< Yeremiya 8 >
1 Yehova akuti, “‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa.
2 Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.
3 Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’”
4 “Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti: “‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso? Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
5 Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera? Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo? Iwo akangamira chinyengo; akukana kubwerera.
6 Ine ndinatchera khutu kumvetsera koma iwo sanayankhulepo zoona. Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake, nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’ Aliyense akutsatira njira yake ngati kavalo wothamangira nkhondo.
7 Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa nthawi yake mlengalenga. Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo, koma anthu anga sadziwa malamulo a Yehova.
8 “‘Inu mukunena bwanji kuti, ‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’ Koma ndi alembi anu amene akulemba zabodza.
9 Anthu anzeru achita manyazi; athedwa nzeru ndipo agwidwa. Iwo anakana mawu a Yehova. Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo.
11 Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba chabe nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere.
12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi? Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe; iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga, akutero Yehova.
13 “‘Ndidzatenga zokolola zawo, Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa kapena nkhuyu pa mkuyu, ndipo masamba ake adzawuma. Zinthu zimene ndinawapatsa ndidzawachotsera.’”
14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani? Tiyeni tonse pamodzi tithawire ku mizinda yotetezedwa ndi kukafera kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa. Watipatsa madzi aululu kuti timwe, chifukwa tamuchimwira.
15 Tinkayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chinachitika, tinkayembekezera kuchira koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.
16 Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani kukumveka kuchokera ku Dani; dziko lonse likunjenjemera chifukwa cha kulira kwa akavalowo. Akubwera kudzawononga dziko ndi zonse zimene zili mʼmenemo. Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
17 Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu, mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza, ndipo zidzakulumani,”
18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri, mtima wanga walefukiratu.
19 Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali: akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake sili kumeneko?” “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema, ndi milungu yawo yachilendo?”
20 “Nthawi yokolola yapita, chilimwe chapita, koma sitinapulumuke.”
21 Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa; ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.
22 Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe singʼanga? Nanga chifukwa chiyani mabala a anthu anga sanapole?