< Yesaya 56 >
1 Yehova akuti, “Chitani chilungamo ndi zinthu zabwino, chifukwa chipulumutso changa chili pafupi ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
Hæc dicit Dominus: Custodite judicium, et facite justitiam, quia juxta est salus mea ut veniat, et justitia mea ut reveletur.
2 Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbika kuzichita, amene amasunga Sabata osaliyipitsa, ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”
Beatus vir qui facit hoc, et filius hominis qui apprehendet istud, custodiens sabbatum ne polluat illud, custodiens manus suas ne faciat omne malum.
3 Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti, “Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.” Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, “Ine ndine mtengo wowuma basi.”
Et non dicat filius advenæ qui adhæret Domino, dicens: Separatione dividet me Dominus a populo suo; et non dicat eunuchus: Ecce ego lignum aridum.
4 Popeza Yehova akuti, “Wofulidwa amene amasunga masabata anga, nachita zokomera Ine ndi kusunga pangano langa,
Quia hæc dicit Dominus eunuchis: Qui custodierint sabbata mea, et elegerint quæ ego volui, et tenuerint fœdus meum,
5 ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake, kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzawapatsa dzina labwino, losatha ndi losayiwalika.”
dabo eis in domo mea et in muris meis locum, et nomen melius a filiis et filiabus: nomen sempiternum dabo eis, quod non peribit.
6 Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova, motero kuti amamutumikira Iye, amakonda dzina la Yehova, amamugwirira ntchito, komanso kusunga Sabata osaliyipitsa ndi kusunga bwino pangano langa,
Et filios advenæ, qui adhærent Domino, ut colant eum, et diligant nomen ejus, ut sint ei in servos; omnem custodientem sabbatum ne polluat illud, et tenentem fœdus meum;
7 amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika, ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero. Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe. Paja nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
adducam eos in montem sanctum meum, et lætificabo eos in domo orationis meæ; holocausta eorum et victimæ eorum placebunt mihi super altari meo, quia domus mea domus orationis vocabitur cunctis populis.
8 Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti, “Ndidzasonkhanitsano anthu ena kuwonjezera amene anasonkhana kale.”
Ait Dominus Deus, qui congregat dispersos Israël: Adhuc congregabo ad eum congregatos ejus.
9 Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo, inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
Omnes bestiæ agri, venite ad devorandum, universæ bestiæ saltus.
10 Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu, onse ndi opanda nzeru; onse ndi agalu opanda mawu, samatha kuwuwa: amagona pansi nʼkumalota amakonda kugona tulo.
Speculatores ejus cæci omnes; nescierunt universi: canes muti non valentes latrare, videntes vana, dormientes, et amantes somnia.
11 Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu; sakhuta konse. Abusa nawonso samvetsa zinthu; onse amachita monga akufunira, aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
Et canes imprudentissimi nescierunt saturitatem; ipsi pastores ignoraverunt intelligentiam: omnes in viam suam declinaverunt; unusquisque ad avaritiam suam, a summo usque ad novissimum.
12 Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo! Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta! Mawa lidzakhala ngati leroli, kapena kuposa lero lino.”
Venite, sumamus vinum, et impleamur ebrietate; et erit sicut hodie, sic et cras, et multo amplius.