< Yeremiya 50 >
1 Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu:
2 “Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina, kweza mbendera ndipo ulengeze; usabise kanthu, koma uwawuze kuti, ‘Babuloni wagwa; mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha. Milungu yake yagwidwa ndi mantha ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’
3 Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni ndi kusandutsa bwinja dziko lake. Kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.
4 “Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.
5 Adzafunsa njira ya ku Ziyoni ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko. Iwo adzadzipereka kwa Yehova pochita naye pangano lamuyaya limene silidzayiwalika.
6 “Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika; abusa awo anawasocheretsa mʼmapiri. Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda mpaka kuyiwala kwawo.
7 Aliyense amene anawapeza anawawononga; adani awo anati, ‘Ife si olakwa, chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniweni ndi amene makolo awo anamukhulupirira.’
8 “Thawaniko ku Babuloni; chokani mʼdziko la Ababuloni. Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto.
9 Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto kudzamenyana ndi Babuloni. Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni. Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso, yosapita padera.
10 Motero Ababuloni adzafunkhidwa; ndipo onse omufunkha adzakhuta,” akutero Yehova.
11 “Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika. Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala. Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.
12 Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri. Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa. Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse. Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.
13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu ndipo adzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.
14 “Inu okoka uta, konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse. Muponyereni mivi yanu yonse chifukwa anachimwira Yehova.
15 Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja. Nsanja zake zagwa. Malinga ake agwetsedwa. Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova. Mulipsireni, mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.
16 Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense, ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola. Poona lupanga la ozunza anzawo, aliyense adzabwerera kwa anthu ake; adzathawira ku dziko la kwawo.
17 “Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika pothamangitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo. Wotsiriza anali Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”
18 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.
19 Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani; adzadya nakhuta ku mapiri a ku Efereimu ndi Giliyadi.
20 Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe, ndipo adzafufuza machimo a Yuda, koma sadzapeza ndi limodzi lomwe, chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.
21 “Lithireni nkhondo dziko la Merataimu ndi anthu okhala ku Pekodi. Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,” akutero Yehova. “Chitani zonse monga momwe ndakulamulani.
22 Mʼdziko muli phokoso la nkhondo, phokoso la chiwonongeko chachikulu!
23 Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi. Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ina!
24 Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni, ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu; unapezeka ndiponso unakodwa chifukwa unalimbana ndi Yehova.
25 Yehova watsekula nyumba ya zida zake ndipo watulutsa zida za ukali wake, pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire mʼdziko la Ababuloni.
26 Mumenyane naye Babuloni mbali zonse. Anthu ake muwawunjike ngati milu ya tirigu. Muwawononge kotheratu ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
27 Iphani ankhondo ake onse. Onse aphedwe ndithu. Tsoka lawagwera pakuti tsiku lawo lachilango lafika.
28 Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloni akulengeza mu Yerusalemu za kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu. Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake.
29 “Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni. Muyitanenso onse amene amakoka mauta. Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira; musalole munthu aliyense kuthawa. Muchiteni monga momwe iye anachitira anthu ena. Iyeyu ananyoza Yehova, Woyera wa Israeli.
30 Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake; ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,” akutero Yehova.
31 “Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,” akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse, “chifukwa tsiku lako lafika, nthawi yoti ndikulange yakwana.
32 Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwa ndipo palibe amene adzakudzutse; ndidzayatsa moto mʼmizinda yake umene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.”
33 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu a ku Israeli akuzunzidwa, pamodzi ndi anthu a ku Yuda, ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa, akukana kuwamasula.
34 Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu; dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo, koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”
35 Yehova akuti, “Imfa yalunjika pa Ababuloni, pa akuluakulu ake ndi pa anthu ake a nzeru!
36 Imfa yalunjika pa aneneri abodza kuti asanduke zitsiru. Imfa yalunjika pa ankhondo ake kuti agwidwe ndi mantha aakulu.
37 Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake. Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo kuti asanduke ngati akazi. Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake kuti chidzafunkhidwe.
38 Chilala chilunjike pa madzi ake kuti aphwe. Babuloni ndi dziko la mafano, ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.
39 “Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko ndipo kudzakhalanso akadzidzi. Kumeneko sikudzapezekako anthu, ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.
40 Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora pamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,” akutero Yehova, “momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko; anthu sadzayendanso mʼmenemo.
41 “Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto; mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri, wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
42 Atenga mauta ndi mikondo; ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo. Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo awo, ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo iwe Babuloni.
43 Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo, ndipo yalobodokeratu. Ikuda nkhawa, ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.
44 Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani kupita ku msipu wobiriwira, momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi. Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine. Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane? Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”
45 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
46 Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera, ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.