recae sobre mí.
5 Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga, ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane,
Pero si ustedes se engrandecen contra mí, y alegan mi oprobio contra mí,
6 pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira ndipo wandizinga ukonde wake.
sepan que ʼElohim me trastornó y me envolvió en su red.
7 “Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha; ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama.
Ciertamente grito: ¡Violencia! Y no se me escucha. Doy voces, y no hay justicia.
8 Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa; waphimba njira zanga ndi mdima.
Él bloqueó mi camino para que no pase. Puso oscuridad sobre mi senda.
9 Iye wandilanda ulemu wanga ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.
Me despojó de mi honor y quitó la corona de mi cabeza.
10 Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu; Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.
Me destroza por todos lados y perezco. Arrancó mi esperanza como un árbol.
11 Wandikwiyira ndipo akundiyesa mmodzi mwa adani ake.
Su ira se encendió contra mí. Me considera su enemigo.
12 Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu, akonzekera zodzalimbana nane ndipo azungulira nyumba yanga.
Llegaron sus tropas unidas, se atrincheran contra mí y acamparon alrededor de mi vivienda.
13 “Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga; wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine.
Alejó a mis hermanos de mí. Mis conocidos, como extraños, se apartaron de mí.
14 Abale anga andithawa; abwenzi anga andiyiwala.
Me fallaron mis parientes, me olvidan mis amigos.
15 Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo; ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo.
Los que viven en mi casa y mis esclavas me miran como extraño. Soy forastero ante ellos.
16 Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha, ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu.
Llamo a mi esclavo, y no responde. Con mi propia boca tengo que rogarle.
17 Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga; ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.
Mi aliento fue repulsivo a mi esposa y odioso ante mis propios hermanos.
18 Inde, ngakhale ana amandinyoza; akandiona amandinyodola.
Hasta los niños me desprecian, y al levantarme hablan contra mí.
19 Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane; iwo amene ndinkawakonda andiwukira.
Todos mis amigos íntimos me aborrecen. Los que yo amaba se volvieron contra mí.
20 Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha; ndapulumuka lokumbakumba.
Mi piel y mi carne se pegan a mis huesos, y quedé solo con la piel de mis dientes.
21 “Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni, pakuti dzanja la Mulungu landikantha.
Ustedes, amigos míos, tengan compasión de mí. Porque me golpeó la mano de ʼElohim.
22 Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu? Kodi simunatope nalo thupi langa?
¿Por qué me persiguen como ʼElohim, y no se sacian de escarnecerme?
23 “Aa, achikhala mawu anga analembedwa, achikhala analembedwa mʼbuku,
¡Ojalá mis palabras fueran escritas! ¡Ojalá fueran escritas en un rollo!
24 akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo, akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!
¡Que fueran talladas con cincel de hierro y plomo para siempre en la roca!
25 Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo, ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
Yo sé que mi Redentor vive, y al fin se levantará sobre el polvo,
26 Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka, mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.
Después de deshecha mi piel, en mi carne veré a ʼElohim,
27 Ine ndemwe ndidzamuona Iye ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi. Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!
a Quien veré por mí mismo. Mis ojos lo verán, y no los de otro. Mi corazón desfallece dentro de mí.
28 “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji, popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’
Porque si la raíz de mi situación está en mí mismo, entonces, ¿por qué dicen ustedes: Persigámoslo?
29 Inu muyenera kuopa lupanga; pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga; zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”
¡Teman ustedes ante la espada! Porque llenos de ira están los castigos de la espada, para que sepan que hay un juicio.