< Yobu 13 >
1 “Ndaziona ndi maso anga zonsezi, ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.
Voilà ce que mon œil a vu et ce qu'a entendu mon oreille.
2 Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa; ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
Tout ce que vous savez je le sais, et, non plus que vous, je ne manque d'intelligence.
3 Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.
Je parlerai donc au Seigneur; je me plaindrai devant lui, s'il ne s'y oppose pas.
4 Koma inu mukundipaka mabodza; nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!
Vous êtes des médecins iniques, et il y a des remèdes pour tous les maux.
5 Achikhala munangokhala chete nonsenu! Apo mukanachita zanzeru.
Que n'avez-vous gardé le silence? la sagesse vous viendrait.
6 Tsopano imvani kudzikanira kwanga; imvani kudandaula kwa pakamwa panga.
Ecoutez les reproches de ma bouche; recueillez le jugement que prononcent mes lèvres.
7 Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu? Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?
N'est-ce pas devant le Seigneur que vous avez discouru et que vous avez dit des mensonges?
8 Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera? Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?
Obéissez-vous à ses ordres? Non, vous vous étiez de vous-mêmes constitués juges.
9 Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa? Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?
C'est bien, s'il suit vos traces; et si, en tout ce que vous avez fait, vous vous êtes conformés à sa pensée,
10 Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani ngati muchita zokondera mseri.
Il ne vous adressera pas le moindre blâme. Mais si, en secret, vous avez eu égard aux apparences,
11 Kodi ulemerero wake sungakuopseni? Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?
Est-ce que son tourbillon ne vous enlèvera pas? L'épouvante qu'il répand tombera sur vous.
12 Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo; mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.
Votre orgueil se dispersera comme de la cendre; votre corps sera comme de la boue.
13 “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule; tsono zimene zindichitikire zichitike.
Ne m'interrompez pas; laissez-moi dire, et mon courroux se calmera.
14 Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
Je prendrai, avec mes dents, ma chair, et je mettrai mon âme sur ma main.
15 Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira; ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
Quand même le Tout-Puissant m'accablerait, puisque aussi bien il a commencé, je ne laisserais pas de parler et de me plaindre devant lui.
16 Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
C'est de là que viendra mon salut; car Dieu n'entendra de ma bouche aucune parole artificieuse.
17 Mvetserani mosamala mawu anga; makutu anu amve zimene ndikunena.
Ecoutez, écoutez mes raisonnements, car je me dévoilerai à vous qui me prêtez l'oreille.
18 Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga, ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
Me voici près du jugement, et je sens que je serai reconnu juste.
19 Kodi alipo wina amene angatsutsane nane? ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.
Car quel est celui qui comparaîtra avec moi devant le juge, pour que maintenant je me taise et que je déserte ma cause?
20 “Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi, ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:
Que deux choses mes soient accordées; alors, ô mon Dieu, je ne me cacherai point de vous.
21 Muchotse dzanja lanu pa ine, ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.
Détournez votre main qui me frappe; délivrez-moi de la crainte que vous inspirez.
22 Tsono muyitane ndipo ndidzayankha, kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.
Ensuite, appelez ma cause, et j'accourrai; accusez-moi, je ne vous ferai pas attendre ma défense.
23 Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati? Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.
Quels sont mes péchés et mes dérèglements? Apprenez-moi quels ils sont?
24 Chifukwa chiyani mukundifulatira ndi kundiyesa ine mdani wanu?
D'où vient que vous vous dérobez à mes regards? Montrez-moi le chemin qui mène à vous.
25 Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo? Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?
Ne me considérez-vous pas comme un adversaire semblable à la feuille desséchée que le moindre souffle emporte, ou au brin d'herbe fanée qu'entraîne le vent?
26 Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.
Et vous avez enregistré ce que je puis avoir fait de mal; et vous m'avez tenu compte des péchés de mon enfance.
27 Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo. Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.
Vous avez mis mes pieds en des entraves; vous avez observé toutes mes œuvres; vous avez cherché l'empreinte de tous mes pas.
28 “Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
Et je suis déjà comme une vieille outre, comme un manteau mangé des vers.