< Yesaya 59 >

1 Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa, kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
耶和华的膀臂并非缩短,不能拯救, 耳朵并非发沉,不能听见,
2 Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.
但你们的罪孽使你们与 神隔绝; 你们的罪恶使他掩面不听你们。
3 Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi. Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu. Pakamwa panu payankhula zabodza, ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.
因你们的手被血沾染, 你们的指头被罪孽沾污, 你们的嘴唇说谎言, 你们的舌头出恶语。
4 Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama, palibe amene akupita ku mlandu moona mtima. Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza; amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
无一人按公义告状, 无一人凭诚实辨白; 都倚靠虚妄,说谎言。 所怀的是毒害; 所生的是罪孽。
5 Iwo amayikira mazira a mamba ndipo amaluka ukonde wakangawude. Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa, ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.
他们抱毒蛇蛋, 结蜘蛛网; 人吃这蛋必死。 这蛋被踏,必出蝮蛇。
6 Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala; ndipo chimene apangacho sangachifunde. Ntchito zawo ndi zoyipa, ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
所结的网不能成为衣服; 所做的也不能遮盖自己。 他们的行为都是罪孽; 手所做的都是强暴。
7 Amathamangira kukachita zoyipa; sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo awo ndi maganizo oyipa; kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
他们的脚奔跑行恶; 他们急速流无辜人的血; 意念都是罪孽, 所经过的路都荒凉毁灭。
8 Iwo sadziwa kuchita za mtendere; zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo. Njira zawo zonse nʼzokhotakhota; aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.
平安的路,他们不知道; 所行的事没有公平。 他们为自己修弯曲的路; 凡行此路的都不知道平安。
9 Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira; ndipo chipulumutso sichitifikira. Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha; tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
因此,公平离我们远, 公义追不上我们。 我们指望光亮,却是黑暗, 指望光明,却行幽暗。
10 Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona, kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso. Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku; timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
我们摸索墙壁,好像瞎子; 我们摸索,如同无目之人。 我们晌午绊脚,如在黄昏一样; 我们在肥壮人中,像死人一般。
11 Tonse timabangula ngati zimbalangondo: Timalira modandaula ngati nkhunda. Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza. Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”
我们咆哮如熊, 哀鸣如鸽; 指望公平,却是没有; 指望救恩,却远离我们。
12 Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu, ndipo machimo athu akutsutsana nafe. Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse ndipo tikuvomereza machimo athu:
我们的过犯在你面前增多, 罪恶作见证告我们; 过犯与我们同在。 至于我们的罪孽,我们都知道:
13 Tawukira ndi kumukana Yehova. Tafulatira Mulungu wathu, pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova, ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.
就是悖逆、不认识耶和华, 转去不跟从我们的 神, 说欺压和叛逆的话, 心怀谎言,随即说出。
14 Motero kuweruza kolungama kwalekeka ndipo choonadi chili kutali ndi ife; kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu, ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.
并且公平转而退后, 公义站在远处; 诚实在街上仆倒, 正直也不得进入。
15 Choonadi sichikupezeka kumeneko, ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto. Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa kuti panalibe chiweruzo cholungama.
诚实少见; 离恶的人反成掠物。 那时,耶和华看见没有公平, 甚不喜悦。
16 Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe, Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera; Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza, ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
他见无人拯救, 无人代求,甚为诧异, 就用自己的膀臂施行拯救, 以公义扶持自己。
17 Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso; anavala kulipsira ngati chovala ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
他以公义为铠甲, 以拯救为头盔, 以报仇为衣服, 以热心为外袍。
18 Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake molingana ndi zimene anachita, adzaonetsa ukali kwa adani ake ndi kubwezera chilango odana naye. Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
他必按人的行为施报, 恼怒他的敌人, 报复他的仇敌 向众海岛施行报应。
19 Choncho akadzabwera ngati madzi oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho. Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
如此,人从日落之处必敬畏耶和华的名, 从日出之地也必敬畏他的荣耀; 因为仇敌好像急流的河水冲来, 是耶和华之气所驱逐的。
20 “Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,” akutero Yehova.
必有一位救赎主来到锡安— 雅各族中转离过犯的人那里。 这是耶和华说的。
21 Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.
耶和华说:“至于我与他们所立的约乃是这样:我加给你的灵,传给你的话,必不离你的口,也不离你后裔与你后裔之后裔的口,从今直到永远;这是耶和华说的。”

< Yesaya 59 >