< Yesaya 65 >
1 “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu; ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze. Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine, ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
They have sought me that before asked not for me, they have found me that sought me not. I said: Behold me, behold me, to a nation that did not call upon my name.
2 Tsiku lonse ndatambasulira manja anga anthu owukira aja, amene amachita zoyipa, natsatira zokhumba zawo.
I have spread forth my hands all the day to an unbelieving people, who walk in a way that is not good after their own thoughts.
3 Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa mopanda manyazi. Iwo amapereka nsembe mʼminda ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
A people that continually provoke me to anger before my face: that immolate in gardens, and sacrifice upon bricks.
4 Amakatandala ku manda ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika. Amadya nyama ya nkhumba, ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
That dwell in sepulchres, and sleep in the temple of idols: that eat swine’s flesh, and profane broth is in their vessels.
5 Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire, chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’ Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga, ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
That say: Depart from me, come not near me, because thou art unclean: these shall be smoke in my anger, a fire burning all the day.
6 “Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo; sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu chifukwa cha machimo awo
Behold it is written before me: I will not be silent, but I will render and repay into their bosom.
7 ndi a makolo awo,” akutero Yehova. “Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo, Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata zimene anachita kale.”
Your iniquities, and the iniquities of your fathers together, saith the Lord, who have sacrificed upon the mountains, and have reproached me upon the hills; and I will measure back their first work in their bosom.
8 Yehova akuti, “Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo, popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’ Inenso chifukwa cha mtumiki wanga; sindidzawononga onse.
Thus saith the Lord: As if a grain be found in a cluster, and it be said: Destroy it not, because it is a blessing: so will I do for the sake of my servants, that I may not destroy the whole.
9 Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo, ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo. Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi, ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
And I will bring forth a seed out of Jacob, and out of Juda a possessor of my mountains: and my elect shall inherit it, and my servants shall dwell there.
10 Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa, ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
And the plains shall be turned to folds of hocks, and the valley of Achor into a place for the herds to lie down in, for my people that have sought me.
11 “Koma inu amene mumasiya Yehova ndi kuyiwala phiri langa lopatulika, amene munamukonzera Gadi chakudya ndi kuthirira Meni chakumwa,
And you, that have forsaken the Lord, that have forgotten my holy mount, that set a table for fortune, and offer libations upon it,
12 ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe, ndipo nonse mudzaphedwa; chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani, ndinayankhula koma simunamvere. Munachita zoyipa pamaso panga ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
I will number you in the sword, and you shall all fall by slaughter: because I called and you did not answer: I spoke, and you did not hear: and you did evil in my eyes, and you have chosen the things that displease me.
13 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi.
Therefore thus saith the Lord God: Behold my servants shall eat, and you shall be hungry: behold my servants shall drink, and you shall be thirsty.
14 Atumiki anga adzayimba mosangalala, koma inu mudzalira kwambiri chifukwa chovutika mu mtima ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
Behold my servants shall rejoice, and you shall be confounded: behold my servants shall praise for joyfulness of heart, and you shall cry for sorrow of heart, and shall howl for grief of spirit.
15 Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera. Ambuye Yehova adzakuphani, koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
And you shall leave your name for an execration to my elect: and the Lord God shall slay thee, and call his servants by another name.
16 Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo adzachita zimenezo kwa Mulungu woona; ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo adzalumbira mwa Mulungu woona. Pakuti mavuto akale adzayiwalika ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
In which he that is blessed upon the earth, shall be blessed in God, amen: and he that sweareth in the earth, shall swear by God, amen: because the former distresses are forgotten, and because they are hid from my eyes.
17 “Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.
For behold I create new heavens, and a new earth: and the former things shall not be in remembrance, and they shell not come upon the heart.
18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya chifukwa cha zimene ndikulenga, pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
But you shall be glad and rejoice for ever in these things, which I create: for behold I create Jerusalem a rejoicing, and the people thereof joy.
19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga. Kumeneko sikudzamvekanso kulira ndi mfuwu wodandaula.
And I will rejoice in Jerusalem, and joy in my people, and the voice of weeping shall no more be heard in her, nor the voice of crying.
20 “Ana sadzafa ali akhanda ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse. Wamngʼono mwa iwo adzafa ali ndi zaka 100. Amene adzalephere kufika zaka 100 adzatengedwa kukhala wotembereredwa.
There shall no more be an infant of days there, nor an old man that shall not fill up his days: for the child shall die a hundred years old, and the sinner being a hundred years old shall be accursed.
21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo, adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
And they shall build houses, and inhabit them; and they shall plant vineyards, and eat the fruits of them.
22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo, kapena kudzala ndi ena nʼkudya. Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito ya manja awo nthawi yayitali.
They shall not build, and another inhabit; they shall not plant, and another eat: for as the days of a tree, so shall be the days of my people, and the works of their hands shall be of long continuance.
23 Sadzagwira ntchito pachabe kapena kubereka ana kuti aone tsoka; chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova, iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
My elect shall not labour in vain, nor bring forth in trouble; for they are the seed of the blessed of the Lord, and their posterity with them.
24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe. Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
And it shall come to pass, that before they call, I will hear; as they are yet speaking, I will hear.
25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ngʼombe, koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala chinthu chopweteka kapena chowononga,” akutero Yehova.
The wolf and the lamb shall feed together; the lion and the ox shall eat straw; and dust shall be the serpent’s food: they shall not hurt nor kill in all my holy mountain, saith the Lord.