< Yobu 18 >

1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
Then Bildad the Shuhite answered,
2 “Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi? Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.
"How long will you hunt for words? Consider, and afterwards we will speak.
3 Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?
Why are we counted as animals, which have become unclean in your sight?
4 Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako, kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo? Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?
You who tear yourself in your anger, shall the earth be forsaken for you? Or shall the rock be removed out of its place?
5 “Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa; malawi a moto wake sakuwalanso.
"Yes, the light of the wicked shall be put out, The spark of his fire shall not shine.
6 Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima; nyale ya pambali pake yazima.
The light shall be dark in his tent. His lamp above him shall be put out.
7 Mayendedwe ake amgugu azilala; fundo zake zomwe zamugwetsa.
The steps of his strength shall be shortened. His own counsel shall cast him down.
8 Mapazi ake amulowetsa mu ukonde ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.
For he is cast into a net by his own feet, and he wanders into its mesh.
9 Msampha wamkola mwendo; khwekhwe lamugwiritsitsa.
A snare will take him by the heel. A trap will catch him.
10 Amutchera msampha pansi mobisika; atchera diwa pa njira yake.
A noose is hidden for him in the ground, a trap for him in the way.
11 Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse, zikutsatira mayendedwe ake onse.
Terrors shall make him afraid on every side, and shall chase him at his heels.
12 Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala, tsoka likumudikira.
His strength shall be famished. Calamity shall be ready at his side.
13 Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse; miyendo yake, manja ake, zonse zawola.
The members of his body shall be devoured. The firstborn of death shall devour his members.
14 Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira, ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.
He shall be rooted out of his tent where he trusts. He shall be brought to the king of terrors.
15 Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo; awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.
There shall dwell in his tent that which is none of his. Sulfur shall be scattered on his habitation.
16 Mizu yake ikuwuma pansi ndipo nthambi zake zikufota
His roots shall be dried up beneath. Above shall his branch be cut off.
17 Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi; sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.
His memory shall perish from the earth. He shall have no name in the street.
18 Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima, ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.
He shall be driven from light into darkness, and chased out of the world.
19 Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake, kulibe wotsala kumene iye ankakhala.
He shall have neither son nor grandson among his people, nor any remaining where he sojourned.
20 Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake; anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.
Those who come after shall be astonished at his day, as those who went before were frightened.
21 Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa; amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”
Surely such are the dwellings of the unrighteous. This is the place of him who doesn't know God."

< Yobu 18 >