< Yesaya 57 >

1 Anthu olungama amafa, ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake; anthu odzipereka amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amatengedwa kuti tsoka lisawagwere.
義人死去,沒有人放在心上;虔誠的人被收去,沒有人予以注意:義人被接去,是為了脫離災難,
2 Iwo amene amakhala moyo wolungama amafa mwamtendere; amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.
而進入安息;躬行正直的人,將安眠於自己的處所。
3 “Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa, inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!
巫女的兒子,姦婦淫女的後裔,你們近前來!
4 Kodi inu mukuseka yani? Kodi mukumunena ndani ndi kupotoza pakamwa panu? Kodi inu si ana owukira, zidzukulu za anthu abodza?
你們戲謔誰呢﹖你們向誰張口吐舌呢﹖不是你們這些反叛的兒子,不忠的後裔,
5 Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu, ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri. Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
在橡樹林中,在一切綠樹下慾火中燒;在山谷中,在磐石的夾縫裏祭殺嬰兒嗎﹖
6 Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo, ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandichititse kuti ndikukomereni mtima?
山谷中的光石竟是你的家產,它們竟成了你的產業;並且你還給它們奠了酒,獻了供物,對這些事我豈能容忍﹖
7 Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali. Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.
在巍峨高聳的山上,你安置了你的床榻,並且上那裏去奉獻犧牲。
8 Mʼnyumba mwanu mwayika mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu. Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu. Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu, ndiye mwazilipira kuti mugone nazo. Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
你在門和門框後安置了你的記號,瞞著我裸體上了床,舖開了你的床榻,你喜歡與誰同寢,便與他茍合,且看了他的手。
9 Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta ndi zonunkhira zochuluka. Munachita kutumiza akazembe anu kutali; inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko! (Sheol h7585)
你擦滿了香膏,加多了香料,往摩肋客那裏去,又遣發使者到遠方去,你甚至深入了陰間。 (Sheol h7585)
10 Inu mumatopa ndi maulendo anu, koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’ Munapezako kumeneko zokhumba zanu nʼchifukwa chake simunalefuke.
你因路途遙遠,已感疲倦,但總不說:「絕望了!」因為你找著了你新生的力量,所以你不覺困乏。
11 “Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa, kotero kuti mwakhala mukundinamiza, ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe, kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine? Kodi mwaleka kundiopa chifukwa choti ndakhala chete nthawi yayitali?
你害怕誰,畏懼誰,竟使你失去忠信,而不懷念我,不關心我﹖難道因為我久不作聲,你就不怕我了嗎﹖
12 Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama, ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.
我要披露你的義舉,以及與你毫無裨益的行為。
13 Pamene mufuwula kupempha thandizo, mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni! Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo, mpweya chabe udzawulutsa mafanowo. Koma munthu amene amadalira ine adzalandira dziko lokhalamo. Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”
當你呼求時,讓你那一夥救你罷!但是一陣風要把它們全部捲走,一口氣要把他們吹去。唯有那依賴我的,將承受地業,繼承我的聖山。
14 Ndipo panamveka mawu akuti, “Undani, undani, konzani msewu! Chotsani zotchinga pa njira yoyendamo anthu anga.”
有個聲音說:「修路,修路!把路修平,把我民族道路上的障礙除去!」
15 Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
因為至高者,卓越者,居於永遠者,名為聖者的這樣說:「我雖居於高處及聖所,但我也與懺悔和心靈謙卑的人在一起,為振奮謙卑者的心情,甦醒懺悔者的心靈。
16 Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya kapena kuwapsera mtima nthawi zonse, popeza kuti ndinalenga anthu anga ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.
我不願永遠爭辯,也不願永久發怒,因為生氣是由我而出,靈魂是由我而造。
17 Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera; ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya, koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.
因了她的罪惡我一時發怒,打擊了她,在怒氣中掩住我的面;可是她仍背叛,走她隨心所欲的道路。
18 Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa; kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,
我看見了她的行為,我要醫治她,我要引她回來,將安慰賜給她和她的憂傷者。
19 anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo. Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,” “Ndipo ndidzawachiritsa.” Akutero Yehova.
在他們的口唇上安放讚頌之辭:「平安,平安歸於遠近的人 !」上主說。【我要醫好她。】
20 Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka, yosatha kukhala bata, mafunde ake amaponya matope ndi ndere.
但惡人將如翻騰的大海,不能平息,它的海浪捲起黃土與淤泥。
21 “Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.
我的天主說:惡人決無平安!

< Yesaya 57 >