< Yeremiya 28 >
1 Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti,
W tym samym roku, na początku królowania Sedekiasza, króla Judy, w piątym miesiącu czwartego roku, Chananiasz, syn Azzura, prorok, który [był] z Gibeonu, powiedział do mnie w domu PANA przed kapłanami i przed całym ludem:
2 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.
Tak mówi PAN zastępów, Bóg Izraela: Złamałem jarzmo króla Babilonu.
3 Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni.
W ciągu dwóch lat sprowadzę z powrotem na to miejsce wszystkie naczynia domu PANA, które Nabuchodonozor, król Babilonu, zabrał z tego miejsca i zawiózł je do Babilonu.
4 Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’”
Także Jechoniasza, syna Joakima, króla Judy, i wszystkich uprowadzonych z Judy, którzy dostali się do Babilonu, ja sprowadzę z powrotem na to miejsce, mówi PAN. Skruszę bowiem jarzmo króla Babilonu.
5 Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova.
Wtedy prorok Jeremiasz powiedział do proroka Chananiasza wobec kapłanów i wobec całego ludu, który stał w domu PANA;
6 Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni.
Prorok Jeremiasz powiedział: Amen, niech PAN tak uczyni! Niech PAN utwierdzi twoje słowa, które prorokowałeś, że sprowadzi z Babilonu na to miejsce naczynia domu PANA i wszystkich, którzy zostali uprowadzeni do niewoli.
7 Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse:
Posłuchaj jednak teraz tego słowa, które ja mówię do twoich uszu i do uszu całego tego ludu:
8 Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu.
Prorocy, którzy byli przede mną i przed tobą od dawna, prorokowali przeciwko wielu ziemiom i przeciwko wielkim królestwom o wojnie, o nieszczęściu i o zarazie.
9 Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”
Ten prorok, który prorokuje o pokoju, [dopiero] będzie uznany za proroka, którego PAN posłał, gdy spełni się jego słowo.
10 Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola,
Wtedy prorok Chananiasz zdjął jarzmo z szyi proroka Jeremiasza i złamał je.
11 ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.
I Chananiasz powiedział wobec całego ludu: Tak mówi PAN: Tak złamię jarzmo Nabuchodonozora, króla Babilonu, znad szyi wszystkich narodów w ciągu dwóch lat. I prorok Jeremiasz poszedł swoją drogą.
12 Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti,
Po jakimś czasie od złamania jarzma na szyi proroka Jeremiasza przez proroka Chananiasza doszło do Jeremiasza słowo PANA mówiące:
13 “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo.
Idź i powiedz Chananiaszowi: Tak mówi PAN: Złamałeś jarzma drewniane, ale sporządzisz zamiast nich jarzma żelazne.
14 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’”
Tak bowiem mówi PAN zastępów, Bóg Izraela: Włożę jarzmo żelazne na szyję wszystkich tych narodów, aby służyły Nabuchodonozorowi, królowi Babilonu; i będą mu służyły. Poddałem mu nawet zwierzęta polne.
15 Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza.
Potem prorok Jeremiasz powiedział do proroka Chananiasza: Posłuchaj teraz, Chananiaszu! PAN cię nie posłał, a sprawiasz, że ludzie ufają kłamstwu.
16 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’”
Dlatego tak mówi PAN: Oto usunę cię z powierzchni ziemi. Umrzesz w tym roku, bo głosiłeś bunt przeciwko PANU.
17 Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.
I umarł prorok Chananiasz w tym roku, w miesiącu siódmym.