< Yeremiya 35 >
1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, kuti:
Palabra que vino a Jeremías de parte de Yahvé en los días de Joacim hijo de Josías, rey de Judá, diciendo:
2 “Pita ku banja la Arekabu ndipo ukawayitane kuti abwere mʼchipinda chimodzi cha Nyumba ya Yehova ndipo akafika uwapatse vinyo kuti amwe.”
“Ve a la casa de los recabitas y habla con ellos, y hazlos entrar en la casa de Yahvé, en una de las habitaciones, y dales de beber vino.”
3 Choncho ndinakatenga Yaazaniya (mwana wa Yeremiya winanso amene anali mwana wa Habaziniya), abale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu.
Entonces tomé a Jaazanías hijo de Jeremías, hijo de Habazzinías, con sus hermanos, con todos sus hijos y con toda la casa de los recabitas;
4 Ndinabwera nawo ku Nyumba ya Yehova, ku chipinda cha ophunzira a mneneri Hanani mwana wa Igidaliya, munthu wa Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, chimene chinali pamwamba pa chipinda cha Maaseya mwana wa Salumu, mlonda wa pa khomo.
y los llevé a la casa de Yahvé, a la habitación de los hijos de Hanán hijo de Igdaliah, el hombre de Dios, que estaba junto a la habitación de los príncipes, que estaba encima de la habitación de Maasías hijo de Salum, el guardián del umbral.
5 Kenaka ndinayika mabotolo odzaza ndi vinyo ndi zikho zake pamaso pa Arekabu ndipo ndinawawuza kuti, “Imwani vinyoyu.”
Puse delante de los hijos de la casa de los recabitas tazones llenos de vino y copas, y les dije: “¡Beban vino!”
6 Koma iwo anayankha kuti, “Ife sitimwa vinyo, chifukwa kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula kuti, ‘Inuyo ngakhale zidzukulu zanu, musadzamwe vinyo mpaka kalekale.
Pero ellos dijeron: “No beberemos vino, porque Jonadab, hijo de Recab, nuestro padre, nos lo ordenó diciendo: “No beberéis vino, ni vosotros ni vuestros hijos, para siempre.
7 Musadzamange nyumba kapena kufesa mbewu, kapena kulima minda ya mpesa; musadzakhale ndi zinthu zimenezi. Mʼmalo mwake muzidzakhale mʼmatenti. Mukadzatero mudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukukhalamo.’
No construiréis casa, ni sembraréis semilla, ni plantaréis viña, ni tendréis nada; sino que todos vuestros días habitaréis en tiendas, para que viváis muchos días en la tierra en que vivís como nómadas.’
8 Ife takhala tikumvera zonse zimene kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula. Ife ngakhale akazi athu kapena ana athu aamuna ndi aakazi sitinamwepo vinyo
Hemos obedecido la voz de Jonadab, hijo de Recab, nuestro padre, en todo lo que nos ordenó: no beber vino en todos nuestros días, ni nosotros, ni nuestras mujeres, ni nuestros hijos, ni nuestras hijas;
9 kapena kumanga nyumba kuti tizikhalamo kapenanso kukhala ndi minda ya mpesa, minda ina iliyonse kapena mbewu.
y no construir casas para habitarlas. No tenemos viña, ni campo, ni semilla;
10 Koma takhala mʼmatenti ndipo tamvera kwathunthu chilichonse chimene kholo lathu Yehonadabu anatilamula.
sino que hemos vivido en tiendas, y hemos obedecido y hecho conforme a todo lo que nos mandó nuestro padre Jonadab.
11 Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.”
Pero cuando Nabucodonosor, rey de Babilonia, subió al país, dijimos: “¡Ven! Vayamos a Jerusalén por miedo al ejército de los caldeos, y por miedo al ejército de los sirios; así moraremos en Jerusalén’”.
12 Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya kuti,
Entonces vino la palabra de Yahvé a Jeremías, diciendo:
13 “Iyeyu, Yehova Mulungu wa Israeli anawuza Yeremiya kuti: Pita ukawawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko phunziro ndi kumvera mawu anga?’ akutero Yehova.
“Yahvé de los Ejércitos, el Dios de Israel, dice: ‘Ve y di a los hombres de Judá y a los habitantes de Jerusalén: “¿No recibiréis instrucción para escuchar mis palabras?”, dice Yahvé.
14 ‘Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamwe vinyo ndipo lamulo limeneli alisunga. Mpaka lero lino iwo samwa vinyo, chifukwa akumvera lamulo la kholo lawo. Koma Ine ndakhala ndikuyankhula nanu kawirikawiri kukuchenjezani, koma inu simunandimvere Ine.
“Las palabras de Jonadab, hijo de Recab, que ordenó a sus hijos que no bebieran vino, se han cumplido; y hasta el día de hoy no beben, pues obedecen el mandato de su padre; pero yo os he hablado, madrugando y hablando, y no me habéis escuchado.
15 Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine.
También os he enviado a todos mis siervos los profetas, madrugando y enviándolos, diciendo: ‘Cada uno de vosotros debe volver ahora de su mal camino, enmendar sus acciones y no ir tras otros dioses para servirles. Entonces habitaréis en la tierra que os he dado a vosotros y a vuestros padres;’ pero no habéis inclinado vuestro oído ni me habéis escuchado.
16 Zidzukulu za Yehonadabu mwana wa Rekabu zakhala zikumvera lamulo limene kholo lawo anazilamula, koma inuyo simunandimvere Ine.
Los hijos de Jonadab, hijo de Recab, han cumplido el mandamiento de su padre que él les ordenó, pero este pueblo no me ha escuchado.”’
17 “Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndidzagwetsera pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu masautso onse amene ndinakonza chifukwa sanandimvere. Ndinawayitana koma iwo sanayankhe.’”
“Por tanto, Yahvé, el Dios de los Ejércitos, el Dios de Israel, dice: ‘He aquí que yo traigo sobre Judá y sobre todos los habitantes de Jerusalén todo el mal que he pronunciado contra ellos, porque les he hablado, pero no han escuchado; y los he llamado, pero no han respondido.’”
18 Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.”
Jeremías dijo a la casa de los recabitas: “Yahvé de los Ejércitos, el Dios de Israel, dice: ‘Porque habéis obedecido el mandato de Jonadab, vuestro padre, y habéis guardado todos sus preceptos, y habéis hecho conforme a todo lo que os ha mandado’,
19 Tsono Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Yehonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wonditumikira Ine nthawi zonse.”
por lo tanto Yahvé de los Ejércitos, el Dios de Israel, dice: ‘A Jonadab, hijo de Recab, no le faltará un hombre que esté delante de mí para siempre’”.