< Yeremiya 10 >
1 Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena.
2 Yehova akuti, “Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
3 Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe. Iwo amakadula mtengo ku nkhalango ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
4 Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke.
5 Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka. Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe ndipo ayenera kunyamulidwa popeza sangathe nʼkuyenda komwe. Musachite nawo mantha popeza sangathe kukuchitani choyipa ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
6 Palibe wofanana nanu, Inu Yehova; Inu ndinu wamkulu, ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
7 Ndani amene angaleke kukuopani, inu Mfumu ya mitundu ya anthu? Chimenechi ndicho chokuyenerani. Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse a mitundu ya anthu, palibe wina wofanana nanu.
8 Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru; malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
9 Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi ndipo golide amachokera naye ku Ufazi. Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide. Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo. Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
10 Koma Yehova ndiye Mulungu woona; Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya. Akakwiya, dziko limagwedezeka; anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.
11 “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’”
12 Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.
13 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba; Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.
14 Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo.
15 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
16 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
17 Sonkhanitsani katundu wanu, inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
18 Pakuti Yehova akuti, “Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse amene akukhala mʼdziko lino; adzakhala pa mavuto mpaka adzamvetsa.”
19 Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga! Chilonda changa nʼchachikulu!” Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi, choncho ndingolipirira.”
20 Tenti yanga yawonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso amene adzandimangire tenti, kapena kufunyulula nsalu yake.
21 Abusa ndi opusa ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova; choncho palibe chimene anapindula ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
22 Tamvani! kukubwera mphekesera, phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto! Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda, malo okhala nkhandwe.
23 Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake; munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
24 Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo, osati ndi mkwiyo wanu, mungandiwononge kotheratu.
25 Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani, ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba. Iwo aja anasakaza Yakobo; amusakaza kotheratu ndipo awononga dziko lake.