< Yesaya 1 >

1 Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
חֲזוֹן֙ יְשַֽׁעְיָ֣הוּ בֶן־אָמ֔וֹץ אֲשֶׁ֣ר חָזָ֔ה עַל־יְהוּדָ֖ה וִירוּשָׁלִָ֑ם בִּימֵ֨י עֻזִּיָּ֧הוּ יוֹתָ֛ם אָחָ֥ז יְחִזְקִיָּ֖הוּ מַלְכֵ֥י יְהוּדָֽה׃
2 Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi! Pakuti Yehova wanena kuti, “Ndinabala ana ndi kuwalera, koma anawo andiwukira Ine.
שִׁמְע֤וּ שָׁמַ֙יִם֙ וְהַאֲזִ֣ינִי אֶ֔רֶץ כִּ֥י יְהוָ֖ה דִּבֵּ֑ר בָּנִים֙ גִּדַּ֣לְתִּי וְרוֹמַ֔מְתִּי וְהֵ֖ם פָּ֥שְׁעוּ בִֽי׃
3 Ngʼombe imadziwa mwini wake, bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake, koma Israeli sadziwa, anthu anga samvetsa konse.”
יָדַ֥ע שׁוֹר֙ קֹנֵ֔הוּ וַחֲמ֖וֹר אֵב֣וּס בְּעָלָ֑יו יִשְׂרָאֵל֙ לֹ֣א יָדַ֔ע עַמִּ֖י לֹ֥א הִתְבּוֹנָֽן׃
4 Haa, mtundu wochimwa, anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoyipa, ana odzipereka ku zoyipa! Iwo asiya Yehova; anyoza Woyerayo wa Israeli ndipo afulatira Iyeyo.
ה֣וֹי ׀ גּ֣וֹי חֹטֵ֗א עַ֚ם כֶּ֣בֶד עָוֺ֔ן זֶ֣רַע מְרֵעִ֔ים בָּנִ֖ים מַשְׁחִיתִ֑ים עָזְב֣וּ אֶת־יְהוָ֗ה נִֽאֲצ֛וּ אֶת־קְד֥וֹשׁ יִשְׂרָאֵ֖ל נָזֹ֥רוּ אָחֽוֹר׃
5 Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe? Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira? Mutu wanu wonse uli ndi mabala, mtima wanu wonse wafowokeratu.
עַ֣ל מֶ֥ה תֻכּ֛וּ ע֖וֹד תּוֹסִ֣יפוּ סָרָ֑ה כָּל־רֹ֣אשׁ לָחֳלִ֔י וְכָל־לֵבָ֖ב דַּוָּֽי׃
6 Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu palibe pabwino, paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda, mabala ali magazi chuchuchu, mabala ake ngosatsuka, ngosamanga ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
מִכַּף־רֶ֤גֶל וְעַד־רֹאשׁ֙ אֵֽין־בּ֣וֹ מְתֹ֔ם פֶּ֥צַע וְחַבּוּרָ֖ה וּמַכָּ֣ה טְרִיָּ֑ה לֹא־זֹ֙רוּ֙ וְלֹ֣א חֻבָּ֔שׁוּ וְלֹ֥א רֻכְּכָ֖ה בַּשָּֽׁמֶן׃
7 Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; minda yanu ikukololedwa ndi alendo inu muli pomwepo, dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
אַרְצְכֶ֣ם שְׁמָמָ֔ה עָרֵיכֶ֖ם שְׂרֻפ֣וֹת אֵ֑שׁ אַדְמַתְכֶ֗ם לְנֶגְדְּכֶם֙ זָרִים֙ אֹכְלִ֣ים אֹתָ֔הּ וּשְׁמָמָ֖ה כְּמַהְפֵּכַ֥ת זָרִֽים׃
8 Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha ngati nsanja mʼmunda wampesa, ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka, ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
וְנוֹתְרָ֥ה בַת־צִיּ֖וֹן כְּסֻכָּ֣ה בְכָ֑רֶם כִּמְלוּנָ֥ה בְמִקְשָׁ֖ה כְּעִ֥יר נְצוּרָֽה׃
9 Yehova Wamphamvuzonse akanapanda kutisiyira opulumuka, tikanawonongeka ngati Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
לוּלֵי֙ יְהוָ֣ה צְבָא֔וֹת הוֹתִ֥יר לָ֛נוּ שָׂרִ֖יד כִּמְעָ֑ט כִּסְדֹ֣ם הָיִ֔ינוּ לַעֲמֹרָ֖ה דָּמִֽינוּ׃ ס
10 Imvani mawu a Yehova, inu olamulira Sodomu; mverani lamulo la Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora!
שִׁמְע֥וּ דְבַר־יְהוָ֖ה קְצִינֵ֣י סְדֹ֑ם הַאֲזִ֛ינוּ תּוֹרַ֥ת אֱלֹהֵ֖ינוּ עַ֥ם עֲמֹרָֽה׃
11 Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka?” “Zandikola nsembe zanu zopsereza za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa; sindikusangalatsidwanso ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
לָמָּה־לִּ֤י רֹב־זִבְחֵיכֶם֙ יֹאמַ֣ר יְהוָ֔ה שָׂבַ֛עְתִּי עֹל֥וֹת אֵילִ֖ים וְחֵ֣לֶב מְרִיאִ֑ים וְדַ֨ם פָּרִ֧ים וּכְבָשִׂ֛ים וְעַתּוּדִ֖ים לֹ֥א חָפָֽצְתִּי׃
12 Ndani anakulamulirani kuti mubwere nazo pamaso panga? Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
כִּ֣י תָבֹ֔אוּ לֵרָא֖וֹת פָּנָ֑י מִי־בִקֵּ֥שׁ זֹ֛את מִיֶּדְכֶ֖ם רְמֹ֥ס חֲצֵרָֽי׃
13 Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo! Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine. Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa, kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
לֹ֣א תוֹסִ֗יפוּ הָבִיא֙ מִנְחַת־שָׁ֔וְא קְטֹ֧רֶת תּוֹעֵבָ֛ה הִ֖יא לִ֑י חֹ֤דֶשׁ וְשַׁבָּת֙ קְרֹ֣א מִקְרָ֔א לֹא־אוּכַ֥ל אָ֖וֶן וַעֲצָרָֽה׃
14 Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera; ndatopa kuzinyamula.
חָדְשֵׁיכֶ֤ם וּמוֹעֲדֵיכֶם֙ שָׂנְאָ֣ה נַפְשִׁ֔י הָי֥וּ עָלַ֖י לָטֹ֑רַח נִלְאֵ֖יתִי נְשֹֽׂא׃
15 Mukamatambasula manja anu popemphera, Ine sindidzakuyangʼanani; ngakhale muchulukitse mapemphero anu, sindidzakumverani. Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
וּבְפָרִשְׂכֶ֣ם כַּפֵּיכֶ֗ם אַעְלִ֤ים עֵינַי֙ מִכֶּ֔ם גַּ֛ם כִּֽי־תַרְבּ֥וּ תְפִלָּ֖ה אֵינֶ֣נִּי שֹׁמֵ֑עַ יְדֵיכֶ֖ם דָּמִ֥ים מָלֵֽאוּ׃
16 sambani, dziyeretseni. Chotsani pamaso panu ntchito zanu zoyipa! Lekani kuchita zoyipa,
רַחֲצוּ֙ הִזַּכּ֔וּ הָסִ֛ירוּ רֹ֥עַ מַעַלְלֵיכֶ֖ם מִנֶּ֣גֶד עֵינָ֑י חִדְל֖וּ הָרֵֽעַ׃
17 phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
לִמְד֥וּ הֵיטֵ֛ב דִּרְשׁ֥וּ מִשְׁפָּ֖ט אַשְּׁר֣וּ חָמ֑וֹץ שִׁפְט֣וּ יָת֔וֹם רִ֖יבוּ אַלְמָנָֽה׃ ס
18 Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.
לְכוּ־נָ֛א וְנִוָּֽכְחָ֖ה יֹאמַ֣ר יְהוָ֑ה אִם־יִֽהְי֨וּ חֲטָאֵיכֶ֤ם כַּשָּׁנִים֙ כַּשֶּׁ֣לֶג יַלְבִּ֔ינוּ אִם־יַאְדִּ֥ימוּ כַתּוֹלָ֖ע כַּצֶּ֥מֶר יִהְיֽוּ׃
19 Ngati muli okonzeka kundimvera mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
אִם־תֹּאב֖וּ וּשְׁמַעְתֶּ֑ם ט֥וּב הָאָ֖רֶץ תֹּאכֵֽלוּ׃
20 koma mukakana ndi kuwukira mudzaphedwa ndi lupanga.” Pakuti Yehova wayankhula.
וְאִם־תְּמָאֲנ֖וּ וּמְרִיתֶ֑ם חֶ֣רֶב תְּאֻכְּל֔וּ כִּ֛י פִּ֥י יְהוָ֖ה דִּבֵּֽר׃ ס
21 Taonani momwe mzinda wokhulupirika wasandukira wadama! Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama; mu mzindamo munali chilungamo, koma tsopano muli anthu opha anzawo!
אֵיכָה֙ הָיְתָ֣ה לְזוֹנָ֔ה קִרְיָ֖ה נֶאֱמָנָ֑ה מְלֵאֲתִ֣י מִשְׁפָּ֗ט צֶ֛דֶק יָלִ֥ין בָּ֖הּ וְעַתָּ֥ה מְרַצְּחִֽים׃
22 Siliva wako wasanduka wachabechabe, vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
כַּסְפֵּ֖ךְ הָיָ֣ה לְסִיגִ֑ים סָבְאֵ֖ךְ מָה֥וּל בַּמָּֽיִם׃
23 Atsogoleri ako ndi owukira, anthu ogwirizana ndi mbala; onse amakonda ziphuphu ndipo amathamangira mphatso. Iwo sateteza ana amasiye; ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
שָׂרַ֣יִךְ סוֹרְרִ֗ים וְחַבְרֵי֙ גַּנָּבִ֔ים כֻּלּוֹ֙ אֹהֵ֣ב שֹׁ֔חַד וְרֹדֵ֖ף שַׁלְמֹנִ֑ים יָתוֹם֙ לֹ֣א יִשְׁפֹּ֔טוּ וְרִ֥יב אַלְמָנָ֖ה לֹֽא־יָב֥וֹא אֲלֵיהֶֽם׃ פ
24 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu, Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti, “Haa, odana nane ndidzawatha, ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
לָכֵ֗ן נְאֻ֤ם הָֽאָדוֹן֙ יְהוָ֣ה צְבָא֔וֹת אֲבִ֖יר יִשְׂרָאֵ֑ל ה֚וֹי אֶנָּחֵ֣ם מִצָּרַ֔י וְאִנָּקְמָ֖ה מֵאוֹיְבָֽי׃
25 Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe; ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa, monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
וְאָשִׁ֤יבָה יָדִי֙ עָלַ֔יִךְ וְאֶצְרֹ֥ף כַּבֹּ֖ר סִיגָ֑יִךְ וְאָסִ֖ירָה כָּל־בְּדִילָֽיִךְ ׃
26 Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana, aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja. Kenaka iweyo udzatchedwa mzinda wolungama, mzinda wokhulupirika.”
וְאָשִׁ֤יבָה שֹׁפְטַ֙יִךְ֙ כְּבָרִ֣אשֹׁנָ֔ה וְיֹעֲצַ֖יִךְ כְּבַתְּחִלָּ֑ה אַחֲרֵי־כֵ֗ן יִקָּ֤רֵא לָךְ֙ עִ֣יר הַצֶּ֔דֶק קִרְיָ֖ה נֶאֱמָנָֽה׃
27 Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama, anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
צִיּ֖וֹן בְּמִשְׁפָּ֣ט תִּפָּדֶ֑ה וְשָׁבֶ֖יהָ בִּצְדָקָֽה׃
28 Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi, ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
וְשֶׁ֧בֶר פֹּשְׁעִ֛ים וְחַטָּאִ֖ים יַחְדָּ֑ו וְעֹזְבֵ֥י יְהוָ֖ה יִכְלֽוּ׃
29 “Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu imene inkakusangalatsani; mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda imene munayipatula.
כִּ֣י יֵבֹ֔שׁוּ מֵאֵילִ֖ים אֲשֶׁ֣ר חֲמַדְתֶּ֑ם וְתַ֨חְפְּר֔וּ מֵהַגַּנּ֖וֹת אֲשֶׁ֥ר בְּחַרְתֶּֽם׃
30 Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota, mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
כִּ֣י תִֽהְי֔וּ כְּאֵלָ֖ה נֹבֶ֣לֶת עָלֶ֑הָ וּֽכְגַנָּ֔ה אֲשֶׁר־מַ֖יִם אֵ֥ין לָֽהּ׃
31 Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma, ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali; motero zonse zidzayakira limodzi, popanda woti azimitse motowo.”
וְהָיָ֤ה הֶחָסֹן֙ לִנְעֹ֔רֶת וּפֹעֲל֖וֹ לְנִיצ֑וֹץ וּבָעֲר֧וּ שְׁנֵיהֶ֛ם יַחְדָּ֖ו וְאֵ֥ין מְכַבֶּֽה׃ ס

< Yesaya 1 >