< Yesaya 64 >

1 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
If thou wouldest open the heaven, trembling will take hold upon the mountains from thee, and they shall melt,
2 Monga momwe moto umatenthera tchire ndiponso kuwiritsa madzi, tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu, ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
as wax melts before the fire; and fire shall burn up the enemies, and thy name shall be manifest among the adversaries: at thy presence the nations shall be troubled,
3 Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere, ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
whenever thou shalt work gloriously; trembling from thee shall take hold upon the mountains.
4 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo kapena kuona Mulungu wina wonga Inu, amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
From of old we have not heard, neither have our eyes seen a God beside thee, and thy works which thou wilt perform to them that wait for mercy.
5 Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amakumbukira njira zanu. Koma Inu munakwiya, ife tinapitiriza kuchimwa. Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
For [these blessings] shall happen to them that work righteousness, and they shall remember thy ways: behold, thou wast angry and we have sinned; therefore we have erred,
6 Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa, ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo; tonse tafota ngati tsamba, ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
and we are all become as unclean, and all our righteousness as a filthy rag: and we have fallen as leaves because of our iniquities; thus the wind shall carry us [away].
7 Palibe amene amapemphera kwa Inu kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu; pakuti mwatifulatira ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
And there is none that calls upon thy name, or that remembers to take hold on thee: for thou hast turned thy face away from us, and hast delivered us up because of our sins.
8 Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
And now, O Lord, thou art our Father, and we are clay, all [of us] the work of thine hands.
9 Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso musakumbukire machimo athu mpaka muyaya. Chonde, mutiganizire, ife tikupempha, pakuti tonsefe ndi anthu anu.
Be not very wroth with us, and remember not our sins for ever; but now look on [us], for we are all thy people.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu; ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
The city of thy holiness has become desolate, Sion has become as a wilderness, Jerusalem a curse.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani, yatenthedwa ndi moto ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
The house, our sanctuary, and the glory which our fathers blessed, has been burnt with fire: and all our glorious things have gone to ruin.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza? Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
And for all these things thou, O Lord, has withholden, thyself, and been silent, and hast brought us very low.

< Yesaya 64 >