< Yobu 16 >

1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
ויען איוב ויאמר
2 “Ndinamvapo zambiri monga zimenezi; nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
שמעתי כאלה רבות מנחמי עמל כלכם
3 Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
הקץ לדברי-רוח או מה-ימריצך כי תענה
4 Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu, inuyo mukanakhala monga ndilili inemu; Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu ndi kukupukusirani mutu wanga.
גם אנכי-- ככם אדברה לו יש נפשכם תחת נפשי-- אחבירה עליכם במלים ואניעה עליכם במו ראשי
5 Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani; chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.
אאמצכם במו-פי וניד שפתי יחשך
6 “Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa; ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
אם-אדברה לא-יחשך כאבי ואחדלה מה-מני יהלך
7 Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu; mwawononga banja langa lonse.
אך-עתה הלאני השמות כל-עדתי
8 Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni; kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
ותקמטני לעד היה ויקם בי כחשי בפני יענה
9 Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane, amachita kulumira mano; mdani wanga amandituzulira maso.
אפו טרף וישטמני--חרק עלי בשניו צרי ילטש עיניו לי
10 Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza; amandimenya pa tsaya mwachipongwe ndipo amagwirizana polimbana nane.
פערו עלי בפיהם--בחרפה הכו לחיי יחד עלי יתמלאון
11 Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
יסגירני אל אל עויל ועל-ידי רשעים ירטני
12 Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
שלו הייתי ויפרפרני-- ואחז בערפי ויפצפצני ויקימני לו למטרה
13 anthu ake oponya mauta andizungulira. Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
יסבו עלי רביו-- יפלח כליותי ולא יחמל ישפך לארץ מררתי
14 Akundivulaza kawirikawiri, akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.
יפרצני פרץ על-פני-פרץ ירץ עלי כגבור
15 “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
שק תפרתי עלי גלדי ועללתי בעפר קרני
16 Maso anga afiira ndi kulira, ndipo zikope zanga zatupa;
פני חמרמרה (חמרמרו) מני-בכי ועל עפעפי צלמות
17 komatu manja anga sanachite zachiwawa ndipo pemphero langa ndi lolungama.
על לא-חמס בכפי ותפלתי זכה
18 “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga; kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
ארץ אל-תכסי דמי ואל-יהי מקום לזעקתי
19 Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
גם-עתה הנה-בשמים עדי ושהדי במרמים
20 Wondipembedzera ndi bwenzi langa, pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
מליצי רעי אל-אלוה דלפה עיני
21 iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu monga munthu amadandaulira bwenzi lake.
ויוכח לגבר עם-אלוה ובן-אדם לרעהו
22 “Pakuti sipapita zaka zambiri ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”
כי-שנות מספר יאתיו וארח לא-אשוב אהלך

< Yobu 16 >