< Yeremiya 51 >

1 Yehova akuti, “Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowononga kuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai.
כה אמר יהוה הנני מעיר על בבל ואל ישבי לב קמי--רוח משחית
2 Ndidzatuma alendo ku Babuloni kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu. Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse pa tsiku la masautso ake.
ושלחתי לבבל זרים וזרוה ויבקקו את ארצה כי היו עליה מסביב ביום רעה
3 Okoka uta musawalekerere kapena wonyadira chovala chawo chankhondo. Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo; koma muwononge ankhondo ake kotheratu.
אל ידרך ידרך הדרך קשתו ואל יתעל בסרינו ואל תחמלו אל בחריה--החרימו כל צבאה
4 Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.
ונפלו חללים בארץ כשדים ומדקרים בחוצותיה
5 Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse, koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo pamaso pa Woyerayo wa Israeli.
כי לא אלמן ישראל ויהודה מאלהיו--מיהוה צבאות כי ארצם מלאה אשם מקדוש ישראל
6 “Thawaniko ku Babuloni! Aliyense apulumutse moyo wake! Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake. Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange; Yehova adzamulipsira.
נסו מתוך בבל ומלטו איש נפשו--אל תדמו בעונה כי עת נקמה היא ליהוה--גמול הוא משלם לה
7 Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova; kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake; nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
כוס זהב בבל ביד יהוה--משכרת כל הארץ מיינה שתו גוים על כן יתהללו גוים
8 Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka. Mulireni! Mfunireni mankhwala opha ululu wake; mwina iye nʼkuchira.”
פתאם נפלה בבל ותשבר הילילו עליה קחו צרי למכאובה--אולי תרפא
9 Ena anati, “‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni, koma sanachire; tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo, pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga, wafika mpaka kumwamba.’
רפאנו את בבל ולא נרפתה--עזבוה ונלך איש לארצו כי נגע אל השמים משפטה ונשא עד שחקים
10 “‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa; tiyeni tilengeze mu Ziyoni zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’
הוציא יהוה את צדקתינו באו ונספרה בציון את מעשה יהוה אלהינו
11 “Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi, popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni. Motero adzalipsira Ababuloni chifukwa chowononga Nyumba yake. Ndiye Yehova akuti, ‘Nolani mivi, tengani zishango.’
הברו החצים מלאו השלטים--העיר יהוה את רוח מלכי מדי כי על בבל מזמתו להשחיתה כי נקמת יהוה היא נקמת היכלו
12 Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni! Limbitsani oteteza, ikani alonda pa malo awo, konzekerani kulalira. Pakuti Yehova watsimikiza ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
אל חומת בבל שאו נס החזיקו המשמר--הקימו שמרים הכינו הארבים כי גם זמם יהוה--גם עשה את אשר דבר אל ישבי בבל
13 Inu muli ndi mitsinje yambiri ndi chuma chambiri. Koma chimaliziro chanu chafika, moyo wanu watha.
שכנתי (שכנת) על מים רבים רבת אוצרת בא קצך אמת בצעך
14 Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti: Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe, kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.
נשבע יהוה צבאות בנפשו כי אם מלאתיך אדם כילק וענו עליך הידד
15 “Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.
עשה ארץ בכחו מכין תבל בחכמתו ובתבונתו נטה שמים
16 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba. Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.
לקול תתו המון מים בשמים ויעל נשאים מקצה ארץ ברקים למטר עשה ויוצא רוח מאצרתיו
17 “Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo.
נבער כל אדם מדעת הביש כל צרף מפסל כי שקר נסכו ולא רוח בם
18 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
הבל המה מעשה תעתעים בעת פקדתם יאבדו
19 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse, kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
לא כאלה חלק יעקוב כי יוצר הכל הוא--ושבט נחלתו יהוה צבאות שמו
20 “Iwe Babuloni ndi ndodo yanga, chida changa chankhondo. Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu, ndi iwe ndimawononga maufumu,
מפץ אתה לי כלי מלחמה ונפצתי בך גוים והשחתי בך ממלכות
21 ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo, ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.
ונפצתי בך סוס ורכבו ונפצתי בך רכב ורכבו
22 Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi, ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata, ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
ונפצתי בך איש ואשה ונפצתי בך זקן ונער ונפצתי בך בחור ובתולה
23 Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto, ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe, ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.
ונפצתי בך רעה ועדרו ונפצתי בך אכר וצמדו ונפצתי בך פחות וסגנים
24 “Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.
ושלמתי לבבל ולכל יושבי כשדים את כל רעתם אשר עשו בציון--לעיניכם נאם יהוה
25 “Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga, amene umawononga dziko lonse lapansi,” akutero Yehova. “Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga, kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako, ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera.
הנני אליך הר המשחית נאם יהוה המשחית את כל הארץ ונטיתי את ידי עליך וגלגלתיך מן הסלעים ונתתיך להר שרפה
26 Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba, chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,” akutero Yehova.
ולא יקחו ממך אבן לפנה ואבן למוסדות כי שממות עולם תהיה נאם יהוה
27 “Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko! Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu! Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo; itanani maufumu awa: Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye; tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.
שאו נס בארץ תקעו שופר בגוים קדשו עליה גוים--השמיעו עליה ממלכות אררט מני ואשכנז פקדו עליה טפסר העלו סוס כילק סמר
28 Konzekeretsani mitundu ya anthu. Amenewa ndiwo mafumu a Amedi, abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo, ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.
קדשו עליה גוים את מלכי מדי את פחותיה ואת כל סגניה ואת כל ארץ ממשלתו
29 Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira, chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni; kusakaza dziko la Babuloni kuti musapezeke wokhalamo.
ותרעש הארץ ותחל כי קמה על בבל מחשבות יהוה לשום את ארץ בבל לשמה מאין יושב
30 Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo; iwo angokhala mʼmalinga awo. Mphamvu zawo zatheratu; ndipo akhala ngati akazi. Malo ake wokhala atenthedwa; mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
חדלו גבורי בבל להלחם ישבו במצדות--נשתה גבורתם היו לנשים הציתו משכנתיה נשברו בריחיה
31 Othamanga akungopezanapezana, amithenga akungotsatanatsatana kudzawuza mfumu ya ku Babuloni kuti alande mzinda wake wonse.
רץ לקראת רץ ירוץ ומגיד לקראת מגיד--להגיד למלך בבל כי נלכדה עירו מקצה
32 Madooko onse alandidwa, malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto, ndipo ankhondo onse asokonezeka.”
והמעברות נתפשו ואת האגמים שרפו באש ואנשי המלחמה נבהלו
33 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti, Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”
כי כה אמר יהוה צבאות אלהי ישראל בת בבל כגרן עת הדריכה עוד מעט ובאה עת הקציר לה
34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga, watiphwanya, ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ngʼona, wakhuta ndi zakudya zathu zokoma, kenaka nʼkutilavula.”
אכלנו (אכלני) הממנו (הממני) נבוכדראצר מלך בבל הציגנו (הציגני) כלי ריק בלענו (בלעני) כתנין מלא כרשו מעדני הדיחנו (הדיחני)
35 Anthu a ku Ziyoni anene kuti, “Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.” Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti, “Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”
חמסי ושארי על בבל תאמר ישבת ציון ודמי אל ישבי כשדים תאמר ירושלם
36 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Taona, ndidzakumenyera nkhondo ndi kukulipsirira; ndidzawumitsa nyanja yake ndipo akasupe ake adzaphwa.
לכן כה אמר יהוה הנני רב את ריבך ונקמתי את נקמתך והחרבתי את ימה והבשתי את מקורה
37 Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka, malo okhala nkhandwe, malo ochititsa mantha ndi onyozedwa, malo wopanda aliyense wokhalamo.
והיתה בבל לגלים מעון תנים שמה ושרקה מאין יושב
38 Anthu ake onse adzabangula ngati mkango, adzadzuma ngati ana amkango.
יחדו ככפרים ישאגו נערו כגורי אריות
39 Ngati achita dyera ndiye ndidzawakonzera madyerero ndi kuwaledzeretsa, kotero kuti adzasangalala, kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,” akutero Yehova.
בחמם אשית את משתיהם והשכרתים למען יעלזו וישנו שנת עולם ולא יקיצו--נאם יהוה
40 “Ine ndidzawatenga kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa, ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
אורידם ככרים לטבוח--כאילים עם עתודים
41 “Ndithu Babuloni walandidwa, mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa! Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ya anthu!
איך נלכדה ששך ותתפש תהלת כל הארץ איך היתה לשמה בבל בגוים
42 Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni; mafunde ake okokoma aphimba Babuloni.
עלה על בבל הים בהמון גליו נכסתה
43 Mizinda yake yasanduka bwinja, dziko lowuma ndi lachipululu, dziko losakhalamo wina aliyense, dziko losayendamo munthu aliyense.
היו עריה לשמה ארץ ציה וערבה ארץ לא ישב בהן כל איש ולא יעבר בהן בן אדם
44 Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni, ndidzamusanzitsa zimene anameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babuloni agwa.
ופקדתי על בל בבבל והצאתי את בלעו מפיו ולא ינהרו אליו עוד גוים גם חומת בבל נפלה
45 “Tulukani mʼBabuloni anthu anga! Pulumutsani miyoyo yanu! Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova.
צאו מתוכה עמי ומלטו איש את נפשו--מחרון אף יהוה
46 Musataye mtima kapena kuchita mantha pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu. Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera za ziwawa mʼdziko lapansi, ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.
ופן ירך לבבכם ותיראו בשמועה הנשמעת בארץ ובא בשנה השמועה ואחריו בשנה השמועה וחמס בארץ ומשל על משל
47 Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni; dziko lake lonse lidzachita manyazi ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
לכן הנה ימים באים ופקדתי על פסילי בבל וכל ארצה תבוש וכל חלליה יפלו בתוכה
48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni. Anthu owononga ochokera kumpoto adzamuthira nkhondo,” akutero Yehova.
ורננו על בבל שמים וארץ וכל אשר בהם כי מצפון יבוא לה השודדים נאם יהוה
49 “Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi. Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwa chifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.
גם בבל לנפל חללי ישראל גם לבבל נפלו חללי כל הארץ
50 Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni, chokani pano ndipo musazengereze! Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali, ganizirani za Yerusalemu.”
פלטים מחרב הלכו אל תעמדו זכרו מרחוק את יהוה וירושלם תעלה על לבבכם
51 Inu mukuti, “Tikuchita manyazi, chifukwa tanyozedwa ndipo nkhope zathu zili ndi manyazi, chifukwa anthu achilendo alowa malo opatulika a Nyumba ya Yehova.”
בשנו כי שמענו חרפה כסתה כלמה פנינו כי באו זרים על מקדשי בית יהוה
52 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake, ndipo mʼdziko lake lonse anthu ovulala adzabuwula.
לכן הנה ימים באים נאם יהוה ופקדתי על פסיליה ובכל ארצה יאנק חלל
53 Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga ndi kulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,” akutero Yehova.
כי תעלה בבל השמים וכי תבצר מרום עזה מאתי יבאו שדדים לה--נאם יהוה
54 “Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni. Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulu kuchokera mʼdziko la Babuloni.
קול זעקה מבבל ושבר גדול מארץ כשדים
55 Pakuti Yehova akuwononga Babuloni, ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu. Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri. Phokoso lawo likunka likwererakwerera.
כי שדד יהוה את בבל ואבד ממנה קול גדול והמו גליהם כמים רבים נתן שאון קולם
56 Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni, ankhondo ake agwidwa, ndipo mauta awo athyoka. Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango; adzabwezera kwathunthu.
כי בא עליה על בבל שודד ונלכדו גבוריה חתתה קשתותם כי אל גמלות יהוה שלם ישלם
57 Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake, abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo; adzagona kwamuyaya osadzukanso,” akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
והשכרתי שריה וחכמיה פחותיה וסגניה וגבוריה וישנו שנת עולם ולא יקיצו נאם המלך--יהוה צבאות שמו
58 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa; mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe. Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
כה אמר יהוה צבאות חמות בבל הרחבה ערער תתערער ושעריה הגבהים באש יצתו ויגעו עמים בדי ריק ולאמים בדי אש ויעפו
59 Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo.
הדבר אשר צוה ירמיהו הנביא את שריה בן נריה בן מחסיה בלכתו את צדקיהו מלך יהודה בבל בשנת הרבעית למלכו ושריה שר מנוחה
60 Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni.
ויכתב ירמיהו את כל הרעה אשר תבוא אל בבל--אל ספר אחד את כל הדברים האלה הכתבים אל בבל
61 Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa.
ויאמר ירמיהו אל שריה כבאך בבל--וראית וקראת את כל הדברים האלה
62 Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’
ואמרת יהוה אתה דברת אל המקום הזה להכריתו לבלתי היות בו יושב למאדם ועד בהמה כי שממות עולם תהיה
63 Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate.
והיה ככלתך לקרא את הספר הזה תקשר עליו אבן והשלכתו אל תוך פרת
64 Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’” Mawu a Yeremiya athera pamenepa.
ואמרת ככה תשקע בבל ולא תקום מפני הרעה אשר אנכי מביא עליה--ויעפו עד הנה דברי ירמיהו

< Yeremiya 51 >