< Yesaya 7 >

1 Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.
ויהי בימי אחז בן יותם בן עזיהו מלך יהודה עלה רצין מלך ארם ופקח בן רמליהו מלך ישראל ירושלם למלחמה עליה ולא יכל להלחם עליה׃
2 Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
ויגד לבית דוד לאמר נחה ארם על אפרים וינע לבבו ולבב עמו כנוע עצי יער מפני רוח׃
3 Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu.
ויאמר יהוה אל ישעיהו צא נא לקראת אחז אתה ושאר ישוב בנך אל קצה תעלת הברכה העליונה אל מסלת שדה כובס׃
4 Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya.
ואמרת אליו השמר והשקט אל תירא ולבבך אל ירך משני זנבות האודים העשנים האלה בחרי אף רצין וארם ובן רמליהו׃
5 Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti,
יען כי יעץ עליך ארם רעה אפרים ובן רמליהו לאמר׃
6 ‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’
נעלה ביהודה ונקיצנה ונבקענה אלינו ונמליך מלך בתוכה את בן טבאל׃
7 Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi: “‘Zimenezo sizidzatheka, sizidzachitika konse,
כה אמר אדני יהוה לא תקום ולא תהיה׃
8 pakuti Siriya amadalira Damasiko, ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi. Zisanathe zaka 65 Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
כי ראש ארם דמשק וראש דמשק רצין ובעוד ששים וחמש שנה יחת אפרים מעם׃
9 Dziko la Efereimu limadalira Samariya ndipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi. Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu, ndithu simudzalimba konse.’”
וראש אפרים שמרון וראש שמרון בן רמליהו אם לא תאמינו כי לא תאמנו׃
10 Yehova anayankhulanso ndi Ahazi,
ויוסף יהוה דבר אל אחז לאמר׃
11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” (Sheol h7585)
שאל לך אות מעם יהוה אלהיך העמק שאלה או הגבה למעלה׃ (Sheol h7585)
12 Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”
ויאמר אחז לא אשאל ולא אנסה את יהוה׃
13 Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga?
ויאמר שמעו נא בית דוד המעט מכם הלאות אנשים כי תלאו גם את אלהי׃
14 Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.
לכן יתן אדני הוא לכם אות הנה העלמה הרה וילדת בן וקראת שמו עמנו אל׃
15 Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino.
חמאה ודבש יאכל לדעתו מאוס ברע ובחור בטוב׃
16 Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja.
כי בטרם ידע הנער מאס ברע ובחר בטוב תעזב האדמה אשר אתה קץ מפני שני מלכיה׃
17 Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”
יביא יהוה עליך ועל עמך ועל בית אביך ימים אשר לא באו למיום סור אפרים מעל יהודה את מלך אשור׃
18 Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya.
והיה ביום ההוא ישרק יהוה לזבוב אשר בקצה יארי מצרים ולדבורה אשר בארץ אשור׃
19 Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto.
ובאו ונחו כלם בנחלי הבתות ובנקיקי הסלעים ובכל הנעצוצים ובכל הנהללים׃
20 Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe.
ביום ההוא יגלח אדני בתער השכירה בעברי נהר במלך אשור את הראש ושער הרגלים וגם את הזקן תספה׃
21 Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri.
והיה ביום ההוא יחיה איש עגלת בקר ושתי צאן׃
22 Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi.
והיה מרב עשות חלב יאכל חמאה כי חמאה ודבש יאכל כל הנותר בקרב הארץ׃
23 Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga.
והיה ביום ההוא יהיה כל מקום אשר יהיה שם אלף גפן באלף כסף לשמיר ולשית יהיה׃
24 Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga.
בחצים ובקשת יבוא שמה כי שמיר ושית תהיה כל הארץ׃
25 Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.
וכל ההרים אשר במעדר יעדרון לא תבוא שמה יראת שמיר ושית והיה למשלח שור ולמרמס שה׃

< Yesaya 7 >