< Yeremiya 40 >

1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya pamene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anamasula Yeremiyayo ku Rama. Anamupeza Yeremiya ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi amʼndende ena onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene ankapita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
Communication adressée à Jérémie de la part de l’Eternel, après que Nebouzaradan, chef des gardes, l’eut renvoyé de Rama: ce dernier le fit chercher alors que, chargé de chaînes, il se trouvait confondu avec tous les expatriés de Jérusalem et de Juda que l’on déportait à Babylone.
2 Mtsogoleriyu anamupeza Yeremiya, anamuwuza kuti, “Yehova Mulungu wako analengeza kale zakuti malo ano adzawonongedwa.
Le chef des gardes se fit amener Jérémie et lui dit: "L’Eternel, ton Dieu, avait décrété cette calamité contre ce pays.
3 Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere.
Il l’a amenée et consommée, l’Eternel, comme il l’avait annoncée; car vous avez prévariqué contre le Seigneur et refusé d’écouter sa voix, et ainsi ces événements vous ont atteints.
4 Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.”
Et maintenant, voici que je te délivre aujourd’hui des chaînes dont tes bras sont chargés. S’Il te plaît de venir avec moi à Babylone, viens, et je veillerai sur ta personne; mais s’il ne te convient pas de m’accompagner à Babylone, n’en fais rien. Examine tout le pays que tu as devant toi et va où il te paraîtra bon et convenable d’aller."
5 Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.” Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite.
Et comme il ne s’en retournait pas encore, Nebouzaradan ajouta: "Retourne donc auprès de Ghedalia, fils d’Ahikam, fils de Chafan, que le roi de Babylone a placé à la tête des villes de Juda, et demeure avec lui parmi le peuple; ou s’il te plaît d’aller ailleurs, tu peux le faire." Et le chef des gardes lui remit des provisions et des présents et le congédia.
6 Motero Yeremiya anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa ndipo anakakhala naye kumeneko pakati pa anthu amene anatsala mʼdzikomo.
Jérémie se rendit auprès de Ghedalia; fils d’Ahikam, à Miçpa, et demeura avec lui au milieu de la population qui était restée dans le pays.
7 Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni.
Lorsque les chefs de troupes, qui se tenaient dans les campagnes, eux et leurs hommes, apprirent que le roi de Babylone avait confié à Ghedalla, fils d’Ahikam, le gouvernement du pays et placé sous son autorité hommes, femmes et enfants, appartenant à la population pauvre du pays qui n’avait pas été déportée à Babylone,
8 Iwowa anapita ku Mizipa kwa Gedaliya. Amene anapitawo ndi awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana a Efai a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu awo.
ils se rendirent auprès de Ghedalia à Miçpa: c’étaient Ismaël, fils de Netania, Johanan et Jonathan, fils de Karéah, Seraïa, fils de Tanhoumet, les fils d’Efaï de Netofa, et Yaazania, fils du Maakhatite, eux et leurs hommes.
9 Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.
Ghedalia, fils d’Ahikam, fils de Chafan, les adjura eux et leurs hommes en disant: "Ne craignez pas de servir les Chaldéens; demeurez dans le pays, soyez les sujets du roi de Babylone, et vous vous en trouverez bien.
10 Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.”
Pour moi, je vais résider à Miçpa, afin de rester en rapports avec les Chaldéens qui viendront à nous; et vous, recueillez du vin, des fruits, de l’huile, pour les mettre dans vos vases, et établissez-vous dans les villes dont vous avez pris possession."
11 Nawonso Ayuda onse a ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu ndi a ku mayiko ena onse anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasiyako anthu ena ku Yuda ndipo kuti inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala bwanamkubwa wawo.
De même tous les Judéens, répandus dans Moab, parmi les Ammonites, dans Edom et dans tous les autres pays, avaient appris que le roi de Babylone avait laissé une colonie en Judée et confié sa direction à Ghedalia, fils d’Ahikam, fils de Chafan.
12 Tsono Ayuda onsewo anabwerera ku Yuda, ku Mizipa kwa Gedaliya, kuchokera ku mayiko onse kumene anabalalikira. Ndipo anakolola zipatso zochuluka ndi vinyo wambiri.
Tous ces Judéens revinrent donc de toutes les contrées où ils étaient relégués. et se rendirent auprès de Ghedalia à Miçpa; puis ils recueillirent du vin et des fruits en grande quantité.
13 Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a ankhondo onse amene sanadzipereke aja anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya
Or Johanan, fils de Karéah et tous les officiers de troupes qui se tenaient dans les campagnes vinrent trouver Ghedalia à Miçpa,
14 ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire.
et lui dirent: "Sais-tu que Baalis, roi des Ammonites, a chargé Ismaël, fils de Netania, de t’assassiner?" Mais Ghedalla, fils d’Ahikam, ne les crut point.
15 Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwamseri anawuza Gedaliya ku Mizipa kuti, “Loleni ndipite ndikaphe Ismaeli mwana wa Netaniya, ndipo palibe amene ati adziwe. Akuphereninji ndi kuchititsa Ayuda onse, amene akuzungulirani kuti abalalike ndi kuti otsala a ku Yuda awonongeke?”
Même, Johanan, fils de Karéah, avait dit confidentiellement à Ghedalia, dans la ville de Miçpa: "Laisse-moi donc aller moi-même frapper à mort Ismaël, fils de Netania, sans que personne le sache! Pourquoi te prendrait-il la vie? Pourquoi permettre, que tous les Judéens, rassemblés autour de toi, se dispersent et que c’en soit fait du reste de Juda?"
16 Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anawuza Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Usachite zimenezo! Zimene ukunena za Ismaeli ndi zabodza.”
Mais Ghedalia, fils d’Ahikam, répondit à Johanan, fils de Karéah: "Ne commets pas un pareil acte; car tu accuses faussement Ismaël."

< Yeremiya 40 >