< Yesaya 61 >

1 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
רוח אדני יהוה עלי יען משח יהוה אתי לבשר ענוים שלחני לחבש לנשברי לב לקרא לשבוים דרור ולאסורים פקח קוח׃
2 Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake; za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake. Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
לקרא שנת רצון ליהוה ויום נקם לאלהינו לנחם כל אבלים׃
3 Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
לשום לאבלי ציון לתת להם פאר תחת אפר שמן ששון תחת אבל מעטה תהלה תחת רוח כהה וקרא להם אילי הצדק מטע יהוה להתפאר׃
4 Adzamanganso mabwinja akale a mzinda ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso. Adzakonzanso mizinda imene inapasuka, imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.
ובנו חרבות עולם שממות ראשנים יקוממו וחדשו ערי חרב שממות דור ודור׃
5 Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu; iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.
ועמדו זרים ורעו צאנכם ובני נכר אכריכם וכרמיכם׃
6 Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova, adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu. Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.
ואתם כהני יהוה תקראו משרתי אלהינו יאמר לכם חיל גוים תאכלו ובכבודם תתימרו׃
7 Chifukwa manyazi awo anali owirikiza; ndi kuti munalandira chitonzo ndi kutukwana, adzakondwera ndi cholowa chawo, tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza, ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.
תחת בשתכם משנה וכלמה ירנו חלקם לכן בארצם משנה יירשו שמחת עולם תהיה להם׃
8 “Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo; ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa. Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika ndikupangana nawo pangano losatha.
כי אני יהוה אהב משפט שנא גזל בעולה ונתתי פעלתם באמת וברית עולם אכרות להם׃
9 Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina. Aliyense wowaona adzazindikira kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”
ונודע בגוים זרעם וצאצאיהם בתוך העמים כל ראיהם יכירום כי הם זרע ברך יהוה׃
10 Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova; moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso, ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo. Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake, ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
שוש אשיש ביהוה תגל נפשי באלהי כי הלבישני בגדי ישע מעיל צדקה יעטני כחתן יכהן פאר וככלה תעדה כליה׃
11 Monga momwe nthaka imameretsa mbewu ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala, momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando pamaso pa mitundu yonse ya anthu.
כי כארץ תוציא צמחה וכגנה זרועיה תצמיח כן אדני יהוה יצמיח צדקה ותהלה נגד כל הגוים׃

< Yesaya 61 >