< Yeremiya 12 >
1 Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse ndikati nditsutsane nanu. Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
Lord, when I complain to you, you always show yourself to be in the right. Even so I still want to present my case to you. Why is it that wicked people do so well? Why do those who are unfaithful to you live so comfortably?
2 Inu munawadzala ndipo anamera mizu; amakula ndi kubereka zipatso. Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse, koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
You planted them, and they've taken root, grown, and produced fruit. They're always talking about you but they don't think of you, even for a moment.
3 Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa; mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga. Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa! Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
But you know me, Lord, you see me, and examine what I think about you. Drag off these people like sheep to be slaughtered; keep them apart for the time when they're killed.
4 Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti? Nyama ndi mbalame kulibiretu chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa. Iwo amati: “Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
How long will the land have to mourn and the grass in every field be dried up because of the evil of the people who live there? The animals and birds have died out because the people have said, “He doesn't know what's going to happen to us.”
5 Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo? Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino, udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango za ku Yorodani?
The Lord says, Once you've become worn out in a foot race against men, how would you win racing against horses? If you trip up in open ground, how would you do in the tangled undergrowth beside the Jordan?
6 Ngakhale abale ako ndi anansi akuwukira, onsewo amvana zokuyimba mlandu. Usawakhulupirire, ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.
Even your own brothers and your father's family have betrayed you; they have publicly criticized you. Don't trust them when they talk nicely to you!
7 “Ine ndawasiya anthu anga; anthu amene ndinawasankha ndawataya. Ndapereka okondedwa anga mʼmanja mwa adani awo.
I have given up on my people; I have abandoned the nation I chose. I have handed over the ones I truly love to their enemies.
8 Anthu amene ndinawasankha asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango. Akundibangulira mwaukali; nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
They've turned into a wild lion, roaring at me—that's why I hate them.
9 Anthu anga amene ndinawasankha asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga imene akabawi ayizinga. Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo. Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
My people are like a spotted bird of prey to me with other birds of prey circling to attack it. Go and bring all the wild animals to eat up the carcass.
10 Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa, anapondereza munda wanga; munda wanga wabwino uja anawusandutsa chipululu.
Many shepherds have come and destroyed my vineyard; they have trampled down the crops in my field. They have turned my pleasant land into an empty wasteland.
11 Unawusandutsadi chipululu. Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine. Dziko lonse lasanduka chipululu chifukwa palibe wolisamalira.
They have made it into a desert; it mourns before me, lying desolate. The whole country is a wasteland, but no one cares.
12 Anthu onse owononga abalalikira ku zitunda zonse za mʼchipululu. Yehova watuma ankhondo ake kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko, ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
The destructive armies have crossed all the bare desert hills for the Lord's sword destroys from one end of the country to the other. No one has any peace.
13 Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga; anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse. Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
My people sowed wheat but harvested thorns. They wore themselves out but gained no benefit. You should be ashamed of such a poor harvest, caused by the Lord's furious anger.
14 “Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo.
This is what the Lord says: When it comes these evil nearby nations who attack the country that I gave to my people Israel, I'm going to uproot them from their land. I'm also going to uproot the people of Judah from among them.
15 Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake.
However, once I have uprooted them, I will have mercy on them again, and bring each one back to their property and their land.
16 Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga.
If they will honestly learn the ways of my people and respect me, making their vows to me, just as they once taught my people to swear by Baal, then they will do well among my people.
17 Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.
But if they refuse to obey, then I will not only uproot that nation but I will completely destroy it, declares the Lord.