< Yeremiya 24 >

1 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova.
The Lord showed me in vision two baskets of figs placed in front of the Lord's Temple. This happened after Nebuchadnezzar, king of Babylon, had taken to Babylon Jehoiachin, son of Jehoiakim, king of Judah, as well as the leaders of Judah, and the craftsmen and metal-workers from Jerusalem.
2 Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.
One basket was full of very good figs, like those that ripen early, but the other basket only had very bad figs, so bad they couldn't be eaten.
3 Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”
“Jeremiah,” the Lord asked, “what can you see?” “I see figs!” I replied. “The good figs look very good, but the bad figs look very bad, so bad they can't be eaten.”
4 Tsono Yehova anandiwuza kuti,
Then a message from the Lord came to me, saying,
5 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi.
This is what the Lord, the God of Israel, says: The good figs represent to me the exiles from Judah, those I have sent away from here to the country of Babylonia.
6 Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula.
I will watch over them and I will bring them back to this country. I will build them up and not tear them down; I will plant them and not uproot them.
7 Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.
I will give them the desire to know me, to know that I am the Lord. They will be my people, and I will be their God, for they will come back completely committed to me.
8 “‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto.
But the bad figs, so bad they cannot be eaten, says the Lord, represent the way I will deal with Zedekiah, king of Judah, his officials, and those who are left of Jerusalem, as well as those remaining in this country and those living in Egypt.
9 Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira.
I'm going to make an example of them that will horrify and offend everyone on earth. They will be disgraced, mocked, ridiculed, and cursed everywhere I've exiled them.
10 Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’”
I'm going to attack them with war and famine and plague, until they're completely wiped out from the country that I gave to them and their forefathers.

< Yeremiya 24 >