< Yesaya 66 >
1 Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
[Hæc dicit Dominus: Cælum sedes mea, terra autem scabellum pedum meorum. Quæ est ista domus quam ædificabitis mihi? et quis est iste locus quietis meæ?
2 Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi, motero zonsezi ndi zanga?” Akutero Yehova. “Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu: amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima, ndipo amamvera mawu anga.
Omnia hæc manus mea fecit, et facta sunt universa ista, dicit Dominus; ad quem autem respiciam, nisi ad pauperculum, et contritum spiritu, et trementem sermones meos?
3 Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna amaphanso munthu, ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa, amaphanso galu. Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya amaperekanso magazi a nkhumba. Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso amapembedzanso fano. Popeza iwo asankha njira zawozawo, ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
Qui immolat bovem, quasi qui interficiat virum; qui mactat pecus, quasi qui excerebret canem; qui offert oblationem, quasi qui sanguinem suillum offerat; qui recordatur thuris, quasi qui benedicat idolo. Hæc omnia elegerunt in viis suis, et in abominationibus suis anima eorum delectata est.
4 Inenso ndawasankhira chilango chowawa ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija. Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha, pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu. Anachita zoyipa pamaso panga ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”
Unde et ego eligam illusiones eorum, et quæ timebant adducam eis; quia vocavi, et non erat qui responderet; locutus sum, et non audierunt; feceruntque malum in oculis meis, et quæ nolui elegerunt.
5 Imvani mawu a Yehova, inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake: “Abale anu amene amakudani, ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti, ‘Yehova alemekezeke kuti ife tione chimwemwe chanu!’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
Audite verbum Domini, qui tremitis ad verbum ejus. Dixerunt fratres vestri odientes vos, et abjicientes propter nomen meum: Glorificetur Dominus, et videbimus in lætitia vestra; ipsi autem confundentur.
6 Imvani mfuwu mu mzinda, imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu! Limenelo ndi liwu la Yehova, kulanga adani ake onse.
Vox populi de civitate, vox de templo, vox Domini reddentis retributionem inimicis suis.
7 “Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa wachira kale; asanayambe kumva ululu, wabala kale mwana wamwamuna.
Antequam parturiret, peperit; antequam veniret partus ejus, peperit masculum.
8 Ndani anamvapo zinthu zoterezi? Ndani anazionapo zinthu zoterezi? Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi, kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi? Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa nthawi yomweyo anabereka ana ake.
Quis audivit umquam tale? et quis vidit huic simile? numquid parturiet terra in die una, aut parietur gens simul, quia parturivit et peperit Sion filios suos?
9 Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira, koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova. “Kodi ndingatseke mimba pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
Numquid ego qui alios parere facio, ipse non pariam? dicit Dominus. Si ego, qui generationem ceteris tribuo, sterilis ero? ait Dominus Deus tuus.
10 “Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye, inu nonse amene mumakonda Yerusalemu, kondwera nayeni kwambiri, nonse amene mumamulira.
Lætamini cum Jerusalem et exsultate in ea, omnes qui diligitis eam; gaudete cum ea gaudio, universi qui lugetis super eam:
11 Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri wa mʼmawere a chitonthozo chake.”
ut sugatis et repleamini ab ubere consolationis ejus; ut mulgeatis et deliciis affluatis ab omnimoda gloria ejus.
12 Yehova akuti, “Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi, ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa, kapena kumufungata pa miyendo yake.
Quia hæc dicit Dominus: Ecce ego declinabo super eam quasi fluvium pacis, et quasi torrentem inundantem gloriam gentium, quam sugetis: ad ubera portabimini, et super genua blandientur vobis.
13 Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo, moteronso Ine ndidzakusangalatsani; ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”
Quomodo si cui mater blandiatur, ita ego consolabor vos, et in Jerusalem consolabimini.
14 Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu. Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
Videbitis, et gaudebit cor vestrum, et ossa vestra quasi herba germinabunt: et cognoscetur manus Domini servis ejus, et indignabitur inimicis suis.
15 Taonani, Yehova akubwera ngati moto, ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu; Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake ndi malawi amoto.
Quia ecce Dominus in igne veniet, et quasi turbo quadrigæ ejus, reddere in indignatione furorem suum et increpationem suam in flamma ignis:
16 Pakuti Yehova adzalanga anthu onse ndi moto ndi lupanga, Yehova adzapha anthu ambiri.
quia in igne Dominus dijudicabit, et in gladio suo ad omnem carnem; et multiplicabuntur interfecti a Domino,
17 Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”
qui sanctificabantur et mundos se putabant in hortis post januam intrinsecus, qui comedebant carnem suillam, et abominationem et murem: simul consumentur, dicit Dominus.
18 “Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.
Ego autem opera eorum et cogitationes eorum venio ut congregem, cum omnibus gentibus et linguis: et venient, et videbunt gloriam meam.
19 “Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
Et ponam in eis signum, et mittam ex eis qui salvati fuerint, ad gentes in mare, in Africam, et Lydiam, tendentes sagittam; in Italiam et Græciam, ad insulas longe, ad eos qui non audierunt de me, et non viderunt gloriam meam. Et annuntiabunt gloriam meam gentibus;
20 Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo.
et adducent omnes fratres vestros de cunctis gentibus donum Domino, in equis, et in quadrigis, et in lecticis, et in mulis, et in carrucis, ad montem sanctum meum Jerusalem, dicit Dominus: quomodo si inferant filii Israël munus in vase mundo in domum Domini.
21 Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
Et assumam ex eis in sacerdotes et Levitas, dicit Dominus.
22 “Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova.
Quia sicut cæli novi et terra nova, quæ ego facio stare coram me, dicit Dominus, sic stabit semen vestrum et nomen vestrum.
23 “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova.
Et erit mensis ex mense, et sabbatum ex sabbato: veniet omnis caro ut adoret coram facie mea, dicit Dominus.
24 “Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”
Et egredientur, et videbunt cadavera virorum qui prævaricati sunt in me; vermis eorum non morietur, et ignis eorum non extinguetur: et erunt usque ad satietatem visionis omni carni.]