< Yeremiya 5 >
1 “Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu, mudzionere nokha, funafunani mʼmabwalo ake. Ngati mungapeze munthu mmodzi amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi, ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
2 Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ komabe akungolumbira mwachinyengo.”
3 Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona? Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka; munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala ndipo anakaniratu kulapa.
4 Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe; anthu ochita zopusa. Sadziwa njira ya Yehova, sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
5 Tsono ndidzapita kwa atsogoleri ndi kukayankhula nawo; ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova, amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.” Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova ndipo anadula msinga zawo.
6 Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha, mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga, kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
7 Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita? Ana anu andisiya Ine ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse. Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa, komabe iwo anachita chigololo namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
8 Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa, aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
9 Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?” akutero Yehova. “Kodi nʼkuleka kuwulipsira mtundu woterewu?
10 “Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga, koma musakayiwononge kotheratu. Sadzani nthambi zake pakuti anthu amenewa si a Yehova.
11 Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
12 Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti, “Yehova sangachite zimenezi! Choyipa sichidzatigwera; sitidzaona nkhondo kapena njala.
13 Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo; ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova. Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
14 Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa, tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
15 Inu Aisraeli,” Yehova akuti, “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali, ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo, mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa, zimene akunena inu simungazimvetse.
16 Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri; onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
17 Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu, adzapha ana anu aamuna ndi aakazi; adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu, adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu. Ndi malupanga awo adzagwetsa mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova.
19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobo ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru, inu amene maso muli nawo koma simupenya, amene makutu muli nawo koma simumva.
22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira; andifulatira ndipo andisiyiratu.
24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti, ‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu. Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika. Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi; ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo ngati zikwere zodzaza ndi mbalame. Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28 Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala. Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire; saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino, sateteza ufulu wa anthu osauka.
29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi? Kodi ndisawulipsire mtundu woterewu? Akutero Yehova.
30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri chachitika mʼdzikomo:
31 Aneneri akunenera zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo, ndipo anthu anga akukonda zimenezi. Koma mudzatani potsiriza?