< Yobu 17 >

1 “Mtima wanga wasweka, masiku anga atha, manda akundidikira.
Тлею духом носимь, прошу же гроба и не улучаю.
2 Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira; maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.
Молю болезнуя, и что сотворю? Украдоша же ми имение чуждии.
3 “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna. Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?
Кто есть сей? Рукою моею связан да будет.
4 Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu; choncho simudzawalola kuti apambane.
Яко сердце их сокрыл еси от мудрости, сего ради да не вознесеши их.
5 Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma, ana ake sadzaona mwayi.
Части возвестит злобы: очи же на сынех истаяста.
6 “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense, munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.
Положил же мя еси в притчу во языцех, смех же бых им.
7 Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni; ndawonda ndi mutu womwe.
Ослепоста бо от гнева очи мои, повоеван бых вельми от всех:
8 Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi; anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.
чудо объя истинных о сем, праведник же на беззаконника да востанет:
9 Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo, ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.
да содержит же верный путь свой, чистый же рукама да приимет дерзость.
10 “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo, sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.
Но обаче вси належите и приидите, не бо обретаю в вас истины.
11 Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka, pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.
Дние мои преидоша в течении, расторгошася же удове сердца моего.
12 Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana, nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’
Нощь в день преложих: свет близ от лица тмы.
13 Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda, ngati ndiyala bedi langa mu mdima, (Sheol h7585)
Аще бо стерплю, ад ми есть дом, в сумраце же постлася ми постеля. (Sheol h7585)
14 ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’
Смерть назвах отца моего быти, матерь же и сестру ми гной.
15 tsono chiyembekezo changa chili kuti? Ndani angaone populumukira panga?
Где убо еще есть ми надежда, или благая моя узрю?
16 Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse, polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.” (Sheol h7585)
Или со мною во ад снидут, или вкупе в персть снидем. (Sheol h7585)

< Yobu 17 >