< Yakobo 4 >
1 Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu?
Ni kitu gani kinachosababisha mapigano na ugomvi miongoni mwenu? Je, haya hayatokani na tamaa zenu zinazoshindana ndani yenu?
2 Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Mnatamani lakini hampati, kwa hiyo mwaua. Mwatamani kupata lakini hampati vile mnavyotaka, kwa hiyo mnajitia katika magomvi na mapigano. Mmepungukiwa kwa sababu hammwombi Mungu.
3 Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.
Mnapoomba hampati kwa sababu mnaomba kwa nia mbaya, ili mpate kuvitumia hivyo mtakavyopata kwa tamaa zenu.
4 Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.
Ninyi wanaume na wanawake wazinzi, hamjui ya kwamba urafiki na dunia ni uadui na Mungu? Kwa hiyo mtu yeyote anayetaka kuwa rafiki wa dunia hufanyika adui wa Mungu.
5 Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife?
Au mwadhani kwamba Andiko lasema bure kuwa huyo Roho ambaye Mungu amemweka ndani yetu hututamani kiasi cha kuona wivu?
6 Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”
Lakini yeye hutupatia neema zaidi. Hii ndiyo sababu Andiko husema: “Mungu huwapinga wenye kiburi, lakini huwapa wanyenyekevu neema.”
7 Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani.
Basi mtiini Mungu. Mpingeni ibilisi, naye atawakimbia.
8 Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira.
Mkaribieni Mungu, naye atawakaribia ninyi. Itakaseni mikono yenu ninyi wenye dhambi, na kuisafisha mioyo yenu ninyi wenye nia mbili.
9 Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni.
Huzunikeni, ombolezeni na kulia. Kicheko chenu na kigeuzwe kuwa kuomboleza, na furaha yenu kuwa huzuni.
10 Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
Jinyenyekezeni mbele za Bwana, naye atawainua.
11 Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza.
Ndugu, msineneane mabaya ninyi kwa ninyi. Mtu yeyote anayesema mabaya dhidi ya ndugu yake au kumhukumu anasema dhidi ya sheria na kuihukumu. Unapoihukumu sheria, basi huishiki sheria bali umekuwa hakimu wa kuihukumu hiyo sheria.
12 Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
Yuko Mtoa sheria mmoja tu na yeye peke yake ndiye Hakimu, ndiye awezaye kuokoa au kuangamiza. Lakini wewe ni nani hata umhukumu jirani yako?
13 Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.”
Basi sikilizeni ninyi msemao, “Leo au kesho tutakwenda katika mji huu ama ule tukae humo mwaka mmoja, tufanye biashara na kupata faida.”
14 Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira.
Lakini hamjui hata litakalotukia kesho. Maisha yenu ni nini? Ninyi ni ukungu ambao huonekana kwa kitambo kidogo kisha hutoweka.
15 Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.”
Badala yake, inawapasa kusema, “Kama Bwana akipenda, tutaishi na kufanya hili ama lile.”
16 Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa.
Kama ilivyo sasa, mnajisifu na kujigamba. Kujisifu kwa namna hiyo ni uovu.
17 Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.
Basi mtu yeyote anayejua jema limpasalo kutenda, lakini asilitende, mtu huyo anatenda dhambi.