< Yobu 12 >

1 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
Respondens autem Iob, dixit:
2 “Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!
Ergo vos estis soli homines, et vobiscum morietur sapientia?
3 Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?
Et mihi est cor sicut et vobis, nec inferior vestri sum: quis enim haec, quae nostis, ignorat?
4 “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!
Qui deridetur ab amico suo sicut ego, invocabit Deum, et exaudiet eum: deridetur enim iusti simplicitas.
5 Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.
Lampas contempta apud cogitationes divitum, parata ad tempus statutum.
6 Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.
Abundant tabernacula praedonum, et audacter provocant Deum, cum ipse dederit omnia in manus eorum.
7 “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;
Nimirum interroga iumenta, et docebunt te: et volatilia caeli, et indicabunt tibi.
8 kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.
Loquere terrae, et respondebit tibi: et narrabunt pisces maris.
9 Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?
Quis ignorat quod omnia haec manus Domini fecerit?
10 Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
In cuius manu anima omnis viventis, et spiritus universae carnis hominis.
11 Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya?
Nonne auris verba diiudicat, et fauces comedentis, saporem?
12 Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?
In antiquis est sapientia, et in multo tempore prudentia.
13 “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.
Apud ipsum est sapientia et fortitudo, ipse habet consilium et intelligentiam.
14 Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.
Si destruxerit, nemo est qui aedificet: si incluserit hominem, nullus est qui aperiat.
15 Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.
Si continuerit aquas, omnia siccabuntur: et si emiserit eas, subvertent terram.
16 Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.
Apud ipsum est fortitudo et sapientia: ipse novit et decipientem, et eum qui decipitur.
17 Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza.
Adducit consiliarios in stultum finem, et iudices in stuporem.
18 Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.
Balteum regum dissolvit, et praecingit fune renes eorum.
19 Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.
Ducit sacerdotes inglorios, et optimates supplantat:
20 Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.
Commutans labium veracium, et doctrinam senum auferens.
21 Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.
Effundit despectionem super principes, eos, qui oppressi fuerant, relevans.
22 Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.
Qui revelat profunda de tenebris, et producit in lucem umbram mortis.
23 Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.
Qui multiplicat gentes et perdit eas, et subversas in integrum restituit.
24 Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.
Qui immutat cor principum populi terrae, et decipit eos ut frustra incedant per invium:
25 Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.
Palpabunt quasi in tenebris, et non in luce, et errare eos faciet quasi ebrios.

< Yobu 12 >