< Yeremiya 17 >
1 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo, lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yawo ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
2 Ngakhale ana awo amakumbukira maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera, pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri, pa mapiri aatali mʼdzikomo.
3 Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense ndidzazipereka kwa ofunkha kuti zikhale dipo lawo chifukwa cha machimo ochitika mʼdziko lonse.
4 Mudzataya dziko limene ndinakupatsani kuti likhale cholowa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu mʼdziko limene inu simukulidziwa, chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto, ndipo udzayaka mpaka muyaya.”
5 Yehova akuti, “Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake, amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize pamene mtima wake wafulatira Yehova.
6 Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu; iye sadzapeza zabwino. Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi, mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.
7 “Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova, amene amatsamira pa Iye.
8 Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
9 Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika. Ndani angathe kuwumvetsa?
10 “Ine Yehova ndimafufuza mtima ndi kuyesa maganizo, ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenera ntchito zake.”
11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire. Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera, ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
12 Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.
13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli, onse amene amakusiyani adzachita manyazi. Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi chifukwa anakana Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
14 Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira; pulumutseni ndipo ndidzapulumuka, chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
15 Anthu akumandinena kuti, “Mawu a Yehova ali kuti? Zichitiketu lero kuti tizione!”
16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange. Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka. Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
17 Musandichititse mantha; ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.
18 Ondizunza anga achite manyazi, koma musandichititse manyazi; iwo achite mantha kwambiri, koma ine mundichotsere manthawo. Tsiku la mavuto liwafikire; ndipo muwawononge kotheratu.
19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu.
20 Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’
21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu.
22 Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu.
23 Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga.
24 Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli.
25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya.
26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova.
27 Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’”