< Yeremiya 4 >

1 “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli, bwererani kwa Ine,” akutero Yehova. “Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga ndipo musasocherenso.
אם תשוב ישראל נאם יהוה אלי תשוב ואם תסיר שקוציך מפני ולא תנוד
2 Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’ Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse ndipo adzanditamanda.”
ונשבעת חי יהוה באמת במשפט ובצדקה והתברכו בו גוים ובו יתהללו
3 Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi: “Limani masala anu musadzale pakati pa minga.
כי כה אמר יהוה לאיש יהודה ולירושלם נירו לכם ניר ואל תזרעו אל קצים
4 Dziperekeni nokha kwa Ine kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse, inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani, chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo popanda wina wowuzimitsa.
המלו ליהוה והסרו ערלות לבבכם איש יהודה וישבי ירושלם פן תצא כאש חמתי ובערה ואין מכבה--מפני רע מעלליכם
5 “Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti, ‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’ Ndipo fuwulani kuti, ‘Sonkhanani! Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
הגידו ביהודה ובירושלם השמיעו ואמרו ותקעו (תקעו) שופר בארץ קראו מלאו ואמרו האספו ונבואה אל ערי המבצר
6 Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni! Musachedwe, thawani kuti mupulumuke! Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
שאו נס ציונה העיזו אל תעמדו כי רעה אנכי מביא מצפון--ושבר גדול
7 Monga mkango umatulukira mʼngaka yake momwemonso wowononga mayiko wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake. Watero kuti awononge dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda wokhalamo.
עלה אריה מסבכו ומשחית גוים נסע יצא ממקמו--לשום ארצך לשמה עריך תצינה מאין יושב
8 Choncho valani ziguduli, lirani ndi kubuwula, pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova sunatichokere.
על זאת חגרו שקים ספדו והילילו כי לא שב חרון אף יהוה ממנו
9 “Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima, ansembe adzachita mantha kwambiri, ndipo aneneri adzathedwa nzeru,” akutero Yehova.
והיה ביום ההוא נאם יהוה יאבד לב המלך ולב השרים ונשמו הכהנים והנבאים יתמהו
10 Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
ואמר אהה אדני יהוה אכן השא השאת לעם הזה ולירושלם לאמר שלום יהיה לכם ונגעה חרב עד הנפש
11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa;
בעת ההיא יאמר לעם הזה ולירושלם רוח צח שפים במדבר דרך בת עמי--לוא לזרות ולוא להבר
12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
רוח מלא מאלה יבוא לי עתה גם אני אדבר משפטים אותם
13 Taonani, adani akubwera ngati mitambo, magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu, akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga. Tsoka ilo! Tawonongeka!
הנה כעננים יעלה וכסופה מרכבותיו--קלו מנשרים סוסיו אוי לנו כי שדדנו
14 Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
כבסי מרעה לבך ירושלם למען תושעי עד מתי תלין בקרבך מחשבות אונך
15 Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani; akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
כי קול מגיד מדן ומשמיע און מהר אפרים
16 Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina, lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti, ‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
הזכירו לגוים הנה השמיעו על ירושלם נצרים באים מארץ המרחק ויתנו על ערי יהודה קולם
17 Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda, chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’” akutero Yehova.
כשמרי שדי היו עליה מסביב כי אתי מרתה נאם יהוה
18 “Makhalidwe anu ndi zochita zanu zakubweretserani zimenezi. Chimenechi ndiye chilango chanu. Nʼchowawa kwambiri! Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
דרכך ומעלליך עשו אלה לך זאת רעתך כי מר כי נגע עד לבך
19 Mayo, mayo, ndikumva kupweteka! Aa, mtima wanga ukupweteka, ukugunda kuti thi, thi, thi. Sindingathe kukhala chete. Pakuti ndamva kulira kwa lipenga; ndamva mfuwu wankhondo.
מעי מעי אחולה (אחילה) קירות לבי המה לי לבי--לא אחרש כי קול שופר שמעתי (שמעת) נפשי תרועת מלחמה
20 Tsoka limatsata tsoka linzake; dziko lonse lasanduka bwinja. Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa, mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
שבר על שבר נקרא כי שדדה כל הארץ פתאם שדדו אהלי רגע יריעתי
21 Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo, ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
עד מתי אראה נס--אשמעה קול שופר
22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.”
כי אויל עמי אותי לא ידעו--בנים סכלים המה ולא נבונים המה חכמים המה להרע ולהיטיב לא ידעו
23 Ndinayangʼana dziko lapansi, ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu; ndinayangʼana thambo, koma linalibe kuwala kulikonse.
ראיתי את הארץ והנה תהו ובהו ואל השמים ואין אורם
24 Ndinayangʼana mapiri, ndipo ankagwedezeka; magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
ראיתי ההרים והנה רעשים וכל הגבעות התקלקלו
25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu; mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
ראיתי והנה אין האדם וכל עוף השמים נדדו
26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu; mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
ראיתי והנה הכרמל המדבר וכל עריו נתצו מפני יהוה--מפני חרון אפו
27 Yehova akuti, “Dziko lonse lidzasanduka chipululu komabe sindidzaliwononga kotheratu.
כי כה אמר יהוה שממה תהיה כל הארץ וכלה לא אעשה
28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira ndipo thambo lidzachita mdima, pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima, ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
על זאת תאבל הארץ וקדרו השמים ממעל--על כי דברתי זמתי ולא נחמתי ולא אשוב ממנה
29 Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi, anthu a mʼmizinda adzathawa. Ena adzabisala ku nkhalango; ena adzakwera mʼmatanthwe mizinda yonse nʼkuyisiya; popanda munthu wokhalamo.
מקול פרש ורמה קשת ברחת כל העיר--באו בעבים ובכפים עלו כל העיר עזובה ואין יושב בהן איש
30 Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja! Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira ndi kuvalanso zokometsera zagolide? Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera, ukungodzivuta chabe. Zibwenzi zako zikukunyoza; zikufuna kuchotsa moyo wako.
ואתי (ואת) שדוד מה תעשי כי תלבשי שני כי תעדי עדי זהב כי תקרעי בפוך עיניך--לשוא תתיפי מאסו בך עגבים נפשך יבקשו
31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka, kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba. Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu. Atambalitsa manja awo nʼkumati, “Kalanga ife! Tikukomoka. Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
כי קול כחולה שמעתי צרה כמבכירה--קול בת ציון תתיפח תפרש כפיה אוי נא לי כי עיפה נפשי להרגים

< Yeremiya 4 >