< Yeremiya 25 >
1 Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni.
猶大王約史雅的兒子約雅金執政第四年, 巴比倫王拿步高元年,有關於全猶大人民的話,傳給耶肋米亞;
2 Choncho mneneri Yeremiya anawuza anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi onse amene amakhala mu Yerusalemu kuti:
耶肋米亞先知便將這話轉告給全猶大人民,和耶路撒冷所有的居民說:「
3 Kwa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda mpaka lero lino, Yehova wakhala akundipatsa mauthenga ake ndipo ine ndakhala ndikuyankhula ndi inu kawirikawiri, koma inu simunamvere.
自猶大王阿孟的兒子約史雅執政第十三魁,直到今日,已經二十三年,凡上主傳給我的話,我都急速告訴了你們,你們卻不聽。
4 Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu.
上主不斷給你們派來他所有的僕人──先知們,你們總是不聽,不願傾耳諦聽。
5 Aneneriwo ankanena kuti, “Ngati aliyense wa inu abwerere, kusiya njira zake zoyipa ndi machitidwe ake oyipa, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko limene Yehova anapereka kwa makolo anu kwamuyaya.
他們說:你們應各自離棄自己的邪道,和自己的邪惡的行為,好能住在上主從永遠到永遠賜給了你們和你們祖先的地域裏;
6 Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.
不要追隨其他的神祇,事奉朝拜,以你們手做的東西來激怒我,你們就不致遭遇災禍。
7 “Koma inu simunandimvere,” akutero Yehova, “ndipo munaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene munapanga ndi manja anu. Choncho munadziwononga nokha.”
你們沒有聽從我──上主的斷語──竟以你們手做的東西來激怒我,自招禍患。
8 Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Chifukwa simunamvere mawu anga,
為此,萬軍的上主這樣說:由於你們不聽我的話,
9 ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya.
看,我必遣人召來北方的一切種族──上主的斷語──和我的僕人巴比倫王拿步高來進攻這地方,和這地方的居民,以及四周所有的民族;我要徹底消滅,任其荒涼,永遠成為笑柄和羞辱的對象。
10 Ndidzathetsa mfuwu wachimwemwe ndi wachisangalalo, mawu a mkwati ndi mkwatibwi, phokoso la mphero ndi kuwala kwa nyale.
此外,我還要息滅他們中歡樂喜慶的歌聲,新郎和新娘的歡笑聲,磨聲和燈光。
11 Dziko lonse lidzakhala bwinja ndi chipululu, ndipo mitundu ina idzatumikira mfumu ya ku Babuloni kwa 70.
這地方要全變為淒涼野,這些民族要七十年服從巴比倫王。
12 “Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya.
但是,一滿了七十年,我必要懲罰巴比倫王和這民族的罪惡──上主的斷語──以及加色丁人的國土,使它永遠成為荒野。
13 Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa.
對這國土,我要執行我論它所說,在這書上所記載先知耶肋米亞論及萬民所預言的一切話,
14 Iwo eni adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi mafumu amphamvu. Ndidzawabwezera molingana ndi zochita zawo ndi ntchito za manja awo.”
因為強盛的民族和有力的君王,要使他們成為自己的奴隸;我必依照他的作為和他們雙手所行的事,報復他們。
15 Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma.
上主,以色列的天主這樣對我說:「你從我手中接過這杯忿怒酒去,讓我派你所到的各民族喝。
16 Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”
他們必要喝,必要在我給他們派來的刀劍前,蹣跚發狂。」
17 Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako:
我便從上主手中接過杯來,給了上主派我所到的各民族喝:使她們荒蕪淒涼,
18 Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino.
受人嘲笑詛咒,像今日一樣;
19 Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse,
給埃及王法郎和他們的臣僕王侯並全體人民;
20 ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi;
給所有的雜族,胡茲地和培肋舍特地的眾君王;給阿市刻隆、迦薩、厄刻龍和阿市多得的遺民;
21 Edomu, Mowabu ndi Amoni.
給厄東、摩阿布和阿孟子民;
22 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja;
給提洛、漆冬和海外島嶼的眾君王;
23 ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali.
給德丹、特瑪、步次和凡剃除鬢髮的人;
24 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu.
給阿剌伯和在沙漠居住的雜族的眾君王;
25 Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya;
給齊默黎、厄藍和瑪待的眾君王;
26 ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.
給北方彼此相離或遠或近的眾君王,以及地面上所有的王國喝;最後喝的,是舍沙客的君王。
27 “Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’
你應對他們說:「萬軍的上主,以色列的天主這樣說:你們要喝,喝醉,嘔吐,倒在我給你們派來的刀劍前,再不起來。
28 Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’”
假使他們不肯從你手中取過杯去喝,你就對他們說:萬軍的上主這樣說:你必須喝。
29 Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.
因為,看,我開始降罰歸我名下的城市,而你們竟想全然免罰嗎﹖你們決不能免罰,因為我要給地上所有的居民招來刀劍──萬軍上主的斷語。
30 “Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti, “‘Yehova adzabangula kumwamba; mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake. Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa, kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
你應給他們預言這一切話,對他們說:上主從高處作獅吼,從他的聖所發出他的聲音,對自己的牧場厲聲怒號,對地上所有的居民,像榨葡萄的人一樣喊叫。
31 Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi, chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse; adzaweruza mtundu wonse wa anthu ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’” akutero Yehova.
一陣喧嘩嘈雜,直至地極,因為上主與萬民有了爭訟,與一切有血肉的人,進行審判,將惡人交給刀劍──上主的斷語──
32 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Taonani! Mavuto akuti akachoka pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina; mphepo ya mkuntho ikuyambira ku malekezero a dziko.”
萬軍的上主這樣說:看,各國相繼發生災禍,由地極捲來強烈的風暴。
33 Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.
到了那一天,從地極到地極,遍是上主戮的人,沒有人哀悼、收殮、埋葬,有如地面上的糞土。
34 Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu; gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa. Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika; mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.
為人牧者,你們應哭泣哀號! 為羊群領導者,你們應在灰塵中輾轉! 因為們的日期已滿,你們要被宰割,像精選的公羊。
35 Abusa adzasowa kothawira, atsogoleri a nkhosa adzasowa malo opulumukira.
為人牧者,無路可逃;為羊群領導者,無法脫身。
36 Imvani kulira kwa abusa, atsogoleri a nkhosa akulira, chifukwa Yehova akuwononga msipu wawo.
聽啊! 為人牧者在哀號,為羊群領導者在哭泣,因為上主摧毀了他們的牧場。
37 Makola awo a nkhosa amene anali pamtendere adzasanduka bwinja chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
寧靜的草場,因上主的怒燄,已成一片荒涼。
38 Ngati mkango, Yehova wasiya phanga lake, pakuti dziko lawo lasanduka chipululu chifukwa cha nkhondo ya owazunza ndiponso chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
獅子離棄了自己的巢穴,因為他們的土地,由於刀劍的無情和上主的盛怒,已成了荒野。