< Yakobo 3 >

1 Abale anga, ambiri musakhale aphunzitsi chifukwa mumadziwa kuti aphunzitsife tidzaweruzidwa mowuma kuposa anthu ena onse.
Que plusieurs d'entre vous ne se fassent pas maîtres, mes frères, sachant que nous recevrons un jugement plus sévère.
2 Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.
Car nous trébuchons tous en beaucoup de choses. Celui qui ne trébuche pas en paroles est une personne parfaite, capable aussi de brider tout le corps.
3 Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse.
En effet, nous mettons des mors dans la bouche des chevaux pour qu'ils nous obéissent, et nous guidons tout leur corps.
4 Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita.
Voici que les navires aussi, bien qu'ils soient si grands et poussés par des vents violents, sont guidés par un tout petit gouvernail, là où le pilote le désire.
5 Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa.
Ainsi la langue est aussi un petit membre, et elle se vante de grandes choses. Voyez comme un petit feu peut se propager en une grande forêt!
6 Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena. (Geenna g1067)
Et la langue est un feu. Le monde de l'iniquité parmi nos membres, c'est la langue, qui souille tout le corps, qui met le feu au cours de la nature, et qui est embrasée par la géhenne. (Geenna g1067)
7 Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta,
Car toute espèce d'animaux, d'oiseaux, de reptiles et de créatures marines peut être domptée et a été domptée par l'homme;
8 koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
mais personne ne peut dompter la langue. C'est un mal sans repos, plein d'un poison mortel.
9 Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu.
Avec elle, nous bénissons notre Dieu et notre Père, et avec elle, nous maudissons les hommes faits à l'image de Dieu.
10 Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi.
De la même bouche sortent la bénédiction et la malédiction. Mes frères, il ne faut pas qu'il en soit ainsi.
11 Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi?
Une source fait-elle jaillir de la même ouverture une eau douce et une eau amère?
12 Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.
Un figuier, mes frères, peut-il produire des olives, ou une vigne des figues? Ainsi, aucune source ne produit à la fois de l'eau salée et de l'eau douce.
13 Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake
Qui est sage et intelligent parmi vous? Qu'il montre par sa bonne conduite que ses actes sont accomplis avec la douceur de la sagesse.
14 Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi.
Mais si tu as dans ton cœur une jalousie amère et une ambition égoïste, ne te vante pas et ne mens pas contre la vérité.
15 “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda.
Cette sagesse n'est pas celle qui descend d'en haut, mais elle est terrestre, sensuelle et démoniaque.
16 Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
Car là où sont la jalousie et l'ambition égoïste, il y a la confusion et toute mauvaise action.
17 Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima.
Mais la sagesse qui vient d'en haut est premièrement pure, puis paisible, douce, raisonnable, pleine de miséricorde et de bons fruits, sans partialité et sans hypocrisie.
18 Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.
Or le fruit de la justice est semé dans la paix par ceux qui font la paix.

< Yakobo 3 >