< Yobu 15 >

1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
respondens autem Eliphaz Themanites dixit
2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere, kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
numquid sapiens respondebit quasi in ventum loquens et implebit ardore stomachum suum
3 Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake, kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
arguis verbis eum qui non est aequalis tui et loqueris quod tibi non expedit
4 Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
quantum in te est evacuasti timorem et tulisti preces coram Deo
5 Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo; ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
docuit enim iniquitas tua os tuum et imitaris linguam blasphemantium
6 Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga; milomo yakoyo ikukutsutsa.
condemnabit te os tuum et non ego et labia tua respondebunt tibi
7 “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
numquid primus homo tu natus es et ante colles formatus
8 Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
numquid consilium Dei audisti et inferior te erit eius sapientia
9 Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa? Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
quid nosti quod ignoremus quid intellegis quod nesciamus
10 Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu, anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
et senes et antiqui sunt in nobis multo vetustiores quam patres tui
11 Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira, mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
numquid grande est ut consoletur te Deus sed verba tua prava hoc prohibent
12 Chifukwa chiyani ukupsa mtima, ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
quid te elevat cor tuum et quasi magna cogitans adtonitos habes oculos
13 moti ukupsera mtima Mulungu ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?
quid tumet contra Deum spiritus tuus ut proferas de ore huiuscemodi sermones
14 “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
quid est homo ut inmaculatus sit et ut iustus appareat natus de muliere
15 Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake, ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
ecce inter sanctos eius nemo inmutabilis et caeli non sunt mundi in conspectu eius
16 nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota, amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.
quanto magis abominabilis et inutilis homo qui bibit quasi aquas iniquitatem
17 “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera; ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
ostendam tibi audi me quod vidi narrabo tibi
18 zimene anandiphunzitsa anthu anzeru, sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
sapientes confitentur et non abscondunt patres suos
19 (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
quibus solis data est terra et non transibit alienus per eos
20 Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake, munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
cunctis diebus suis impius superbit et numerus annorum incertus est tyrannidis eius
21 Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake, pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
sonitus terroris semper in auribus illius et cum pax sit ille insidias suspicatur
22 Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa; iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
non credit quod reverti possit de tenebris circumspectans undique gladium
23 Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya; amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
cum se moverit ad quaerendum panem novit quod paratus sit in manu eius tenebrarum dies
24 Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri; zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
terrebit eum tribulatio et angustia vallabit eum sicut regem qui praeparatur ad proelium
25 chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
tetendit enim adversus Deum manum suam et contra Omnipotentem roboratus est
26 Amapita mwa mwano kukalimbana naye atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.
cucurrit adversus eum erecto collo et pingui cervice armatus est
27 “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
operuit faciem eius crassitudo et de lateribus eius arvina dependet
28 munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu, nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
habitavit in civitatibus desolatis et in domibus desertis quae in tumulos sunt redactae
29 Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa, ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
non ditabitur nec perseverabit substantia eius nec mittet in terra radicem suam
30 Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo; lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake, ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
non recedet de tenebris ramos eius arefaciet flamma et auferetur spiritu oris sui
31 Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe, pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
non credat frustra errore deceptus quod aliquo pretio redimendus sit
32 Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane, ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
antequam dies eius impleantur peribit et manus eius arescet
33 Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse, adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
laedetur quasi vinea in primo flore botrus eius et quasi oliva proiciens florem suum
34 Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
congregatio enim hypocritae sterilis et ignis devorabit tabernacula eorum qui munera libenter accipiunt
35 Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa; mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”
concepit dolorem et peperit iniquitatem et uterus eius praeparat dolos

< Yobu 15 >