< Yeremiya 15 >

1 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite!
耶和华对我说:“虽有摩西和撒母耳站在我面前代求,我的心也不顾惜这百姓。你将他们从我眼前赶出,叫他们去吧!
2 Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti, “‘Oyenera kufa adzafa; oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga; oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala; oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
他们问你说:‘我们往哪里去呢?’你便告诉他们,耶和华如此说: 定为死亡的,必致死亡; 定为刀杀的,必交刀杀; 定为饥荒的,必遭饥荒; 定为掳掠的,必被掳掠。”
3 “Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.
耶和华说:“我命定四样害他们,就是刀剑杀戮、狗类撕裂、空中的飞鸟,和地上的野兽吞吃毁灭;
4 Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
又必使他们在天下万国中抛来抛去,都因犹大王希西家的儿子玛拿西在耶路撒冷所行的事。”
5 “Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu? Kodi adzakulira ndani? Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
耶路撒冷啊,谁可怜你呢? 谁为你悲伤呢? 谁转身问你的安呢?
6 Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova. “Inu mukubwererabe mʼmbuyo. Choncho Ine ndidzakukanthani. Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
耶和华说:你弃绝了我, 转身退后; 因此我伸手攻击你,毁坏你。 我后悔甚不耐烦。
7 Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
我在境内各城门口, 用簸箕簸了我的百姓, 使他们丧掉儿女。 我毁灭他们, 他们仍不转离所行的道。
8 Ndinachulukitsa amayi awo amasiye kupambana mchenga wa kunyanja. Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna dzuwa lili pamutu. Mwadzidzidzi ndinawagwetsera kuwawa mtima ndi mantha.
他们的寡妇在我面前比海沙更多; 我使灭命的午间来, 攻击少年人的母亲, 使痛苦惊吓忽然临到她身上。
9 Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka ndipo akupuma wefuwefu. Dzuwa lake lalowa ukanali usana; anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru. Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,” akutero Yehova.
生过七子的妇人力衰气绝; 尚在白昼,日头忽落; 她抱愧蒙羞。 其余的人, 我必在他们敌人跟前,交与刀剑。 这是耶和华说的。
10 Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine, munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse! Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu, komatu aliyense akunditemberera.
我的母亲哪,我有祸了!因你生我作为遍地相争相竞的人。我素来没有借贷与人,人也没有借贷与我,人人却都咒骂我。
11 Yehova anati, “Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino. Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka ndi ya mavuto awo.
耶和华说:“我必要坚固你,使你得好处。灾祸苦难临到的时候,我必要使仇敌央求你。(
12 “Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo, makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.
人岂能将铜与铁,就是北方的铁折断呢?)
13 Anthu ako ndi chuma chako ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu onse a mʼdziko lanu lonse.
“我必因你在四境之内所犯的一切罪,把你的货物财宝当掠物,白白地交给仇敌。
14 Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu mʼdziko limene inu simulidziwa, chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto umene udzakutenthani.”
我也必使仇敌带这掠物到你所不认识的地去,因我怒中起的火要将你们焚烧。”
15 Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse; kumbukireni ndi kundisamalira. Ndilipsireni anthu ondizunza. Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga. Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
耶和华啊,你是知道的; 求你记念我,眷顾我, 向逼迫我的人为我报仇; 不要向他们忍怒取我的命, 要知道我为你的缘故受了凌辱。
16 Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.
耶和华—万军之 神啊, 我得着你的言语就当食物吃了; 你的言语是我心中的欢喜快乐, 因我是称为你名下的人。
17 Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera, sindinasangalale nawo anthu amenewo. Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.
我没有坐在宴乐人的会中, 也没有欢乐; 我因你的感动独自静坐, 因你使我满心愤恨。
18 Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Bwanji chilonda changa sichikupola? Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe, kapena ngati kasupe wopanda madzi?”
我的痛苦为何长久不止呢? 我的伤痕为何无法医治、不能痊愈呢? 难道你待我有诡诈,像流干的河道吗?
19 Tsono Yehova anandiyankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso ndipo udzakhalanso mtumiki wanga. Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe, udzakhalanso mneneri wanga. Anthu adzabwera kwa iwe ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
耶和华如此说:你若归回, 我就将你再带来, 使你站在我面前; 你若将宝贵的和下贱的分别出来, 你就可以当作我的口。 他们必归向你, 你却不可归向他们。
20 Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba ngati mkuwa kwa anthu awa. Adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, pakuti Ine ndili nawe kukulanditsa ndi kukupulumutsa,” akutero Yehova.
我必使你向这百姓成为坚固的铜墙; 他们必攻击你,却不能胜你; 因我与你同在,要拯救你,搭救你。 这是耶和华说的。
21 “Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”
我必搭救你脱离恶人的手, 救赎你脱离强暴人的手。

< Yeremiya 15 >