< Yesaya 8 >

1 Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.
ויאמר יהוה אלי קח לך גליון גדול וכתב עליו בחרט אנוש למהר שלל חש בז׃
2 Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
ואעידה לי עדים נאמנים את אוריה הכהן ואת זכריהו בן יברכיהו׃
3 Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’
ואקרב אל הנביאה ותהר ותלד בן ויאמר יהוה אלי קרא שמו מהר שלל חש בז׃
4 Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
כי בטרם ידע הנער קרא אבי ואמי ישא את חיל דמשק ואת שלל שמרון לפני מלך אשור׃
5 Yehova anayankhulanso ndi Ine;
ויסף יהוה דבר אלי עוד לאמר׃
6 “Popeza anthu a dziko ili akana madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu, ndipo akukondwerera Rezini ndi mwana wa Remaliya,
יען כי מאס העם הזה את מי השלח ההלכים לאט ומשוש את רצין ובן רמליהו׃
7 nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo; mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo. Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse ndi mʼmagombe ake onse.
ולכן הנה אדני מעלה עליהם את מי הנהר העצומים והרבים את מלך אשור ואת כל כבודו ועלה על כל אפיקיו והלך על כל גדותיו׃
8 Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira, adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi. Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse, iwe Imanueli!”
וחלף ביהודה שטף ועבר עד צואר יגיע והיה מטות כנפיו מלא רחב ארצך עמנו אל׃
9 Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere! Tamverani, inu mayiko onse akutali. Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere! Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
רעו עמים וחתו והאזינו כל מרחקי ארץ התאזרו וחתו התאזרו וחתו׃
10 Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu, kambiranani zochita, koma zidzalephereka, pakuti Mulungu ali nafe.
עצו עצה ותפר דברו דבר ולא יקום כי עמנו אל׃
11 Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:
כי כה אמר יהוה אלי בחזקת היד ויסרני מלכת בדרך העם הזה לאמר׃
12 “Usamanene kuti ndi chiwembu, chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu usamaope zimene anthuwa amaziopa, ndipo usamachite nazo mantha.
לא תאמרון קשר לכל אשר יאמר העם הזה קשר ואת מוראו לא תיראו ולא תעריצו׃
13 Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
את יהוה צבאות אתו תקדישו והוא מוראכם והוא מערצכם׃
14 ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika; koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala mwala wopunthwitsa, mwala umene umapunthwitsa anthu, thanthwe limene limagwetsa anthu. Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
והיה למקדש ולאבן נגף ולצור מכשול לשני בתי ישראל לפח ולמוקש ליושב ירושלם׃
15 Anthu ambiri adzapunthwapo adzagwa ndi kuthyokathyoka, adzakodwa ndi kugwidwa.”
וכשלו בם רבים ונפלו ונשברו ונוקשו ונלכדו׃
16 Manga umboniwu ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
צור תעודה חתום תורה בלמדי׃
17 Ndidzayembekezera Yehova, amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo. Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
וחכיתי ליהוה המסתיר פניו מבית יעקב וקויתי לו׃
18 Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
הנה אנכי והילדים אשר נתן לי יהוה לאתות ולמופתים בישראל מעם יהוה צבאות השכן בהר ציון׃
19 Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo,
וכי יאמרו אליכם דרשו אל האבות ואל הידענים המצפצפים והמהגים הלוא עם אל אלהיו ידרש בעד החיים אל המתים׃
20 kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.
לתורה ולתעודה אם לא יאמרו כדבר הזה אשר אין לו שחר׃
21 Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo.
ועבר בה נקשה ורעב והיה כי ירעב והתקצף וקלל במלכו ובאלהיו ופנה למעלה׃
22 Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.
ואל ארץ יביט והנה צרה וחשכה מעוף צוקה ואפלה מנדח׃

< Yesaya 8 >