< Yeremiya 18 >

1 Yehova anawuza Yeremiya kuti,
ヱホバよりヱレミヤにのぞめる言いふ
2 “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.”
汝起て陶人の屋にくだれ我かしこに於てわが言を汝に聞しめんと
3 Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero.
われすなはち陶人の屋にくだり視るに轆轤をもて物をつくりをりしが
4 Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
その泥をもて造れるところの器陶人の手のうちに傷ねたれば彼その心のままに之をもて別の器をつくれり
5 Kenaka Yehova anandiwuza kuti,
時にヱホバの言我にのぞみていふ
6 “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.
ヱホバいふイスラエルの家よこの陶人のなすが如くわれ汝になすことをえざるかイスラエルの家よ陶人の手に泥のあるごとく汝らはわが手にあり
7 Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga,
われ急に民あるひは國をぬくべし敗るべし滅すべしといふことあらんに
8 ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira.
もし我いひしところの國その惡を離れなば我之に災を降さんとおもひしことを悔ん
9 Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu.
我また急に民あるいは國を立べし植べしといふことあらんに
10 Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.
もし其國わが目に惡く見ゆるところの事を行ひわが聲に遵はずば我これに福祉を錫へんといひしことを悔ん
11 “Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’
汝いまユダの人々とヱルサレムに住る者にいへヱホバかくいへり視よ我汝らに災をくださんと思ひめぐらし汝らをはかる計策を設く故に汝らおのおの其惡き途を離れ其途と行をあらためよと
12 Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’”
しかるに彼らいふ是は徒然なりわれらは自己の圖維ところにしたがひ各自その惡き心の剛愎なるを行はんと
13 Yehova akuti, “Uwafunse anthu a mitundu ina kuti: Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi? Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita chinthu choopsa kwambiri.
この故にヱホバかくいひたまふ汝ら異國のうちに問へ斯の如きことを聞し者ありやイスラエルの處女はいと驚くべきことをなせり
14 Kodi chisanu chimatha pa matanthwe otsetsereka a phiri la Lebanoni? Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera ku phiri la Lebanoni adzamphwa?
レバノンの雪豈野の磐を離れんや遠方より流くる冷なる水豈涸かんや
15 Komatu anthu anga andiyiwala; akufukiza lubani kwa mafano achabechabe. Amapunthwa mʼnjira zawo zakale. Amayenda mʼnjira zachidule ndi kusiya njira zabwino.
しかるに我民は我をわすれて虛き物に香を焚り是等の物彼らをその途すなはち古き途に蹶かせまた徑すなはち備なき道に行しめ
16 Dziko lawo amalisandutsa chipululu, chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse; onse odutsapo adzadabwa kwambiri ndipo adzapukusa mitu yawo.
その地を荒して恒に人の笑とならしめん凡て其處を過る者は驚きてその首を搖らん
17 Ngati mphepo yochokera kummawa, ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo; ndidzawafulatira osawathandiza pa tsiku la mavuto awo.”
われ東風のごとくに彼らをその敵の前に散さん其滅亡の日にはわれ背を彼らに向て面をむけじ
18 Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”
彼らいふ去來われら計策を設てヱレミヤをはからんそれ祭司には律法あり智慧ある者には謀畧あり預言者には言ありて失ざるべし去來われら舌をもて彼を撃ちその諸の言を聽ことをせざらんと
19 Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni; imvani zimene adani anga akunena za ine!
ヱホバよ我にききたまへ又我と爭ふ者の聲をききたまへ
20 Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino? Komabe iwo andikumbira dzenje. Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu kudzawapempherera kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
惡をもて善に報ゆべきものならんや彼らはわが生命をとらん爲に坑を掘れりわが汝の前に立て彼らを善く言ひ汝の憤怒を止めんとせしを憶えたまへ
21 Choncho langani ana awo ndi njala; aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga. Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye; amuna awo aphedwe ndi mliri, anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
さればかれらの子女を饑饉にあたへ彼らを劍の刃にわたしたまへ其妻は子を失ひ且寡となり其男は死をもて亡されその少者は劍をもて戰に殺されよかし
22 Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe. Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo ndipo atchera msampha mapazi anga.
汝突然に敵をかれらに臨ませたまふ時號呼をその家の内より聞えしめよそは彼ら坑を掘りて我を執へんとしまた機檻を置てわが足を執へんとすればなり
23 Koma Inu Yehova, mukudziwa ziwembu zawo zonse zofuna kundipha. Musawakhululukire zolakwa zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu. Agonjetsedwe pamaso panu; muwalange muli wokwiya.”
ヱホバよ汝はかれらが我を殺さんとするすべての謀畧を知りたまふ其惡を赦すことなく其罪を汝の前より抹去りたまふなかれ彼らを汝の前に仆れしめよ汝の怒りたまふ時にかく彼らになしたまへ

< Yeremiya 18 >