< Yeremiya 13 >

1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.”
כה אמר יהוה אלי הלוך וקנית לך אזור פשתים ושמתו על מתניך ובמים לא תבאהו׃
2 Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
ואקנה את האזור כדבר יהוה ואשם על מתני׃
3 Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti,
ויהי דבר יהוה אלי שנית לאמר׃
4 “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.”
קח את האזור אשר קנית אשר על מתניך וקום לך פרתה וטמנהו שם בנקיק הסלע׃
5 Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
ואלך ואטמנהו בפרת כאשר צוה יהוה אותי׃
6 Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.”
ויהי מקץ ימים רבים ויאמר יהוה אלי קום לך פרתה וקח משם את האזור אשר צויתיך לטמנו שם׃
7 Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
ואלך פרתה ואחפר ואקח את האזור מן המקום אשר טמנתיו שמה והנה נשחת האזור לא יצלח לכל׃
8 Pamenepo Yehova anandiwuza kuti,
ויהי דבר יהוה אלי לאמר׃
9 “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
כה אמר יהוה ככה אשחית את גאון יהודה ואת גאון ירושלם הרב׃
10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.
העם הזה הרע המאנים לשמוע את דברי ההלכים בשררות לבם וילכו אחרי אלהים אחרים לעבדם ולהשתחות להם ויהי כאזור הזה אשר לא יצלח לכל׃
11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
כי כאשר ידבק האזור אל מתני איש כן הדבקתי אלי את כל בית ישראל ואת כל בית יהודה נאם יהוה להיות לי לעם ולשם ולתהלה ולתפארת ולא שמעו׃
12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’
ואמרת אליהם את הדבר הזה כה אמר יהוה אלהי ישראל כל נבל ימלא יין ואמרו אליך הידע לא נדע כי כל נבל ימלא יין׃
13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu.
ואמרת אליהם כה אמר יהוה הנני ממלא את כל ישבי הארץ הזאת ואת המלכים הישבים לדוד על כסאו ואת הכהנים ואת הנביאים ואת כל ישבי ירושלם שכרון׃
14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’”
ונפצתים איש אל אחיו והאבות והבנים יחדו נאם יהוה לא אחמול ולא אחוס ולא ארחם מהשחיתם׃
15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu, musadzitukumule, pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
שמעו והאזינו אל תגבהו כי יהוה דבר׃
16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu asanagwetse mdima, mapazi anu asanayambe kupunthwa mʼchisisira chamʼmapiri. Asanasandutse kuwala mukuyembekezerako kukhala mdima wandiweyani.
תנו ליהוה אלהיכם כבוד בטרם יחשך ובטרם יתנגפו רגליכם על הרי נשף וקויתם לאור ושמה לצלמות ישית לערפל׃
17 Koma ngati simumvera, ndidzalira kwambiri chifukwa cha kunyada kwanu. Mʼmaso mwanga mwadzaza ndi misozi yowawa chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
ואם לא תשמעוה במסתרים תבכה נפשי מפני גוה ודמע תדמע ותרד עיני דמעה כי נשבה עדר יהוה׃
18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumuyo, pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo zagwa pansi.”
אמר למלך ולגבירה השפילו שבו כי ירד מראשותיכם עטרת תפארתכם׃
19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo, watengedwa yense ukapolo.
ערי הנגב סגרו ואין פתח הגלת יהודה כלה הגלת שלומים׃
20 Tukula maso ako kuti uwone amene akubwera kuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija?
שאי עיניכם וראי הבאים מצפון איה העדר נתן לך צאן תפארתך׃
21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira? Kodi sudzamva zowawa ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
מה תאמרי כי יפקד עליך ואת למדת אתם עליך אלפים לראש הלוא חבלים יאחזוך כמו אשת לדה׃
22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti, “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?” Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zingʼambike ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
וכי תאמרי בלבבך מדוע קראני אלה ברב עונך נגלו שוליך נחמסו עקביך׃
23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake, kapena kambuku kusintha mawanga ake? Inunso amene munazolowera kuchita zoyipa simungathe kusintha.
היהפך כושי עורו ונמר חברברתיו גם אתם תוכלו להיטיב למדי הרע׃
24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
ואפיצם כקש עובר לרוח מדבר׃
25 Limeneli ndiye gawo lanu, chilango chimene ndakukonzerani chifukwa chondiyiwala Ine ndi kutumikira milungu yabodza, akutero Yehova.
זה גורלך מנת מדיך מאתי נאם יהוה אשר שכחת אותי ותבטחי בשקר׃
26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso kuti umaliseche wanu uwonekere.
וגם אני חשפתי שוליך על פניך ונראה קלונך׃
27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu ndi ziwerewere zanu, zochitika pa mapiri ndi mʼminda. Tsoka iwe Yerusalemu! Udzakhala wosayeretsedwa pa zachipembedzo mpaka liti?”
נאפיך ומצהלותיך זמת זנותך על גבעות בשדה ראיתי שקוציך אוי לך ירושלם לא תטהרי אחרי מתי עד׃

< Yeremiya 13 >