< Yeremiya 22 >
1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti,
2 ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi.
3 Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.
4 Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo.
5 Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’”
6 Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi: “Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine, ngati msonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, ngati mizinda yopanda anthu.
7 Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge, munthu aliyense ali ndi zida zake, ndipo adzadula mikungudza yako yokongola nadzayiponya pa moto.
8 “Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’
9 Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’”
10 Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo; mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo, chifukwa sadzabwereranso kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
11 Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso.
12 Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”
13 “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake zosanja monyenga, pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata, osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
14 Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’ Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
15 “Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri zingachititse iwe kukhala mfumu? Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa. Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera, ndipo zonse zinkawayendera bwino.
16 Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?” akutero Yehova.
17 “Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
18 Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
19 Adzayikidwa ngati bulu, kuchita kumuguguza ndi kukamutaya kunja kwa zipata za Yerusalemu.”
20 “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko, mawu anu akamveke mpaka ku Basani. Mulire mofuwula muli ku Abarimu chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
21 Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere. Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’ Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono. Simunandimvere Ine.
22 Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo. Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
23 Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni, amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!
24 “Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya.
25 Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake.
26 Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko.
27 Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”
28 Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka imene anthu sakuyifunanso? Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake, achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
29 Iwe dziko, dziko, dziko, Imva mawu a Yehova!
30 Yehova akuti, “Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino. Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide ndi kulamulira Yuda.”