< Yeremiya 2 >
1 Yehova anandiwuza kuti,
Et factum est verbum Domini ad me, dicens:
2 “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti, “‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako, mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi, mmene unkanditsata mʼchipululu muja; mʼdziko losadzalamo kanthu.
Vade, et clama in auribus Jerusalem, dicens: Hæc dicit Dominus: Recordatus sum tui, miserans adolescentiam tuam, et caritatem desponsationis tuæ, quando secuta es me in deserto, in terra quæ non seminatur.
3 Israeli anali wopatulika wa Yehova, anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola; onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa ndipo mavuto anawagwera,’” akutero Yehova.
Sanctus Israël Domino, primitiæ frugum ejus: omnes qui devorant eum delinquunt: mala venient super eos, dicit Dominus.
4 Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo, inu mafuko onse a Israeli.
Audite verbum Domini, domus Jacob, et omnes cognationes domus Israël.
5 Yehova akuti, “Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji, kuti andithawe? Iwo anatsata milungu yachabechabe, nawonso nʼkusanduka achabechabe.
Hæc dicit Dominus: Quid invenerunt patres vestri in me iniquitatis, quia elongaverunt a me, et ambulaverunt post vanitatem, et vani facti sunt?
6 Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti, amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma ndi lokumbikakumbika, mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima, dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
Et non dixerunt: Ubi est Dominus qui ascendere nos fecit de terra Ægypti; qui traduxit nos per desertum, per terram inhabitabilem et inviam, per terram sitis, et imaginem mortis, per terram in qua non ambulavit vir, neque habitavit homo?
7 Ndinakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.
Et induxi vos in terram Carmeli, ut comederetis fructum ejus et optima illius: et ingressi contaminastis terram meam, et hæreditatem meam posuistis in abominationem.
8 Ansembe nawonso sanafunse kuti, ‘Yehova ali kuti?’ Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe; atsogoleri anandiwukira. Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala, ndi kutsatira mafano achabechabe.
Sacerdotes non dixerunt: Ubi est Dominus? et tenentes legem nescierunt me, et pastores prævaricati sunt in me, et prophetæ prophetaverunt in Baal, et idola secuti sunt.
9 “Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
Propterea adhuc judicio contendam vobiscum, ait Dominus, et cum filiis vestris disceptabo.
10 Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone, tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino; ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:
Transite ad insulas Cethim, et videte: et in Cedar mittite, et considerate vehementer: et videte si factum est hujuscemodi:
11 Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake? (Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe). Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero ndi mafano achabechabe.
si mutavit gens deos suos, et certe ipsi non sunt dii: populus vero meus mutavit gloriam suam in idolum.
12 Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi, ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,” akutero Yehova.
Obstupescite, cæli, super hoc, et portæ ejus, desolamini vehementer, dicit Dominus.
13 “Popeza anthu anga achita machimo awiri: Andisiya Ine kasupe wa madzi a moyo, ndi kukadzikumbira zitsime zawo, zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.
Duo enim mala fecit populus meus: me dereliquerunt fontem aquæ vivæ, et foderunt sibi cisternas, cisternas dissipatas, quia continere non valent aquas.
14 Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi. Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?
Numquid servus est Israël, aut vernaculus? quare ergo factus est in prædam?
15 Adani ake abangulira ndi kumuopseza ngati mikango. Dziko lake analisandutsa bwinja; mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
Super eum rugierunt leones, et dederunt vocem suam: posuerunt terram ejus in solitudinem. Civitates ejus exustæ sunt, et non est qui habitet in eis.
16 Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu.
Filii quoque Mempheos et Taphnes constupraverunt te usque ad verticem.
17 Zimenezitu zakuchitikirani chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
Numquid non istud factum est tibi, quia dereliquisti Dominum Deum tuum eo tempore quo ducebat te per viam?
18 Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto, kukamwa madzi a mu Sihori? Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya, kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
Et nunc quid tibi vis in via Ægypti, ut bibas aquam turbidam? et quid tibi cum via Assyriorum, ut bibas aquam fluminis?
19 Kuyipa kwanuko kudzakulangani; kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani. Tsono ganizirani bwino, popeza ndi chinthu choyipa kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu; ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu. Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
Arguet te malitia tua, et aversio tua increpabit te. Scito et vide quia malum et amarum est reliquisse te Dominum Deum tuum, et non esse timorem mei apud te, dicit Dominus Deus exercituum.
20 “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu ndi kudula msinga zanu; munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere. Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
A sæculo confregisti jugum meum: rupisti vincula mea, et dixisti: Non serviam. In omni enim colle sublimi, et sub omni ligno frondoso, tu prosternebaris meretrix.
21 Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika; unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika. Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa wachabechabe wonga wa kutchire?
Ego autem plantavi te vineam electam, omne semen verum: quomodo ergo conversa es mihi in pravum, vinea aliena?
22 Ngakhale utasamba ndi soda kapena kusambira sopo wambiri, kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,” akutero Ambuye Yehova.
Si laveris te nitro, et multiplicaveris tibi herbam borith, maculata es in iniquitate tua coram me, dicit Dominus Deus.
23 “Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse; sindinatsatire Abaala’? Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja; zindikira bwino zomwe wachita. Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro yomangothamanga uku ndi uku,
Quomodo dicis: Non sum polluta; post Baalim non ambulavi? Vide vias tuas in convalle; scito quid feceris: cursor levis explicans vias suas.
24 wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu, yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika. Ndani angayiretse chilakolako chakecho? Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika. Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.
Onager assuetus in solitudine, in desiderio animæ suæ attraxit ventum amoris sui: nullus avertet eam: omnes qui quærunt eam non deficient: in menstruis ejus invenient eam.
25 Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu. Koma unati, ‘Zamkutu! Ine ndimakonda milungu yachilendo, ndipo ndidzayitsatira.’
Prohibe pedem tuum a nuditate, et guttur tuum a siti. Et dixisti: Desperavi: nequaquam faciam: adamavi quippe alienos, et post eos ambulabo.
26 “Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa, moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi; Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo, ansembe ndi aneneri awo.
Quomodo confunditur fur quando deprehenditur, sic confusi sunt domus Israël, ipsi et reges eorum, principes, et sacerdotes, et prophetæ eorum,
27 Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’
dicentes ligno: Pater meus es tu: et lapidi: Tu me genuisti. Verterunt ad me tergum et non faciem, et in tempore afflictionis suæ dicent: Surge, et libera nos.
28 Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha? Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani pamene muli pamavuto! Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.
Ubi sunt dii tui quos fecisti tibi? surgant, et liberent te in tempore afflictionis tuæ: secundum numerum quippe civitatum tuarum erant dii tui, Juda.
29 “Kodi mukundizengeranji mlandu? Nonse mwandiwukira,” akutero Yehova.
Quid vultis mecum judicio contendere? omnes dereliquistis me, dicit Dominus.
30 “Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu; iwo sanaphunzirepo kanthu. Monga mkango wolusa, lupanga lanu lapha aneneri anu.
Frustra percussi filios vestros: disciplinam non receperunt. Devoravit gladius vester prophetas vestros: quasi leo vastator
31 “Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova: “Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda; sitidzabweranso kwa Inu’?
generatio vestra. Videte verbum Domini: numquid solitudo factus sum Israëli, aut terra serotina? quare ergo dixit populus meus: Recessimus; non veniemus ultra ad te?
32 Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake, kapena kuyiwala zovala zake za ukwati? Komatu anthu anga andiyiwala masiku osawerengeka.
Numquid obliviscetur virgo ornamenti sui, aut sponsa fasciæ pectoralis suæ? populus vero meus oblitus est mei diebus innumeris.
33 Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi! Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.
Quid niteris bonam ostendere viam tuam ad quærendam dilectionem, quæ insuper et malitias tuas docuisti vias tuas,
34 Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
et in alis tuis inventus est sanguis animarum pauperum et innocentum? non in fossis inveni eos, sed in omnibus quæ supra memoravi.
35 inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa, sadzatikwiyira.’ Ndidzakuyimbani mlandu chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’
Et dixisti: Absque peccato et innocens ego sum, et propterea avertatur furor tuus a me. Ecce ego judicio contendam tecum, eo quod dixeris: Non peccavi.
36 Chifukwa chiyani mukunkabe nimusinthasintha njira zanu? Aigupto adzakukhumudwitsani monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.
Quam vilis facta es nimis, iterans vias tuas! et ab Ægypto confunderis, sicut confusa es ab Assur.
37 Mudzachokanso kumeneko manja ali kunkhongo. Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira, choncho sadzakuthandizani konse.
Nam et ab ista egredieris, et manus tuæ erunt super caput tuum: quoniam obtrivit Dominus confidentiam tuam, et nihil habebis prosperum in ea.