< Yeremiya 48 >
1 Ponena za Mowabu: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa. Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa; linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
2 Palibenso amene akutamanda Mowabu; ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa: ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’ Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete; ankhondo adzakupirikitsani.
3 Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu. Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
4 Mowabu wawonongeka; ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
5 Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti, akulira kwambiri pamene akupita. Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka pa njira yotsikira ku Horonaimu.
6 Thawani! Dzipulumutseni; khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
7 Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu, nanunso mudzatengedwa ukapolo, ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
8 Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse, ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke. Chigwa chidzasanduka bwinja ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa monga Yehova wayankhulira.
9 Mtsineni khutu Mowabu chifukwa adzasakazika; mizinda yake idzasanduka mabwinja, wopanda munthu wokhalamo.
10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika! Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!
11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina; iye sanatengedwepo ukapolo. Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja ndipo fungo lake silinasinthe.
12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko ndipo adzamukhutula; adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, monga momwe Aisraeli anachitira manyazi ndi Beteli amene ankamukhutulira.
14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali. Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
15 Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake; anyamata ake okongola apita kukaphedwa,” ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16 Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi; masautso ake akubwera posachedwa.
17 Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira, inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake; nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija, taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”
18 “Tsikani pa ulemerero wanu ndipo khalani pansi powuma, inu anthu okhala ku Diboni, pakuti wowononga Mowabu wabwera kudzamenyana nanu, wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
19 Inu amene mumakhala ku Aroeri, imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera. Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka, afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’”
20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika. Lirani mwachisoni ndipo fuwulani! Lengezani ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wawonongedwa.
21 Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri, ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
22 Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
23 Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
24 Keriyoti ndi Bozira ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
25 Mphamvu za Mowabu zawonongeka; mkono wake wathyoka,” akutero Yehova.
26 “Muledzeretseni Mowabu, chifukwa anadzikuza powukira Yehova. Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake; mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
27 Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka? Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba kuti nthawi zonse poyankhula za iye, iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
28 Inu amene mumakhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe. Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake pa khomo la phanga.
29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu, kunyada kwake nʼkwakukulu. Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula. Ali ndi mtima wodzikweza.
30 Ine ndikuzidziwa ntchito zake, akutero Yehova. Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
31 Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu, ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu, ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri. Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja; zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri. Wowononga wasakaza zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
33 Chimwemwe ndi chisangalalo zatha ku minda ya zipatso ya ku Mowabu. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa; palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa. Ngakhale kufuwula kulipo, koma sikufuwula kwa chimwemwe.
34 “A ku Hesiboni ndi Eleali akulira ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi, kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya. Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35 Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,” akutero Yehova.
36 “Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
37 Aliyense wameta mutu wake ndi ndevu zake; manja a munthu aliyense ndi ochekacheka, ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
38 Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso mʼmisewu yake anthu akungolira, pakuti ndaphwanya Mowabu ngati mtsuko wopanda ntchito,” akutero Yehova.
39 “Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira! Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi. Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
40 Yehova akuti, “Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
41 Mizinda idzagwidwa ndipo malinga adzalandidwa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
42 Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
43 Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira inu anthu a ku Mowabu,” akutero Yehova.
44 “Aliyense wothawa zoopsa adzagwera mʼdzenje, aliyense wotuluka mʼdzenje adzakodwa mu msampha. Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu pa nthawi ya chilango chake,” akutero Yehova.
45 “Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni chifukwa chotopa. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni. Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu onyada.
46 Tsoka kwa iwe Mowabu! Anthu opembedza Kemosi awonongeka. Ana ako aamuna ndi aakazi atengedwa ukapolo.
47 “Komabe masiku akutsogolo ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,” akutero Yehova. Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.