< Yeremiya 6 >

1 “Thawani, inu anthu a ku Benjamini! Tulukani mu Yerusalemu! Lizani lipenga ku Tekowa! Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu! Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto, ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
הָעִ֣זוּ ׀ בְּנֵ֣י בִניָמִ֗ן מִקֶּ֙רֶב֙ יְר֣וּשָׁלִַ֔ם וּבִתְק֙וֹעַ֙ תִּקְע֣וּ שׁוֹפָ֔ר וְעַל־בֵּ֥ית הַכֶּ֖רֶם שְׂא֣וּ מַשְׂאֵ֑ת כִּ֥י רָעָ֛ה נִשְׁקְפָ֥ה מִצָּפ֖וֹן וְשֶׁ֥בֶר גָּדֽוֹל׃
2 Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri, kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
הַנָּוָה֙ וְהַמְּעֻנָּגָ֔ה דָּמִ֖יתִי בַּת־צִיּֽוֹן׃
3 Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo; adzamanga matenti awo mowuzinga, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”
אֵלֶ֛יהָ יָבֹ֥אוּ רֹעִ֖ים וְעֶדְרֵיהֶ֑ם תָּקְע֨וּ עָלֶ֤יהָ אֹהָלִים֙ סָבִ֔יב רָע֖וּ אִ֥ישׁ אֶת־יָדֽוֹ׃
4 Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo! Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano. Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka, ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
קַדְּשׁ֤וּ עָלֶ֙יהָ֙ מִלְחָמָ֔ה ק֖וּמוּ וְנַעֲלֶ֣ה בַֽצָּהֳרָ֑יִם א֥וֹי לָ֙נוּ֙ כִּי־פָנָ֣ה הַיּ֔וֹם כִּ֥י יִנָּט֖וּ צִלְלֵי־עָֽרֶב׃
5 Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno ndi kuwononga malinga ake!”
ק֚וּמוּ וְנַעֲלֶ֣ה בַלָּ֔יְלָה וְנַשְׁחִ֖יתָה אַרְמְנוֹתֶֽיהָ׃ ס
6 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Dulani mitengo ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu. Mzinda umenewu uyenera kulangidwa; wadzaza ndi kuponderezana.
כִּ֣י כֹ֤ה אָמַר֙ יְהוָ֣ה צְבָא֔וֹת כִּרְת֣וּ עֵצָ֔ה וְשִׁפְכ֥וּ עַל־יְרוּשָׁלִַ֖ם סֹלְלָ֑ה הִ֚יא הָעִ֣יר הָפְקַ֔ד כֻּלָּ֖הּ עֹ֥שֶׁק בְּקִרְבָּֽהּ׃
7 Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake. Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo; nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
כְּהָקִ֥יר בַּ֙יִר֙ מֵימֶ֔יהָ כֵּ֖ן הֵקֵ֣רָה רָעָתָ֑הּ חָמָ֣ס וָ֠שֹׁד יִשָּׁ֨מַע בָּ֧הּ עַל־פָּנַ֛י תָּמִ֖יד חֳלִ֥י וּמַכָּֽה׃
8 Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja mopanda munthu wokhalamo.”
הִוָּסְרִי֙ יְר֣וּשָׁלִַ֔ם פֶּן־תֵּקַ֥ע נַפְשִׁ֖י מִמֵּ֑ךְ פֶּן־אֲשִׂימֵ֣ךְ שְׁמָמָ֔ה אֶ֖רֶץ ל֥וֹא נוֹשָֽׁבָה׃ פ
9 Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti, “Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli, monga momwe amachitira populula mphesa. Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
כֹּ֤ה אָמַר֙ יְהֹוָ֣ה צְבָא֔וֹת עוֹלֵ֛ל יְעוֹלְל֥וּ כַגֶּ֖פֶן שְׁאֵרִ֣ית יִשְׂרָאֵ֑ל הָשֵׁב֙ יָדְךָ֔ כְּבוֹצֵ֖ר עַל־סַלְסִלּֽוֹת׃
10 Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza? Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve? Makutu awo ndi otsekeka kotero kuti sangathe kumva. Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo; sasangalatsidwa nawo.
עַל־מִ֨י אֲדַבְּרָ֤ה וְאָעִ֙ידָה֙ וְיִשְׁמָ֔עוּ הִנֵּה֙ עֲרֵלָ֣ה אָזְנָ֔ם וְלֹ֥א יוּכְל֖וּ לְהַקְשִׁ֑יב הִנֵּ֣ה דְבַר־יְהוָ֗ה הָיָ֥ה לָהֶ֛ם לְחֶרְפָּ֖ה לֹ֥א יַחְפְּצוּ־בֽוֹ׃
11 Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova, ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova. Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi; pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
וְאֵת֩ חֲמַ֨ת יְהוָ֤ה ׀ מָלֵ֙אתִי֙ נִלְאֵ֣יתִי הָכִ֔יל שְׁפֹ֤ךְ עַל־עוֹלָל֙ בַּח֔וּץ וְעַ֛ל ס֥וֹד בַּחוּרִ֖ים יַחְדָּ֑ו כִּֽי־גַם־אִ֤ישׁ עִם־אִשָּׁה֙ יִלָּכֵ֔דוּ זָקֵ֖ן עִם־מְלֵ֥א יָמִֽים׃
12 Nyumba zawo adzazipereka kwa ena, pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo. Ndidzatambasula dzanja langa kukantha anthu okhala mʼdzikomo,” akutero Yehova.
וְנָסַ֤בּוּ בָֽתֵּיהֶם֙ לַאֲחֵרִ֔ים שָׂד֥וֹת וְנָשִׁ֖ים יַחְדָּ֑ו כִּֽי־אַטֶּ֧ה אֶת־יָדִ֛י עַל־יֹשְׁבֵ֥י הָאָ֖רֶץ נְאֻם־יְהוָֽה׃
13 “Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba; aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo.
כִּ֤י מִקְּטַנָּם֙ וְעַד־גְּדוֹלָ֔ם כֻּלּ֖וֹ בּוֹצֵ֣עַ בָּ֑צַע וּמִנָּבִיא֙ וְעַד־כֹּהֵ֔ן כֻּלּ֖וֹ עֹ֥שֶׂה שָּֽׁקֶר׃
14 Amapoletsa zilonda za anthu anga pamwamba pokha. Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’ pamene palibe mtendere.
וַֽיְרַפְּא֞וּ אֶת־שֶׁ֤בֶר עַמִּי֙ עַל־נְקַלָּ֔ה לֵאמֹ֖ר שָׁל֣וֹם ׀ שָׁל֑וֹם וְאֵ֖ין שָׁלֽוֹם׃
15 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo? Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe; sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,” akutero Yehova.
הֹבִ֕ישׁוּ כִּ֥י תוֹעֵבָ֖ה עָשׂ֑וּ גַּם־בּ֣וֹשׁ לֹֽא־יֵב֗וֹשׁוּ גַּם־הַכְלִים֙ לֹ֣א יָדָ֔עוּ לָכֵ֞ן יִפְּל֧וּ בַנֹּפְלִ֛ים בְּעֵת־פְּקַדְתִּ֥ים יִכָּשְׁל֖וּ אָמַ֥ר יְהוָֽה׃ ס
16 Yehova akuti, “Imani pa mphambano ndipo mupenye; kumeneko ndiye kuli njira zakale, funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
כֹּ֣ה אָמַ֣ר יְהוָ֡ה עִמְדוּ֩ עַל־דְּרָכִ֨ים וּרְא֜וּ וְשַׁאֲל֣וּ ׀ לִנְתִב֣וֹת עוֹלָ֗ם אֵי־זֶ֨ה דֶ֤רֶךְ הַטּוֹב֙ וּלְכוּ־בָ֔הּ וּמִצְא֥וּ מַרְגּ֖וֹעַ לְנַפְשְׁכֶ֑ם וַיֹּאמְר֖וּ לֹ֥א נֵלֵֽךְ׃
17 Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’ koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
וַהֲקִמֹתִ֤י עֲלֵיכֶם֙ צֹפִ֔ים הַקְשִׁ֖יבוּ לְק֣וֹל שׁוֹפָ֑ר וַיֹּאמְר֖וּ לֹ֥א נַקְשִֽׁיב׃
18 Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina; yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano, chimene chidzawachitikire anthuwo.
לָכֵ֖ן שִׁמְע֣וּ הַגּוֹיִ֑ם וּדְעִ֥י עֵדָ֖ה אֶת־אֲשֶׁר־בָּֽם׃
19 Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi, ndikubweretsa masautso pa anthu awa. Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo. Iwowa sanamvere mawu anga ndipo anakana lamulo langa.
שִׁמְעִ֣י הָאָ֔רֶץ הִנֵּ֨ה אָנֹכִ֜י מֵבִ֥יא רָעָ֛ה אֶל־הָעָ֥ם הַזֶּ֖ה פְּרִ֣י מַחְשְׁבוֹתָ֑ם כִּ֤י עַל־דְּבָרַי֙ לֹ֣א הִקְשִׁ֔יבוּ וְתוֹרָתִ֖י וַיִּמְאֲסוּ־בָֽהּ׃
20 Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba, kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali? Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira; nsembe zanu sizindikondweretsa.”
לָמָּה־זֶּ֨ה לִ֤י לְבוֹנָה֙ מִשְּׁבָ֣א תָב֔וֹא וְקָנֶ֥ה הַטּ֖וֹב מֵאֶ֣רֶץ מֶרְחָ֑ק עֹלֽוֹתֵיכֶם֙ לֹ֣א לְרָצ֔וֹן וְזִבְחֵיכֶ֖ם לֹא־עָ֥רְבוּ לִֽי׃ ס
21 Choncho Yehova akuti, “Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa. Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa; anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
לָכֵ֗ן כֹּ֚ה אָמַ֣ר יְהוָ֔ה הִנְנִ֥י נֹתֵ֛ן אֶל־הָעָ֥ם הַזֶּ֖ה מִכְשֹׁלִ֑ים וְכָ֣שְׁלוּ בָ֠ם אָב֨וֹת וּבָנִ֥ים יַחְדָּ֛ו שָׁכֵ֥ן וְרֵע֖וֹ וְאָבָֽדוּ׃ פ
22 Yehova akunena kuti, “Taonani, gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
כֹּ֚ה אָמַ֣ר יְהוָ֔ה הִנֵּ֛ה עַ֥ם בָּ֖א מֵאֶ֣רֶץ צָפ֑וֹן וְג֣וֹי גָּד֔וֹל יֵע֖וֹר מִיַּרְכְּתֵי־אָֽרֶץ׃
23 Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo. Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo, kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
קֶ֣שֶׁת וְכִיד֞וֹן יַחֲזִ֗יקוּ אַכְזָרִ֥י הוּא֙ וְלֹ֣א יְרַחֵ֔מוּ קוֹלָם֙ כַּיָּ֣ם יֶהֱמֶ֔ה וְעַל־סוּסִ֖ים יִרְכָּ֑בוּ עָר֗וּךְ כְּאִישׁ֙ לַמִּלְחָמָ֔ה עָלַ֖יִךְ בַּת־צִיּֽוֹן׃
24 A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo, ndipo manja anthu alefukiratu. Nkhawa yatigwira, ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
שָׁמַ֥עְנוּ אֶת־שָׁמְע֖וֹ רָפ֣וּ יָדֵ֑ינוּ צָרָה֙ הֶחֱזִיקַ֔תְנוּ חִ֖יל כַּיּוֹלֵדָֽה׃
25 Musapite ku minda kapena kuyenda mʼmisewu, pakuti mdani ali ndi lupanga, ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
אַל־תֵּֽצְאוּ֙ הַשָּׂדֶ֔ה וּבַדֶּ֖רֶךְ אַל־תֵּלֵ֑כוּ כִּ֚י חֶ֣רֶב לְאֹיֵ֔ב מָג֖וֹר מִסָּבִֽיב׃
26 Inu anthu anga, valani ziguduli ndipo gubudukani pa phulusa; lirani mwamphamvu ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi wowonongayo adzabwera kudzatipha.
בַּת־עַמִּ֤י חִגְרִי־שָׂק֙ וְהִתְפַּלְּשִׁ֣י בָאֵ֔פֶר אֵ֤בֶל יָחִיד֙ עֲשִׂ֣י לָ֔ךְ מִסְפַּ֖ד תַּמְרוּרִ֑ים כִּ֣י פִתְאֹ֔ם יָבֹ֥א הַשֹּׁדֵ֖ד עָלֵֽינוּ׃
27 “Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo. Uwayese anthu anga monga ungayesere chitsulo kuti uwone makhalidwe awo.
בָּח֛וֹן נְתַתִּ֥יךָ בְעַמִּ֖י מִבְצָ֑ר וְתֵדַ֕ע וּבָחַנְתָּ֖ אֶת־דַּרְכָּֽם׃
28 Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira ndipo akunka nanena zamiseche. Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo. Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
כֻּלָּם֙ סָרֵ֣י סֽוֹרְרִ֔ים הֹלְכֵ֥י רָכִ֖יל נְחֹ֣שֶׁת וּבַרְזֶ֑ל כֻּלָּ֥ם מַשְׁחִיתִ֖ים הֵֽמָּה׃
29 Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri; mtovu watha kusungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
נָחַ֣ר מַפֻּ֔חַ מֵאֵ֖שׁ תַּ֣ם עֹפָ֑רֶת לַשָּׁוְא֙ צָרַ֣ף צָר֔וֹף וְרָעִ֖ים לֹ֥א נִתָּֽקוּ׃
30 Iwo ali ngati siliva wotayidwa, chifukwa Yehova wawakana.”
כֶּ֣סֶף נִמְאָ֔ס קָרְא֖וּ לָהֶ֑ם כִּֽי־מָאַ֥ס יְהוָ֖ה בָּהֶֽם׃ פ

< Yeremiya 6 >