< Yesaya 6 >
1 Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
웃시야 왕의 죽던 해에 내가 본즉 주께서 높이 들린 보좌에 앉으셨는데 그 옷자락은 성전에 가득하였고
2 Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira.
스랍들은 모셔 섰는데 각기 여섯 날개가 있어 그 둘로는 그 얼굴을 가리었고 그 둘로는 그 발을 가리었고 그 둘로는 날며
3 Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
서로 창화하여 가로되 거룩하다 거룩하다 거룩하다 만군의 여호와여 그 영광이 온 땅에 충만하도다
4 Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
이같이 창화하는 자의 소리로 인하여 문지방의 터가 요동하며 집에 연기가 충만한지라
5 Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
그 때에 내가 말하되 화로다 나여 망하게 되었도다 나는 입술이 부정한 사람이요 입술이 부정한 백성 중에 거하면서 만군의 여호와이신 왕을 뵈었음이로다
6 Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe.
때에 그 스랍의 하나가 화저로 단에서 취한 바 핀 숯을 손에 가지고 내게로 날아와서
7 Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
그것을 내 입에 대며 가로되 보라 이것이 네 입에 닿았으니 네 악이 제하여졌고 네 죄가 사하여졌느니라 하더라
8 Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?” Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
내가 또 주의 목소리를 들은즉 이르시되 내가 누구를 보내며 누가 우리를 위하여 갈꼬 그 때에 내가 가로되 내가 여기 있나이다 나를 보내소서
9 Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa: “‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa; kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
여호와께서 가라사대 가서 이 백성에게 이르기를 너희가 듣기는 들어도 깨닫지 못할 것이요 보기는 보아도 알지 못하리라 하여
10 Tsono anthu amenewa uwaphe mtima; uwagonthetse makutu, ndipo uwatseke mʼmaso. Mwina angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi mitima yawo, kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
이 백성의 마음으로 둔하게 하며 그 귀가 막히고 눈이 감기게 하라 염려컨대 그들이 눈으로 보고 귀로 듣고 마음으로 깨닫고 다시 돌아와서 고침을 받을까 하노라
11 Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?” Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti, “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja nʼkusowa wokhalamo, mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
내가 가로되 주여 어느 때까지니이까 대답하시되 성읍들은 황폐하여 거민이 없으며 가옥들에는 사람이 없고 이 토지가 전폐하게 되며
12 mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali, dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
사람들이 여호와께 멀리 옮기워서 이 땅 가운데 폐한 곳이 많을 때까지니라
13 Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko, nachonso chidzawonongedwa. Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu imasiyira chitsa pamene ayidula, chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”
그 중에 십분의 일이 오히려 남아 있을지라도 이것도 삼키운바 될 것이나 밤나무, 상수리나무가 베임을 당하여도 그 그루터기는 남아 있는 것 같이 거룩한 씨가 이 땅의 그루터기니라