< Yobu 11 >
1 Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti,
2 “Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa? Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa?
3 Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza?
4 Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’
5 Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe
6 ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake, pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri. Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena.
7 “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?
8 Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani? Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani? (Sheol )
9 Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja.
10 “Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa?
11 Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo; akaona choyipa, kodi sachizindikira?
12 Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu.
13 “Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,
14 ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako,
15 udzatukula mutu wako wosachita manyazi; udzayima chilili ndipo sudzachita mantha.
16 Udzayiwala ndithu zowawa zako, zidzakhala ngati madzi amene apita kale.
17 Moyo wako udzawala kupambana usana, ndipo mdima udzakhala ngati mmawa.
18 Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo; ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka.
19 Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo.
20 Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza, ndipo adzasowa njira yothawirapo; chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.”