< Yeremiya 49 >

1 Yehova ananena izi: Amoni, “Kodi Israeli alibe ana aamuna? Kapena alibe mlowamʼmalo? Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi? Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
Of the children of Ammon. Yahweh says: “Has Israel no sons? Has he no heir? Why then does Malcam possess Gad, and his people dwell in its cities?
2 Koma nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo ku Raba, likulu la Amoni; ndipo malo awo opembedzera milungu yawo adzatenthedwa ndi moto. Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,” akutero Yehova.
Therefore behold, the days come,” says Yahweh, “that I will cause an alarm of war to be heard against Rabbah of the children of Ammon, and it will become a desolate heap, and her daughters will be burned with fire; then Israel will possess those who possessed him,” says Yahweh.
3 “Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika! Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba! Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu; thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga, chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
“Wail, Heshbon, for Ai is laid waste! Cry, you daughters of Rabbah! Clothe yourself in sackcloth. Lament, and run back and forth among the fences; for Malcam will go into captivity, his priests and his princes together.
4 Chifukwa chiyani mukunyadira chigwa chanu, inu anthu osakhulupirika amene munadalira chuma chanu nʼkumati: ‘Ndani angandithire nkhondo?’
Why do you boast in the valleys, your flowing valley, backsliding daughter? You trusted in her treasures, saying, ‘Who will come to me?’
5 Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe zochokera kwa onse amene akuzungulira,” akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse. “Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake. Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.
Behold, I will bring a terror on you,” says the Lord, Yahweh of Armies, “from all who are around you. All of you will be driven completely out, and there will be no one to gather together the fugitives.
6 “Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,” akutero Yehova.
“But afterward I will reverse the captivity of the children of Ammon,” says Yahweh.
7 Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu: “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani? Kodi anzeru analeka kupereka uphungu? Kodi nzeru zawo zinatheratu?
Of Edom, Yahweh of Armies says: “Is wisdom no more in Teman? Has counsel perished from the prudent? Has their wisdom vanished?
8 Inu anthu a ku Dedani, thawani, bwererani ndi kukabisala ku makwalala chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
Flee! Turn back! Dwell in the depths, inhabitants of Dedan; for I will bring the calamity of Esau on him when I visit him.
9 Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha? Anthu akuba akanafika usiku akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
If grape gatherers came to you, would they not leave some gleaning grapes? If thieves came by night, wouldn’t they steal until they had enough?
10 Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau. Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo, kotero kuti sadzathanso kubisala. Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka. Palibe wonena kuti,
But I have made Esau bare, I have uncovered his secret places, and he will not be able to hide himself. His offspring is destroyed, with his brothers and his neighbors; and he is no more.
11 ‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza. Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’”
Leave your fatherless children. I will preserve them alive. Let your widows trust in me.”
12 Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho.
For Yahweh says: “Behold, they to whom it didn’t pertain to drink of the cup will certainly drink; and are you he who will altogether go unpunished? You won’t go unpunished, but you will surely drink.
13 Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
For I have sworn by myself,” says Yahweh, “that Bozrah will become an astonishment, a reproach, a waste, and a curse. All its cities will be perpetual wastes.”
14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova: Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu! Konzekerani nkhondo!”
I have heard news from Yahweh, and an ambassador is sent among the nations, saying, “Gather yourselves together! Come against her! Rise up to the battle!”
15 “Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina. Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
“For, behold, I have made you small among the nations, and despised among men.
16 Kuopseza kwako kwakunyenga; kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa, iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri. Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga, ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,” akutero Yehova.
As for your terror, the pride of your heart has deceived you, O you who dwell in the clefts of the rock, who hold the height of the hill, though you should make your nest as high as the eagle, I will bring you down from there,” says Yahweh.
17 “Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake.
“Edom will become an astonishment. Everyone who passes by it will be astonished, and will hiss at all its plagues.
18 Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora, pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,” akutero Yehova, “motero palibe munthu amene adzakhala mu Edomu.
As in the overthrow of Sodom and Gomorrah and its neighbor cities,” says Yahweh, “no man will dwell there, neither will any son of man live therein.
19 “Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
“Behold, he will come up like a lion from the pride of the Jordan against the strong habitation; for I will suddenly make them run away from it, and whoever is chosen, I will appoint him over it. For who is like me? Who will appoint me a time? Who is the shepherd who will stand before me?”
20 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani. Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
Therefore hear the counsel of Yahweh, that he has taken against Edom, and his purposes that he has purposed against the inhabitants of Teman: Surely they will drag them away, the little ones of the flock. Surely he will make their habitation desolate over them.
21 Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera; kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
The earth trembles at the noise of their fall; there is a cry, the noise which is heard in the Red Sea.
22 Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Behold, he will come up and fly as the eagle, and spread out his wings against Bozrah. The heart of the mighty men of Edom at that day will be as the heart of a woman in her pangs.
23 Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa: “Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha chifukwa amva nkhani yoyipa. Mitima yawo yagwidwa ndi mantha ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
Of Damascus: “Hamath and Arpad are confounded, for they have heard evil news. They have melted away. There is sorrow on the sea. It can’t be quiet.
24 Anthu a ku Damasiko alefuka. Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu. Ali ndi nkhawa komanso mantha ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
Damascus has grown feeble, she turns herself to flee, and trembling has seized her. Anguish and sorrows have taken hold of her, as of a woman in travail.
25 Mzinda wotchuka ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
How is the city of praise not forsaken, the city of my joy?
26 Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa; ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Therefore her young men will fall in her streets, and all the men of war will be brought to silence in that day,” says Yahweh of Armies.
27 “Ndidzatentha malinga a Damasiko; moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
“I will kindle a fire in the wall of Damascus, and it will devour the palaces of Ben Hadad.”
28 Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa: “Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara. Kawonongeni anthu a kummawako.
Of Kedar, and of the kingdoms of Hazor, which Nebuchadnezzar king of Babylon struck, Yahweh says: “Arise, go up to Kedar, and destroy the children of the east.
29 Landani matenti awo ndi nkhosa zawo, ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo. Mutengenso ngamira zawo. Anthu adzafuwula kwa iwo kuti, ‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
They will take their tents and their flocks. they will carry away for themselves their curtains, all their vessels, and their camels; and they will cry to them, ‘Terror on every side!’
30 “Thawani mofulumira! Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,” akutero Yehova. “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu; wakonzekera zoti alimbane nanu.
Flee! Wander far off! Dwell in the depths, you inhabitants of Hazor,” says Yahweh; “for Nebuchadnezzar king of Babylon has taken counsel against you, and has conceived a purpose against you.
31 “Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere, umene ukukhala mosatekeseka,” akutero Yehova, “mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo; anthu ake amakhala pa okha.
Arise! Go up to a nation that is at ease, that dwells without care,” says Yahweh; “that has neither gates nor bars, that dwells alone.
32 Ngamira zawo zidzafunkhidwa, ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa. Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali. Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,” akutero Yehova.
Their camels will be a booty, and the multitude of their livestock a plunder. I will scatter to all winds those who have the corners of their beards cut off; and I will bring their calamity from every side of them,” says Yahweh.
33 “Hazori adzasanduka bwinja, malo okhalamo nkhandwe mpaka muyaya. Palibe munthu amene adzayendemo.”
Hazor will be a dwelling place of jackals, a desolation forever. No man will dwell there, neither will any son of man live therein.”
34 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:
Yahweh’s word that came to Jeremiah the prophet concerning Elam, in the beginning of the reign of Zedekiah king of Judah, saying,
35 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, umene uli chida chawo champhamvu.
“Yahweh of Armies says: ‘Behold, I will break the bow of Elam, the chief of their might.
36 Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga; ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi, ndipo sipadzakhala dziko limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
I will bring on Elam the four winds from the four quarters of the sky, and will scatter them toward all those winds. There will be no nation where the outcasts of Elam will not come.
37 A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo. Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga ndipo adzakhala pa mavuto,” akutero Yehova. “Ndidzawapirikitsa ndi lupanga mpaka nditawatheratu.
I will cause Elam to be dismayed before their enemies, and before those who seek their life. I will bring evil on them, even my fierce anger,’ says Yahweh; ‘and I will send the sword after them, until I have consumed them.
38 Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,” akutero Yehova.
I will set my throne in Elam, and will destroy from there king and princes,’ says Yahweh.
39 “Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera anthu a ku Elamu dziko lawo,” akutero Yehova.
‘But it will happen in the latter days that I will reverse the captivity of Elam,’ says Yahweh.”

< Yeremiya 49 >